Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Sindinabwerere M’mbuyo Ngakhale Kuti Ndili ndi Matenda Olepheretsa Kuwerenga

Sindinabwerere M’mbuyo Ngakhale Kuti Ndili ndi Matenda Olepheretsa Kuwerenga

Sindinabwerere M’mbuyo Ngakhale Kuti Ndili ndi Matenda Olepheretsa Kuwerenga

Yosimbidwa ndi Michael Henborg

Ndimavutika kuwerenga chifukwa cha matenda amene ndili nawo. Bambo anga, mayi anga komanso ang’ono anga awiri alinso ndi matenda amenewa. Ndimavutika kuwerenga Chidanishi chomwe ndi chilankhulo chathu ndipo kusukulu sizinkayenda ayi. Ngakhale zili choncho, ndathandizidwa ndi kulimbikitsidwa kwambiri makamaka ndi achibale anga.

INE ndinabadwira m’banja la Mboni. Nawonso agogo anga ndi makolo awo anali Mboni za Yehova. Nthawi zonse banja lathu limawerenga Baibulo ndi mabuku ena ofotokoza Baibulo. Ine ndi mng’ono wanga Fleming tinkakonda kuyenda ndi bambo anga polalikira, ndipo izi zinatichititsa kuona kuti kuwerenga ndi kulemba bwino n’kofunika kwambiri.

Ndili wamng’ono ndinkawerenga magazini iliyonse ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndipo zinkanditengera maola pafupifupi 15 kuti ndimalize magazini imodzi. Kenako ndinali ndi cholinga choti ndiwerenge Baibulo lonse. Komanso ndinayamba Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imene Mboni za Yehova padziko lonse zimachita. Sukulu imeneyi imaphunzitsa anthu kuwerenga bwino, kulankhula bwino komanso kukamba nkhani pagulu. Zinthu zonsezi zandithandiza kwambiri polimbana ndi vuto langali. Komabe sindinkadziwa kuti ndidzatha kuphunzira zinthu zambiri mtsogolo. Ndiloleni kuti ndifotokoze.

Kuphunzira Chingelezi

Mu 1988, ndili ndi zaka 24, ndinayamba upainiya. Iyi ndi ntchito yolalikira uthenga wabwino nthawi zonse. Koma ndinafunika kulalikira choonadi cha m’Baibulo kwa anthu ambirimbiri amene anasamukira ku Denmark. Kuti zimenezi zitheke ndinafunika kuphunzira Chingelezi. Iyitu inali ntchito yovuta kwambiri. Ngakhale zinali choncho, ndinachita khama kwambiri n’kumaphunziranso pandekha moti ndinayamba kuchidziwa Chingelezi. Patapita nthawi ndinayamba kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa anthu olankhula Chingelezi m’tauni yakwathu yotchedwa Copenhagen. Ndinkalakwitsa ndithu zinthu zina komabe sindinabwerere m’mbuyo.

Chifukwa chodziwa Chingelezi, ndinagwira nawo ntchito ya zomangamanga imene Mboni za Yehova zimagwira m’mayiko osiyanasiyana. Poyamba ananditumiza ku Greece, kenako ndinakathandizanso kumanga ofesi ya nthambi ku Madrid, m’dziko la Spain.

Pofuna kuchita zambiri pantchito yolalikira, ndinafunsira mwayi wokalowa nawo Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Sukulu ya Mboni za Yehova imeneyi imatenga miyezi iwiri ndipo imaphunzitsa Akhristu osakwatira kuti athe kuchita zambiri pantchito yolalikira kumadera amene kulibe alaliki authenga wabwino ambiri. (Maliko 13:10) Anandiitana kuti ndikachite maphunzirowa m’Chingelezi ku Sweden.

Tinayamba maphunzirowa pa September 1, 1994. Pokonzekera maphunzirowa ndinayambiranso kuphunzira Chingelezi ndipo ndinkaphunzira kwa maola anayi patsiku kwa miyezi 8 komanso ndinayamba kupita ku mpingo wa Chingelezi. Titayamba sukuluyo sindinalole kuti vuto langalo lindilepheretse kupita patsogolo. Mwachitsanzo, aphunzitsi akafunsa funso ndinkakweza mkono kuti ndiyankhe ngakhale kuti nthawi zina sindinkadziwa mawu amene ndingagwiritse ntchito. Titamaliza maphunzirowa ananditumiza ku Copenhagen kukachita upainiya. Chingelezi chinandivuta kuphunzira koma kenako ndinakumananso ndi chilankhulo china chovuta kuposa Chingelezi.

