Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ana Amalikonda Bukuli

Ana Amalikonda Bukuli

Ana Amalikonda Bukuli

▪ Ana a zaka zosiyanasiyana amakonda kwambiri buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Mtsikana wina analemba kuti: “Bukuli lili ndi zinthu zambiri zimene ndimazikonda. Mwachitsanzo, lili ndi zithunzi zokongola kwambiri. Powerenga bukuli, ndinkatenga nthawi yaitali kuganizira mafanizo ake ndi mmene akugwirizanira ndi nkhaniyo.

“Chinthu chinanso chomwe ndimakondera bukuli n’chakuti mawu ake ndi osavuta kumva, ndipo zimenezi zimachititsa kuti munthu uzingofunabe kuliwerenga.

“Nditawerenga bukuli ndinachita chidwi kwambiri ndi mmene limafotokozera mavuto amene timakumana nawo masiku ano ndi mmene tingawapewere. Mitu yomwe ndinasangalala nayo kwambiri ndi yakuti, ‘Tifunika Kukana Ziyeso,’ ‘Phunziro la Kukhala Wokoma Mtima,’ ndiponso ‘Kodi Nthawi Zonse Umafuna Kukhala Woyamba?’”

Mukhoza kuitanitsa buku la zithunzi zokongola la masamba 256 limeneli. Masamba a bukuli ndi aakulu mofanana ndi a magazini ino. Mukhoza kuitanitsa bukuli polemba adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.