Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kukachitika Ngozi Mumadziwitsa Ndani?

Kodi Kukachitika Ngozi Mumadziwitsa Ndani?

Kodi Kukachitika Ngozi Mumadziwitsa Ndani?

Tikangolandira uthenga woti kwinakwake kwachitika ngozi, timadina batani la mu ambulansi yathu ndipo nyali ya pamwamba imayamba kung’anima. Anthu oyenda pansi ndiponso magalimoto akangomva kulira kwa ambulansi, amatipatsa mpata kuti tidutse pokathandiza anthu kumalo a ngozi.

NDAKHALA ndikugwira ntchito yothandiza anthu pangozi kwa zaka zoposa 20. * Tsiku lililonse tikayamba ntchito, sitidziwa kuti tikumana ndi zotani. Ndakumanapo ndi ngozi zosiyanasiyana pantchito yanga, zina zoopsa koma zina zosaopsa kwenikweni. Ndipo anthu ena amene ndawathandiza anachira koma ena anamwalira.

Timathandiza Kwambiri Anthu

Ku Canada, * anthu othandiza anzawo pangozi amagwira ntchito yofunika kwambiri. Thandizo limene amapereka kwa munthu asanam’pititse kuchipatala, lingachititse kuti munthuyo asafe, asamve kupweteka kwambiri kapena kuti vutolo lisakule kwambiri.

M’mayiko ena, anthu othandiza anzawo pangozi amapezeka maola 24 patsiku, masiku 365 pachaka. Iwo amatha kulembedwa ntchito ndi boma, makampani kapena zipatala. Ena amayenda pa ambulansi ndipo ena pagalimoto yozimitsa moto.

Anthu ogwira ntchito imeneyi sachedwa kufika pamalo angozi akangolandira uthenga. Uthengawo umatha kuwapeza nthawi ina iliyonse, mwinanso asakuyembekezera. Kodi ntchito yawo ndi yotani?

Timaphunzitsidwa Kupulumutsa Anthu

Ku Canada, anthu othandiza anzawo pangozi ali m’magulu osiyanasiyana m’madera osiyanasiyananso. Nthambi za boma komanso zipatala, zimafuna kuti munthu akhale ndi satifiketi asanalembedwe ntchito imeneyi.

Ku Canada kuno, kuti munthu ayambe ntchito imeneyi, amafunika kuphunzira masiku ambiri m’kalasi, m’chipatala ndiponso mu ambulansi. Timaphunzira mmene tingayezere anthu ndi kuwathandiza kuti azipuma bwino. Komanso timaphunzira kuthandiza anthu omwe mtima wawo wasiya kugunda. Timaphunziranso mmene tingamangire anthu mabandeji ndiponso kuthandiza anthu amene athyoka msana.

Kenako kwa milungu iwiri timaphunzira kusamalira odwala m’chipinda cha anthu ovulala pangozi, cha anthu odwala kwambiri ndiponso choberekera ana m’zipatala zosiyanasiyana. Ndimakumbukirabe nthawi yoyamba imene ndinathandiza kubadwitsa mwana. Zimenezi ndiponso zochitika zina zinandithandiza kukonzekera maphunziro a pa ambulansi, amene ananditengera milungu inanso iwiri. Ndinkaphunzitsidwa ndi anthu awiri othandiza anzawo pangozi. Nditakhoza mayeso, ndinapatsidwa satifiketi ndipo ndinayamba ntchito yothandiza anthu pangozi.

Nditamaliza maphunziro anga, ndinagwira ntchito m’madera osiyanasiyana, a m’midzi ndiponso a m’tawuni. Pasanapite nthawi, ndinapulumutsa munthu wogwira ntchito ya zomangamanga ndipo ndinazindikira kuti ntchito yanga ndiyofunika kwambiri. Iye ankamva kuwawa pachifuwa ndipo anafikira kumalo olandirira anthu ovulala pangozi. Atangofika, anakomoka ndipo mtima wake unasiya kugunda. Ndinathandizana ndi madokotala komanso manesi kuika makina amagetsi pachifuwa pa munthuyo kuti mtima wake uyambenso kugunda bwinobwino. Patangopita mphindi zochepa, mtima wake unayambanso kugunda ndipo anayamba kupuma bwinobwino. Kenako iye anaikidwa m’chipinda cha anthu odwala mwakayakaya. Tsiku lotsatira, ndinapita ndi dokotala m’chipindachi ndipo tinam’peza munthuyu atakhala pabedi akulankhula ndi mkazi wake. Ine sindinamuzindikire mpaka pamene ananena kuti: “Mwandikumbukira? Ndinu munandipulumutsa dzulo.” Ndinasangalala kwambiri kumva mawu amenewa.

