Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndipeze Anzanga Ena Abwino?

Kodi Ndipeze Anzanga Ena Abwino?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndipeze Anzanga Ena Abwino?

“Ndikakwiya ndimafuna nditauzako wina zimene zandichitikira. Ndikakhumudwa ndimafuna munthu wina andilimbikitse. Ndikasangalala ndimafunanso kuti ena asangalale nane. Ineyo ndimaona kuti sindingakhale wopanda anzanga.”—Anatero Brittany.

ANTHU ambiri amati ana ang’onoang’ono amafuna anzawo oti azisewera nawo koma achinyamata amafuna anzawo apamtima oti azicheza nawo. Kodi pali kusiyana kulikonse?

Pali anzanu ena omwe ndi ongosewera nawo basi.

Mnzanu wapamtima ndi munthu amene amakonda zinthu zimene inunso mumakonda.

Baibulo limati: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo m’bale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” (Miyambo 17:17) Lembali limafotokoza za ubwenzi weniweni osati kungosewera ndi anzanu basi.

Dziwani izi: Mukamakula mumafunikira anzanu omwe

(1) Ali ndi makhalidwe abwino

(2) Amatsatira mfundo za m’Baibulo.

(3) Amakulimbikitsani kuchita zabwino.

Funso: Kodi mungadziwe bwanji kuti anzanu ali ndi makhalidwe amenewa? Tiyeni tione khalidwe lililonse palokha.

Choyamba: Makhalidwe Abwino

Zimene muyenera kudziwa. Si anzanu onse amene akuyenereradi kukhala anzanu apamtima. Baibulo limati: “Woyanjana ndi ambiri angodziwononga.” (Miyambo 18:24) Ena angaone ngati mawu amenewa ndi okokomeza, koma taganizirani mfundo iyi: Kodi munakhalapo ndi “mnzanu” yemwe ankakukondani chifukwa chofuna chinachake kwa inu? Kodi munakhalapo ndi mnzanu yemwe ankakunenani miseche kapena kufalitsa zabodza zokhudza inuyo? Ngati ndi choncho, zimenezi zingakuchititseni kuti musiye kukhulupirira anzanu. * Nthawi zonse muzikumbukira kuti ndi bwino kukhala ndi anzanu ochepa koma akhalidwe labwino kusiyana n’kukhala ndi anzanu ambiri koma akhalidwe loipa.

Zimene mungachite. Muzisankha anzanu amene ali ndi makhalidwe abwino oti mukhoza kuwatsatira.

“Anthu ambiri amasirira khalidwe labwino la mnzanga, Fiona. Nanenso ndimafuna nditakhala ndi mbiri yabwino ngati iyeyo. Ndimafuna n’takhala ndi khalidwe langati lake. Ndimaona kuti khalidwe limeneli ndi labwino.”—Anatero Yvette, wazaka 17.

Yesani kuchita izi.

1. Werengani Agalatiya 5:22, 23.

2. Dzifunseni kuti, ‘Kodi anzanga ali ndi makhalidwe amene amasonyeza “zipatso za mzimu”’?

3. Lembani pansipa maina a anzanu onse apamtima. Ndipo pafupi ndi dzina lililonse, lembani khalidwe limene mnzanuyo ali nalo.

Dzina Khalidwe

․․․․․ ․․․․․

․․․․․ ․․․․․

․․․․․ ․․․․․

Malangizo: Ngati mwaona kuti anzanuwo ali ndi makhalidwe oipa, mwina zingakhale bwino kupeza anzanu amakhalidwe abwino.

Chachiwiri: Amatsatira mfundo za m’Baibulo

Zimene muyenera kudziwa. Mukamapupuluma kupeza anzanu, mudzapeza anzanu osayenera. Baibulo limati: “Mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Mawu akuti “opusa” sakutanthauza anthu opanda nzeru. Koma amanena za anthu amene samvera malangizo ndipo amachita zinthu zosayenera. Awa ndi anthu amene safunika kukhala anzanu.

Zimene mungachite. M’malo mongocheza ndi aliyense, muzisankha. (Salmo 26:4) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti mukhale munthu watsankho. Apa tikutanthauza kuti muyenera kukhala wosamala kuti muzitha “kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.”—Malaki 3:18.

Mulungu alibe tsankho komabe amasankha anthu oti ‘agonere m’chihema mwake.’ (Salmo 15:1-5) Inunso muyenera kuchita zimenezi. Muzitsatira mfundo za m’Baibulo ndipo anthu ena amene akuyesetsanso kuchita zimenezi angafune kuti mukhale mnzawo. Ndipo mudzapeza anzanu apamtima abwino kwambiri.

“Ndimathokoza kwambiri makolo anga chifukwa anandithandiza kupeza anzanga amsinkhu wanga amene amatsatira mfundo za m’Baibulo.”—Anatero Christopher.

Yesani kuchita izi.

Yankhani mafunso otsatirawa:

Kodi ndikakhala ndi anzanga ndimachita mantha kuti mwina andikakamiza kuchita zinthu zoipa?

□ Inde □ Ayi

▪ Kodi ndimalephera kupita ndi anzanga kunyumba chifukwa choopa kuti makolo anga andiletsa kucheza nawo?

□ Inde □ Ayi

Malangizo: Ngati mwayankha kuti inde pa mafunso amene ali pamwambawa, pezani anzanu ena amakhalidwe abwino. Mungachite bwino kupeza anzanu okulirapo kuposa inuyo omwe amasonyeza makhalidwe abwino kwambiri achikhristu.

