Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Chalakwika N’chiyani Pachithunzichi?

Werengani Yoswa 2:15-18; 6:15-21; 7:1, 20, 21. Ndiyeno onani chithunzichi. N’chiyani chalakwika pachithunzichi? Lembani mayankho anu m’mizere yomwe ili m’munsiyi.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

4. ․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi Mulungu amamuona bwanji munthu amene watenga zinthu zomwe si zake?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 5 Kodi Danieli ankadziwika chifukwa chiyani ? Danieli 6:․․․

TSAMBA 6 Kodi anthu ayenera kuzindikira chiyani za inuyo? Afilipi 4:․․․

TSAMBA 28 Kodi ukwati uyenera kukhala wotani pakati pa onse? Aheberi 13:․․․

TSAMBA 28 Kodi chilakolako chikatenga pathupi, chimabala chiyani? Yakobe 1:․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pachithunzi chilichonse.

Kodi Mumadziwa Chiyani za Aneneri?

Werengani 2 Mbiri 18:1–19:3. Ndiyeno yankhani mafunso otsatirawa.

5. ․․․․․

Tchulani dzina la mneneri amene mfumu Ahabu ankadana naye?

6. ․․․․․

N’chifukwa chiyani Ahabu ankadana ndi mneneri ameneyu?

7. ․․․․․

Kodi mneneriyu anamuuza chiyani Ahabu ndipo Ahabu anatani?

KAMBIRANANI:

Kodi ndi panthawi iti imene mungafunikire kulimba mtima ngati mneneriyu?

▪ Mayankho ali pa tsamba 14

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Makoma a Yeriko anagwa Aisiraeli asanaukire mzindawo.

2. Chingwe chimene Rahabi anatsitsa chinali chofiira osati cha buluu.

3. Akani anaba malaya, chikute cha golide, masekeli a siliva, osati fano

4. Sanaukire usiku.

5. Mikaya.

6. Ananena zoti Yehova aweruza Ahabu.

7. Kuti Ahabu akagonja ku nkhondo. Ahabu anatsekera Mikaya m’ndende.