Nditatsala pang’ono kumaliza maphunziro anga, ndinagwira ntchito ndi dokotala wina kwa maola 12. Dokotalayu ankaona mmene ndinkasamalirira odwala. Kenako ndinakhoza mayeso ndipo ndinapatsidwa satifiketi yapamwamba kuposa yoyamba ija.

Othandiza anthu pangozi amayang’aniridwa ndi mkulu wachipatala, yemwe nthawi zambiri amathandizana ndi komiti ya alangizi a zachipatala polemba malangizo a mmene angasamalirire odwala. Othandiza anthu pangozi amatsatira malangizo amenewa komanso amalankhulana pawailesi kapena pafoni ndi gulu lina la madokotala. N’chifukwa chake othandiza anzawo pangozi amatchedwa maso, makutu ndi manja a madokotala. Timathandiza anthu m’zipatala, m’nyumba zawo kapena pamalo angozi. Timathandiza anthu kuyambanso kupuma, kuwapatsa mankhwala, kuwathandiza kuti mtima uyambenso kugunda ndiponso kuwachita opaleshoni.—Onani bokosi lakuti  “Njira Zopulumutsira Anthu.”

Mavuto Amene Timakumana Nawo

Pafupifupi tsiku lililonse, timakumana ndi mavuto pantchito yathu. Timagwira ntchito m’nyengo iliyonse ndipo nthawi zina m’malo oopsa. Nthawi zinanso timadutsa m’misewu yoopsa kuti tikafike kumalo kumene kwachitikira ngozi.

N’zosavutanso kutenga matenda chifukwa nthawi zina timatha kugwira magazi kapena madzi a m’thupi. Kuti tisatenge matenda, timavala zinthu zoteteza m’manja, kumaso, ndiponso thupi lonse.

Nthawi zina, achibale a odwalawo, anzawo, kapena anthu ena amativutitsa. Anthu amenewa amatha kutipsera mtima n’kutichitira zomwe sitimayembekezera. Zimamvetsa chisoni kwambiri ngati mwamuna kapena mkazi wamwalira pambuyo pokhala nthawi yaitali limodzi. Zimavuta kudziwitsa winayo za imfa ya mwamuna kapena mkazi wake. Mwachitsanzo, panthawi ina ndinauza mkazi wina kuti mwamuna wake wamwalira. Iye atangomva zimenezi, anandimenya ndipo anatuluka m’nyumba n’kuyamba kuthamanga mumsewu kwinaku akulira. Nditamuthamangira ndinamupeza ndipo anandikumbatira ndi kuyamba kulira kwambiri.

Timafunikanso kukhala omvetsa, ochenjera komanso okoma mtima pothandiza anthu osokonekera maganizo kapena oledzera, chifukwa sudziwa kuti anthu otere akuchitira chiyani. Pazaka zomwe ndakhala pa ntchitoyi, ndalumidwapo, kulavuliridwa, ndiponso kumenyedwa ndi odwala.

Ntchitoyi imafuna mphamvu chifukwa nthawi zambiri timanyamula zolemera. Tikamathandiza odwala, timagwada ndiponso kuwerama nthawi yaitali. Anthu amathanso kuvulala ali pantchitoyi. Ambiri ogwira ntchitoyi amavulala msana, mapewa ndi mawondo. Ena amatha kuvulala kwambiri moti sangathenso kugwira ntchitoyi. Popeza kuti timagwira ntchito masana komanso usiku, timatopa kwambiri.

Kusamalira anthu amene akudwala matenda akayakaya kapena amene avulala kwambiri, n’kotopetsa. Othandiza anthu pangozi amafunika kudekha ndiponso kuganiza bwino panthawi ya ngozi. Anthu amenewa amaona ndi maso awo anthu akuvutika ndiponso akufa. Amathandiza anthu amene avulala modetsa nkhawa. Sindiiwala mnyamata wina amene anavulala kwambiri kuntchito moti zinali zovuta kumuzindikira. Iye anatipempha ineyo ndi mnzanga kuti timuthandize kuti asafe. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ngakhale kuti ifeyo ndiponso madokotala ndi manesi tinayesetsa kwambiri kumuthandiza, mnyamatayu anamwalira pasanathe ola limodzi.