Chachitatu: Amakulimbikitsani kuchita zabwino

Zimene muyenera kudziwa. Baibulo limati: “Mayanjano oipa amawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33) Wachinyamata wina, dzina lake Lauren, anavomereza kuti zimenezi n’zoona ndipo anati: “Anzanga akusukulu ankandikonda ndikavomera kuchita zimene iwo akufuna kuti ndichite. Ndinalibe ocheza naye, choncho ndinaganiza kuti ndizingochita zimene iwo akufuna.” Monga mmene Lauren anaonera, ukavomera kuchita zimene ena akufuna kuti uchite, umakhala ngati kachidole kawo ndipo amangokuseweretsa mmene akufunira. Kodi mungakonde kuti azikuchitani zimenezo?

Zimene mungachite. Siyani kucheza ndi anthu amene amakukakamizani kuti muzichita zimene iwo akufuna. Mukatero, simudzakhumudwa ndipo mudzakhala ndi mwayi wopeza anzanu abwino amene angakulimbikitseni kuchita zinthu zabwino.—Aroma 12:2.

“Clint ndi mnzanga wapamtima ndipo ndi munthu womvetsa zinthu ndiponso wachifundo. Amandilimbikitsa kwambiri chifukwa cha khalidwe lakeli.”—Anatero Jason.

Yesani kuchita izi.

Dzifunseni mafunso otsatirawa:

Kodi ndimasintha kavalidwe, kalankhulidwe kapena khalidwe langa kuti ndisangalatse anzanga?

□ Inde □ Ayi

Kodi ndimapezeka ku malo okayikitsa, amene ndikanakhala kuti sindicheza ndi anzanga amenewa sindikanapitako?

□ Inde □ Ayi

Malangizo: Ngati mwayankha kuti inde pamafunso ali pamwambawa, funsani makolo anu kapena munthu aliyense wachikulire kuti akuthandizeni. Koma ngati ndinu Mboni ya Yehova mungapemphe mkulu wachikhristu kuti akuthandizeni kupeza anzanu abwino amene angakulimbikitseni.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Tikudziwa kuti aliyense amalakwitsa. (Aroma 3:23) Choncho ngati mnzanu wakulakwirani koma wakupepesani kuchokera pansi pamtima, muzikumbukira kuti “chikondi chimakwirira machimo ochuluka.”—1 Petulo 4:8.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi mungafune kuti anzanu akhale ndi makhalidwe ati, ndipo n’chifukwa chiyani?

▪ Kodi ndi makhalidwe ati amene mukufuna kuti mukhale nawo kuti anzanu azikukondani?

[Bokosi/Zithunzi patsamba 19]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

“Makolo anga atandiletsa kucheza ndi anzanga enaake, ndinadandaula chifukwa ndinkawakonda kwambiri. Malangizo a makolowa anali abwino ndipo nditayamba kuwaganizira, ndinazindikira kuti ndikhoza kupeza mosavuta anzanga abwino.”— Anatero Cole.

“Ndaona kuti kulalikira limodzi ndi Akhristu anzanga ndi njira yabwino ndiponso yondithandiza kudziwana ndi anthu a mumpingo mwathu. Ndimacheza ndi anthu osiyanasiyana, aang’ono ndi aakulu omwe. Ndipo panopo ndimacheza ndi anthu amene amakonda Yehova.”—Anatero Yvette.

“Ndinkapemphera kuti ndithe kupeza anzanga koma ineyo pandekha sindinkachita khama kuti ndipeze anzanga abwino. Choncho ndinayamba kucheza ndi anthu kumisonkhano yachikhristu. Pasanapite nthawi, ndinapeza anzanga atsopano ambirimbiri. Panopo sindisowanso ocheza naye.”—Anatero Sam.

[Bokosi patsamba 20]

YESANI KUCHITA IZI

Kambiranani ndi makolo anu nkhani zokhudza anzanu. Afunseni kuti ali achinyamata ankacheza ndi anzawo otani. Kodi panopo amadandaula chifukwa chocheza ndi anthu amenewo? Ngati amadandaula, n’chifukwa chiyani? Afunseni kuti akuuzeni zimene mungachite kuti musakumane ndi mavuto omwe iwo anakumana nawo.

Dziwitsani makolo anu anzanu omwe mumacheza nawo. Ngati simukufuna kuwadziwitsa, dzifunseni kuti, ‘N’chifukwa chiyani?’ Kodi anzanuwo ali ndi khalidwe linalake limene mukudziwa kuti makolo anu sangasangalale nalo? Ngati ndi choncho, muyenera kusankha bwino anzanu ocheza nawo.

[Bokosi patsamba 20]

NJIRA ZITATU ZOKUTHANDIZANI KUTI ANZANU AZIKUKONDANI

Muziwamvetsera. Muzichita chidwi ndi zimene zikuwachitikira anzanu ndiponso zimene zikuwadetsa nkhawa.—Afilipi 2:4.

Muziwakhululukira. Musayembekezere kuti anzanu azichita zinthu mosalakwitsa. “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.”—Yakobe 3:2.

Muziwapatsa mpata. Palibe chifukwa choti muziwakakamira anzanu. Anzanu apamtima amakuthandizanibe panthawi imene mukufunikira thandizo ngakhale mutapanda kuwakakamira.—Mlaliki 4:9, 10.

[Chithunzi pamasamba 18, 19]

Ukavomera kuchita zimene ena akufuna kuti uchite, umakhala ngati kachidole kawo ndipo amangokuseweretsa mmene akufunira