Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzindisangalatsa?

Kodi Ndingatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzindisangalatsa?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzindisangalatsa?

Kodi mumawerenga Baibulo pafupipafupi motani? (Chongani yankho limodzi)

□ Tsiku lililonse

□ Mlungu uliwonse

□ Yankho lina ․․․․․

Malizani chiganizo chotsatirachi.

Kuwerenga Baibulo kukamapanda kundisangalatsa, chimakhala chifukwa chakuti . . . (Chongani zonse zimene zimakuchititsani)

□ Zimene ndikuwerengazo sizikundisangalatsa

□ Limandisokoneza

□ Ndimasokonezeka ndi zochitika zina

□ Zifukwa zina ․․․․․

KODI kuwerenga Baibulo sikukusangalatsani? Ngati ndi choncho, mwina mungavomereze zimene mnyamata wina wazaka 18, dzina lake Will, ananena. Iye anati: “Baibulo silisangalatsa ngati sudziwa kawerengedwe kake.”

N’chifukwa chiyani mufunika kudziwa mmene mungawerengere Baibulo? Baibulo lingakuthandizeni kudziwa mmene

mungasankhire zochita

mungapezere anzanu apamtima

mungathetsere nkhawa

Baibulo lili ndi malangizo abwino pankhani zimenezi ndi zinanso zambiri. N’zoona kuti pamafunika khama kuti mupeze malangizo amenewa. Komabe kuchita zimenezi kuli ngati kufunafuna chuma. Mukachivutikira kwambiri, mumasangalala kwambiri mukachipeza.—Miyambo 2:1-5.

Kodi malangizo a m’Baibulo mungawapeze bwanji? Kabokosi kamene kali kumanjaka kangakuthandizeni kudziwa zimene mungawerenge ndiponso mmene mungawerengere (onani kabokosi kakuseri). Yesaninso kutsatira mfundo zimene mukuona kuti zingakuthandizeni, pamasamba otsatirawa.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

Ngati mumagwiritsa ntchito Intaneti, mungawerenge Baibulo pa adiresi iyi, www.pr418.com.

ZOTI MUGANIZIRE

Anthu amanena kuti kanthu n’khama.

▪ Kodi zimenezi zikugwirizana bwanji ndi kuwerenga Baibulo?

▪ Kodi ndi nthawi iti imene mungamawerenge Baibulo?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 23]

MMENE MUNGAWERENGERE BAIBULO

Musanayambe kuwerenga . . .

▪ Onetsetsani kuti mwasankha malo opanda phokoso.

▪ Pempherani kuti mumvetse zimene mukuwerengazo.

Mukamawerenga . . .

▪ Gwiritsani ntchito mapu ndi zithunzi zokhudza nkhani za m’Baibulo kuti muziona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika.

▪ Ganizirani za malo amene nkhaniyo ikuchitikira ndiponso mfundo zofunika za m’nkhaniyo.

▪ Onani mawu amunsi ndi malemba ena ofotokoza nkhaniyo.

▪ Dzifunseni mafunso monga awa:

MFUNDO: Kodi zimenezi zinachitika liti? Ndani analankhula mawu amenewa? Ndipo ankauza ndani?

TANTHAUZO: Kodi ndingamufotokozere bwanji munthu wina nkhani imeneyi?

PHINDU: Kodi n’chifukwa chiyani Yehova Mulungu analemba nkhani imeneyi m’Mawu ake? Kodi nkhaniyi ikundiuza chiyani za khalidwe lake komanso mmene amachitira zinthu? Kodi nkhaniyi ingandithandize bwanji pamoyo wanga?

Mukamaliza kuwerenga . . .

▪ Fufuzani mfundo zina. Gwiritsani ntchito mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova otsatirawa ngati muli nawo: Insight on the Scriptures ndi “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial.”

▪ Pempheraninso. Muuzeni Yehova mfundo zimene mwawerenga ndi mmene mukufunira kuzigwiritsira ntchito. Muthokozeni chifukwa cha Mawu ake, Baibulo.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]

 KODI MUNGAWERENGE MOTANI BAIBULO?

Mungasankhe izi:

□ Kuwerenga kuyambira buku loyamba mpaka lomaliza.

□ Kuwerenga motsatira nthawi imene mabuku a m’Baibulo analembedwa kapena nthawi imene zinthu zinachitika.

□ Kuwerenga malemba ochokera mbali zosiyanasiyana za Baibulo tsiku lililonse.

Lolemba: Nkhani zosangalatsa zokhudza mbiri yakale (Genesis mpaka Estere)

Lachiwiri: Moyo wa Yesu ndi zimene ankaphunzitsa. (Mateyo mpaka Yohane)

Lachitatu: Mpingo wakale wachikhristu (Machitidwe)

Lachinayi: Ulosi ndi malangizo ofunika pamoyo (Yesaya mpaka Malaki, Chivumbulutso)

Lachisanu: Ndakatulo ndi nyimbo (Yobu, Masalmo, Nyimbo ya Solomo)

Loweruka: Nzeru zofunika pamoyo (Miyambo, Mlaliki)

Lamlungu: Makalata opita ku mipingo (Aroma mpaka Yuda)

Mulimonse mmene mungawerengere, onetsetsani kuti mukutsatira ndandanda yanu. Mukamaliza kuwerenga chaputala chilichonse, chongani kapena gwiritsani ntchito chizindikiro china chilichonse.