Ngozi zina zimakhala zochititsa mantha kwambiri. Mwachitsanzo, tsiku lina m’mawa tinalandira uthenga wakuti nyumba inayake ikupsa. Pamene mwamuna wa panyumbapo anafika kuchokera kuntchito, anapeza nyumba yake ikuyaka. Mkazi ndiponso mwana wake wazaka zitatu anali atapulumutsidwa. Koma ana ena atatu amisinkhu yoyambira miyezi inayi mpaka zaka zisanu komanso agogo awo aamuna analephera kutuluka mpaka anthu ozimitsa moto anabwera kudzawatulutsa. Anthuwa anavulala kwambiri ndipo gulu lathu ndi magulu ena a anthu othandiza anzawo pangozi tinayesetsa kuwapulumutsa koma n’zomvetsa chisoni kuti ntchito yathu inapita pachabe chifukwa anthuwa anamwalira.

Pazonse zimene ndafotokozazi, mwina mukudzifunsa kuti, ‘Kodi n’chifukwa chiyani anthu amayamba ntchito imeneyi?’ Inenso nthawi zina ndimadzifunsa funso limeneli. Koma ndimakumbukira za fanizo la Yesu la Msamariya wachifundo amene anadzipereka kuthandiza munthu wina wovulala. (Luka 10:30-37) Kugwira ntchito yothandiza anthu pangozi kumafunadi munthu wodzipereka kwambiri. Ineyo ndimasangalala kugwira ntchito imeneyi, komabe ndikudziwa kuti m’tsogolomu ndidzakhala lova chifukwa Mulungu analonjeza kuti posachedwapa palibe munthu amene adzanena kuti: “Ine ndidwala.” Ndiponso ‘imfa kapena kulira sizidzakhalaponso.’ (Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:4)—Yosimbidwa ndi munthu wothandiza anthu pangozi ku Canada.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Kuti mudziwe ngati ntchito yothandiza anthu pangozi ingatsutsane ndi chikumbumtima cha Mkhristu, onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1999, tsamba 29, ndi ya Chingelezi ya April 1, 1975, tsamba 215 mpaka 216.

^ ndime 5 M’mayiko ena, anthu othandiza anzawo pangozi sakhala ndi ambulansi. Choncho, woyendetsa galimoto ndi amene amafunika kupita mwamsanga ku chipatala ndi anthu ovulala.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

Ine sindinamuzindikire mpaka pamene iye anandifunsa kuti: “Mwandikumbukira? Ndinu munandipulumutsa dzulo.” Ndinasangalala kwambiri kumva mawu amenewa

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Pazaka zomwe ndakhala pantchitoyi, ndalumidwapo, kulavuliridwa, ndiponso kumenyedwa ndi odwala

[Bokosi/Chithunzi patsamba 15]

 NJIRA ZOPULUMUTSIRA ANTHU

Munthu wothandiza ena pangozi amaphunzitsidwa kuonetsetsa kuti wodwala akupuma bwino. Kuti achite zimenezi, nthawi zina pamafunika kumuika paipi yofewa yoti azipumira. Paipiyi amaidutsitsa mkamwa mpaka kummero. Nthawi zinanso pangafunike kung’amba pakhosi n’kuika paipiyo. Amathanso kuika paipi kudzera pachifuwa ngati munthuyo akudwala mwakayakaya ndiponso ngati mapapo ake asiya kugwira ntchito.

Njira ina ndiyo kuika paipi mu mtsempha. Amagwiritsa ntchito singano poika paipi mu mtsempha wa magazi. Choncho, zinthu zina monga madzi amchere zimaikidwa m’thupi kudzera mu paipi imeneyi. Nthawi zina amaika paipi mu fupa n’cholinga choti aikemo mankhwala.

Njira ina n’kugwiritsa ntchito makina pofuna kuona mmene mtima ukugundira. Akaona kuti mtima sukugunda bwino, amagwiritsa ntchito makina omwe amachititsa wodwalayo kugwidwa shoko. Zimenezi zimachititsa kuti mtima uyambe kugunda bwino. Makina amenewa amagwiritsidwanso ntchito pothandiza munthu amene mtima wake ukugunda pang’onopang’ono kuti uzigunda mofulumira.

[Mawu a Chithunzi]

All photos: Taken by courtesy of City of Toronto EMS

[Mawu a Chithunzi patsamba 12]

Taken by courtesy of City of Toronto EMS