Kuphunzira Chitamilu

Mu December, chaka cha 1995, ndinatumizidwa ku mpingo wa chinenero cha Chitamilu mu tawuni ya Herning ku Denmark. Poyamba ndinkaganiza kuti chilankhulo cha Chitamilu ndi chimodzi mwa zilankhulo zovuta kwambiri. Chili ndi zilembo 250, ndipo pazilembozi, 31 zimalembedwa pazokha pomwe zinazo amaphatikiza zilembo zingapo kuti apange chilembo chimodzi.

Poyamba ndinkakamba nkhani mu Chidanishi ena n’kumamasulira mu Chitamilu. Kenako ndinadzakamba nkhani yanga yoyamba mu Chitamilu koma sindikukhulupirira kuti ndinkalankhula zomveka. Komabe anthu ankamvetsera mwachidwi ngakhale kuti ena ankaseka. Pofuna kuphunzira msanga chilankhulochi, ndinasamukira m’dziko la Sri Lanka lomwe muli anthu ambiri olankhula Chitamilu.

Ndinafika ku Sri Lanka mu October m’chaka cha 1996. Panthawiyi m’dzikoli munali nkhondo yapachiweniweni. Kwakanthawi ndinakhala mu tawuni yotchedwa Vavuniya yomwe inali pakati pa madera awiri amene amamenyanawa. Amboni a kumeneku anali osauka, koma anali achikondi kwambiri komanso odziwa kulandira alendo ndipo anachita khama kundiphunzitsa Chitamilu. Anthu ena akumeneku ankasangalala kwambiri kuona kuti ndimalankhula nawo m’chinenero chawo ngakhale kuti ndine wochokera ku dziko lina. Anali anthu oyamikira komanso odzichepetsa ndipo izi zinachititsa kuti ndisamavutike pophunzira nawo Baibulo.

Mu January 1997, ndinabwerera ku Denmark ndipo chaka chotsatira ndinakwatira Camilla yemwe ankachitanso upainiya. Mu December 1999, anandiitananso ku Sri Lanka ndipo paulendowu ndinapita ndi mkazi wanga. Pasanapite nthawi yaitali, tinkachititsa maphunziro a Baibulo ndi anthu ambiri ndipo ena anali mabanja. Ndipo a abale akumeneko ankatitenganso popita ku maphunziro awo a Baibulo. Tinkalimbikira kwambiri utumiki ndiponso kuphunzira chinenero.

M’mwezi wa March m’chaka cha 2000, tinabwerera ku Denmark. Zinali zovuta kwambiri kusiyana ndi abale athu komanso anthu amene timaphunzira nawo Baibulo, chifukwa tinkawakonda kwambiri. Komabe sitikanachitira mwina chifukwa panali ntchito yaikulu yoti tichite. Ndipo tinafunikira kuphunziranso chinenero china.

Tinayamba Kuphunzira Chilativiya

M’mwezi wa May 2002, ine ndi mkazi wanga Camilla, tinapemphedwa kuti tikakhale amishonale ku Latvia. Dzikoli lili ku Ulaya, kum’mawa kwa dziko la Denmark. Apa n’kuti titatha zaka zinayi tili m’banja. Camilla anaphunzira msanga chinenerochi, moti ankatha kuchilankhula patangopita mwezi umodzi ndi theka basi. Koma ineyo zinkandivuta. Ndipo ngakhale panopo ndimaona kuti sindinapite patsogolo kwambiri, ngakhale kuti anthu amayesetsa kundithandiza. Komabe sindibwerera m’mbuyo. *

Mkazi wanga Camilla amandithandiza kwambiri, ndipo tonse tikusangalala kwambiri mu utumiki wathu wa umishonale. Pofika pano, taphunzira Baibulo ndi anthu ambiri ofuna kumva choonadi. Ndikaiwala mawu enaake kapena kulankhula zinthu zina molakwika, Mboni za kumeneku komanso anthu amene timawaphunzitsa Baibulo amayesetsa kumvetsa chimene ndikufuna kunena n’kundithandiza. Zimenezi zimandilimbitsa mtima polalikira anthu osiyanasiyana komanso ndikamakamba nkhani za m’Baibulo pa misonkhano yachikhristu.

