Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ Kafukufuku wina wasonyeza kuti pafupifupi 33 peresenti ya zamoyo zimene zimapanga miyala yokongola ya pansi pamadzi zikutha chifukwa cha kusintha kwa nyengo kapena chifukwa chakuti anthu akuwononga zachilengedwe.—SCIENCE, U.S.A.
▪ Pa ana oposa 2, 000 amene ali ndi matenda ovutika kupuma omwe anawapima pa chipatala cha ana mumzinda wa Athens ku Greece, panapezeka kuti ana 65 pa 100 alionse anali ndi vutoli ndipo linayamba chifukwa chakuti mmodzi wa makolo awo kapena onse awiri amasuta fodya.”—KATHIMERINI—ENGLISH EDITION, GREECE.
▪ Kukwera mtengo kwa mafuta ndiponso zinthu zofunika pamoyo, . . . kulowa pansi kwa zachuma . . . , ndiponso kuwonjezereka kwa masoka achilengedwe, zikungosonyeza kuti tilibe njira yeniyeni yothetsera mavuto amenewa.”—LLUÍS MARIA DE PUIG PRESIDENT OF PARLIAMENTARY ASSEMBLY OF THE COUNCIL OF EUROPE.
▪ M’chaka cha 2006 ku Poland, anyamata 17 pa 100 alionse ndiponso atsikana 18 pa 100 alionse anagwiritsapo ntchito mankhwala osokoneza bongo ali ndi zaka 15.—ŻYCIE WARSZAWY, POLAND.
Mikango ndi Anthu Zikuphana
Magazini ina ya ku Cape Town inanena kuti: “Nthawi zambiri anthu akumapha mikango, mikangonso ikumapha anthu.” Zimenezi zikuchitika chifukwa chakuti nyama zakuthengo zikusowa pokhala kaamba ka kuchuluka kwa anthu. (Africa Geographic) Zikuoneka kuti mikango “ikaona anthu ikumayesa ngati yapeza chakudya.” Mwachitsanzo kuyambira mu 1990, mikango yakhala ikupha anthu 70 chaka chilichonse ku Tanzania. Magaziniyi inanenanso kuti nthawi zina mikango “ikumagwira anthu panyumba zawo popasula madenga ndiponso kugumula makoma a nyumbazo.”
Apeza Nkhokwe Zakale ku Egypt
Akatswiri ofukula zinthu zakale a ku yunivesite ya Chicago apeza nkhokwe 7 kum’mwera kwa Egypt. Nkhokwezi ndi zazikulu kwambiri kuposa nkhokwe zonse zakale m’dzikolo. Zinthu zina zimene apeza pafupi ndi pomwe anapeza nkhokwezi zathandiza kwambiri akatswiri kudziwa kuti nkhokwezi zinamangidwa pakati pa 1630 ndi 1520 B.C.E. Ngati zakazi n’zolondola, ndiye kuti nkhokwezi zinamangidwa m’nthawi ya Mose. Nkhokwezi n’zozungulira, zomangidwa ndi njerwa, zazikulu mamita 5.5 mpaka 6.5 m’mimba mwake ndipo n’zazitali mamita 7.5. Nkhokwezi zinali zaboma. Lipoti la ku yunivesiteyi linafotokozanso kuti malo ngati amenewa “ankagwiritsidwa ntchito ndi boma posungira zakudya zimene anthu okhala mphepete mwa mtsinje wa Nile ankakolola. Olamulira a ku Iguputo ankagwiritsira ntchito zokololazo polimbitsa ulamuliro wawo.” Magaziniyi inanenanso kuti: “Anthu ankatenga zokololazo ngati ndalama, choncho nkhokwezi zinali ngati banki ndiponso mosungira chakudya.”
Mapepala Olimba Ngati Chitsulo
Akatswiri ofufuza zinthu a ku yunivesite ina ku Sweden, atulukira njira ina yopangira mapepala olimba pogwiritsa ntchito makungwa a mitengo. Nthawi zambiri opanga mapepala amapanga mapepala opyapyala chifukwa choti amachepetsa mphamvu ya timaulusi tamitengo yopangira mapepalayo. Koma akatswiriwa apeza njira yosungunulira timaulusiti ndi mankhwala, kenako n’kuchotsa zinthu zosafunikazo m’madzi pogwiritsa ntchito makina. Timaulusiti tikauma, timagwirana n’kupanga mapepala olimba kwambiri ngati chitsulo.