Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kodi Mipukutu Yakale Inalembedwa Liti? (February 2008) Nkhani imeneyi sindinasangalale nayo. Ndikudziwa kuti C.E. amaimira nyengo yathu ino ndipo B.C.E. amaimira nthawi yakale anthu asanayambe kugwiritsira ntchito C.E. Komabe, kwa zaka 70 zimene ndakhala ndi moyo, ndaona B.C. ndi A.D zikugwiritsidwa ntchito kuimira Yesu asanabadwe ndiponso atafa. Choncho, ndikuona kuti anthu amene amagwiritsira ntchito B.C.E. kapena C.E., sakhulupirira za kubadwa kwa Yesu.

R. W., United States

Yankho la “Galamukani!”: Ngakhale kuti A.D. (Anno Domini, kapena kuti “chaka cha Ambuye wathu”) ndi B.C. (Khristu asanabadwe), zimagwiritsidwa ntchito kwambiri m’mayiko achikhristu, ife tinasankha kugwiritsira ntchito C.E. (Nyengo yathu ino) ndiponso B.C.E. (Nyengo yathu ino isanafike). Tachita zimenezi pazifukwa zingapo. Choyamba, pali umboni wokwanira wosonyeza kuti Yesu anabadwa m’chaka cha 2 B.C.E. Chachiwiri, mabuku ndi magazini a Mboni za Yehova amatulutsidwa m’zinenero zina zoti anthu ake si Akhristu. Chachitatu, mawu akuti “Khristu” amatanthauza “Wodzozedwa.” Koma Yesu anakhala Mesiya kapena kuti Khristu pomwe anadzozedwa ndi mzimu wa Mulungu paubatizo wake mu 29 C.E. (Mateyo 3:13-17) Choncho, iye sanabadwe ali Khristu koma anakhala Khristu atabatizidwa. Komanso mawu akuti C.E. ndi B.C.E. akugwiritsidwa ntchito kwambiri masiku ano, ndipo ngakhale mabuku ambiri otanthauzira mawu ndiponso mabuku ena, akugwiritsa ntchito mawu amenewa. Dziwani kuti Mboni za Yehova zimadziwa kuti Yesu komanso nsembe yake n’zofunikira kwambiri pantchito yopulumutsa anthu komanso pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu.

Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Kodi Ndingatani Ngati Ndili Ndi Matenda Aakulu Kapena Chilema? (February 2008) Ndinasangalala kwambiri kuwerenga magazini amenewa. M’mbuyomu ndinadwala kwambiri ndipo anandigoneka m’chipatala kwa milungu itatu. Nthawi imene ndinalandira magaziniyi n’kuti atanditulutsa kumene. Ndinaona kuti ndakumana ndi zinthu zofanana ndi achinyamata amene anatchulidwa m’nkhani imeneyi. Ndikukuthokozani kwambiri chifukwa cha malangizo amene ali m’nkhaniyi.

K. P., Canada

Ndinasangalala kwambiri kudziwa kuti Yehova Mulungu amatonthoza ngakhale anthu olumala ngati ineyo. Ndili mwana anandipeza ndi matenda a muubongo owumitsa ziwalo. Ngakhale kuti sindingayende, ndimalalikirabe maola 50 mwezi uliwonse. Ndikuyembekezera dziko lapansi la Paradaiso pamene onse olumala “adzatumpha ngati nswala.”—Yesaya 35:5, 6.

J. J., Republic of Korea

Ndawerenga nkhaniyi kambirimbiri. Ndinalira nditamva mmene Yehova amaonera anthu olumala. Ndaona kuti Yehova amatiteteza kuti tisavulazidwe. Zikomo kwambiri.

M. T., Japan

Kodi Imfa Ndi Mapeto a Zonse? (December 2007) Mayi anga anamwalira miyezi inayi ndisanalandire magaziniyi. Choncho, zimene nkhani imeneyi inafotokoza, makamaka zakuti akufa adzauka, zinandilimbikitsa kwambiri. Zikomo kwambiri. Nkhaniyi yanditonthoza kwambiri.

M. R., Madagascar