Kuphunzira zinthu kumandivuta kwambiri koma ndalolera kuphunzira zinenero zina chifukwa cha chikondi. Sikuti ndimangophunzira zinenero zina chifukwa choti zimandisangalatsa, koma ndimakonda kwambiri anthu. Kuthandiza munthu kuti adziwe komanso kukonda Mulungu woona, Yehova, ndi mwayi waukulu kwambiri. Ndipo kuti uthandize bwino kwambiri anthu m’njira imeneyi, uyenera kulankhula nawo m’chinenero cha makolo awo chomwe tingati ndi chinenero chapamtima pawo. Amishonale ambiri angavomereze zimenezi.

Pazaka zimene zapitazi, ineyo ndi mkazi wanga tathandiza anthu ambiri kudziwa choonadi cha m’Baibulo molondola. Zimenezi sizinatheke chifukwa cha nzeru kapena khama lathu ayi. Koma zinatheka chifukwa cha Yehova. Mulungu ndi amene amakulitsa mbewu za choonadi cha m’Baibulo, ifeyo timangobzala ndi kuthirira basi.—1 Akorinto 3:6.

Ukaipa Dziwa Nyimbo

Vuto langali landithandizanso pa zinthu zina. Mwachitsanzo, ndikamakamba nkhani za m’Baibulo ku mpingo ndimavutika kuwerenga zimene ndalemba. Komabe zimenezi zimandithandiza kuti nthawi zambiri ndiziyang’ana omvetsera. Komanso ndimakonda kugwiritsira ntchito zitsanzo chifukwa n’zosavuta kukumbukira. Motero tingati vuto langali landithandizanso kukhala ndi luso lophunzitsa.

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko, kuti achititse manyazi zinthu zamphamvu.” (1 Akorinto 1:27) N’zoona kuti vuto langali landipangitsa kukhala ‘chinthu chofooka’ pa zinthu zina. Komabe ndaona kuti Yehova angathe kundithandiza kwambiri pa zimene ndikulephera, ndipo anthu ena ambiri angavomereze zimenezi. Pamangofunika kudziwa zochita basi komabe tisaganize kuti kuchita zinthuzo ndi kophweka ayi. Tikatero tipemphe Mulungu kuti atipatse mzimu woyera kenako n’kuyamba kuchita zinthuzo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Posachedwapa banja la a Henborg linatumizidwa ku Ghana, litatumikira ku Latvia kwa zaka 6. 

[Bokosi patsamba 22]

MATENDA OLEPHERETSA KUWERENGA

Kodi matendawa ndi otani? Matendawa amalepheretsa munthu kuphunzira kuwerenga ndipo alibe mankhwala. Anthu amene ali ndi vuto limeneli satha kugwirizanitsa zilembo ndi katchulidwe ka zilembozo. Koma zizindikiro za matendawa zimakhala zosiyanasiyana kwa anthu osiyanasiyana.

Kodi chimayambitsa matendawa n’chiyani? Mpaka pano anthu sakudziwa chimene chimayambitsa matendawa, koma ena amatengera kwa makolo awo. Ofufuza ena apeza kuti vutoli limabwera chifukwa cha mavuto ena mu ubongo, koma sikuti kumakhala kupanda nzeru kapena kusafuna kuphunzira. Ndipotu anthu amene ali ndi matenda amenewa amakhala akatswiri pa zinthu zina zosadalira kwambiri pa kuwerenga ndi kulemba.

Kodi anthu odwala matendawa angathandizidwe bwanji? Zimakhala bwino munthu akadziwika msanga kuti ali ndi vutoli. Kuti munthu wotere aphunzire kulemba kapena kuwerenga afunika kuphunzitsidwa pogwiritsa ntchito zinthu zoti azitha kuzimva, kuziona komanso kuzikhudza. Ambiri amafunika kuphunzitsidwa paokha kuti athe kuphunzira bwino. Komanso amafunika kuwalimbikitsa chifukwa amakhumudwa ndi zinthu zimene zimawavuta kuphunzira. Anthuwa angathe kudziwa kuwerenga ndi kulemba bwinobwino ngati atakhala ndi mphunzitsi wabwino komanso atachita khama. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 31 Mfundozi zachokera ku bungwe la pa dziko lonse loona za matenda olepheretsa kuphunzira (lotchedwa International Dyslexia Association). Onaninso nkhani yakuti “Kuthandiza Ana Amene Ali ndi Vuto Lophunzira” mu Galamukani! ya January 2009.

[Chithunzi patsamba 23]

Ndili ndi mnzanga wa Mboni ku Sri Lanka

[Chithunzi patsamba 23]

Ndili ndi Camilla ku Latvia