Dulani kabokosika ndi kukasunga m’Baibulo lanu.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]

MUZISANGALALA POWERENGA BAIBULO

Pezani njira zokuthandizani kusangalala ndi zimene mukuwerenga. Mwachitsanzo:

□ Mukamawerenga maina a anthu, muziwaika m’magulu mogwirizana ndi chibale chawo.

□ Lembani tchati. Mwachitsanzo, mukamawerenga za munthu wina wokhulupirika, gwirizanitsani makhalidwe ndiponso zochita za munthuyo ndi madalitso amene anapeza.—Miyambo 28:20.

[Chithunzi]

Bwenzi la Mulungu

Kumvera

Kukhulupirika

↑ ↑

Abulahamu

□ Jambulani zithunzi zofotokoza nkhaniyo.

□ Jambulani zithunzi zosavuta kujambula zofotokoza zimene zikuchitika m’nkhaniyo. Fotokozani zimene zikuchitika m’chigawo chilichonse cha nkhaniyo.

□ Jambulani zithunzi za zinthu zimene mukuwerenga. Mwachitsanzo chombo cha Nowa. Onani Galamukani! ya January 2007, tsamba 22.

Werengani mokweza pamodzi ndi anzanu kapena achibale anu. Mungauze munthu mmodzi kuti awerenge nkhaniyo ndipo enanu mungamawerenge mawu a anthu ena amene akupezeka m’nkhaniyo.

□ Sankhani nkhani ndipo isintheni kuti mukhale ngati mukuwerenga nkhaniyo pa wailesi kapena pa TV. Powerenga nkhaniyo mungafunse mafunso munthu amene akuimira mwininkhani kapena amene akuimira anthu amene analipo pamene nkhaniyo inkachitika.

□ Sankhani nkhani imene mwiniwake anachita zinthu zoipa ndipo ganizirani zimene akanachita kuti zinthu zimuyendere bwino. Mwachitsanzo, ganizirani mmene Petulo anakanira Yesu. (Maliko 14:66-72) Kodi Petulo akanatani panthawiyo kuti zinthu zimuyendere bwino?

□ Onerani kapena mvetserani masewero a m’Baibulo.

Lembani sewero lanu. Sonyezanimo phunziro limene anthu angapeze m’nkhaniyo.—Aroma 15:4.

NGATI MUNGAKONDE: Chitani seweroli ndi anzanu.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 25]

KUTI KUWERENGA BAIBULO KUZIKUSANGALATSANI:

▪ Khalani ndi cholinga. Lembani pansipa tsiku limene mukufuna kuyamba kuwerenga Baibulo.

․․․․․

▪ Sankhani buku la m’Baibulo limene limakusangalatsani. Onani bokosi lakuti  “Zimene Mungawerenge M’Baibulo.” Kenako lembani pansipa mbali ya Baibulo imene mukufuna kuyamba kuwerenga.

․․․․․

▪ Yambani ndi kuwerenga nthawi yochepa. Mphindi 15 n’zokwanira kusiyana ndi kusawerenga n’komwe. Lembani pansipa kuchuluka kwa nthawi imene mungamathere kuwerenga Baibulo.

․․․․․

Mungachite izi: Khalani ndi Baibulo loti muzingoligwiritsa ntchito powerenga basi. Muzilembamo mfundo zanu. Muzichonga mavesi amene mumawakonda.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 25]

ZIMENE ANZANU AMANENA

“Ndimayesetsa kuwerenga Baibulo mavesi ochepa tsiku lililonse ndisanagone. Zimenezi zimandithandiza kuti ndiganizire mfundo inayake yabwino.”—Anatero Megan.

“Ndimawerenga vesi limodzi kwa mphindi 15. Ndipo ndimawerenga mawu a m’munsi, mavesi ena ofotokoza mfundo yofanana ndi ya vesilo, ndiponso kufufuza m’mabuku ena. Nthawi zina sindimaliza kufufuza mfundo zonse za vesi limodzi, koma ndimadziwa zambiri chifukwa chowerenga chonchi.”—Anatero Corey.

“Ndinawerengapo Baibulo lonse kwa miyezi 10. Ndipo zinandithandiza kuona kugwirizana kwa nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo zimene poyamba sindinkazimvetsa.”—Anatero John.

[Bokosi patsamba 25]

MUFUNIKA KUSANKHA

Sankhani nkhani. M’Baibulo muli nkhani zambiri zosangalatsa zimene zinachitikadi. Sankhani nkhani imene imakusangalatsani ndipo iwerengeni yonse.

Mungachite izi: Pezani mfundo zina zokuthandizani kumvetsa nkhaniyo m’buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, tsamba 292. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Sankhani Buku la Uthenga Wabwino. Werengani buku la Mateyo (buku loyamba la Uthenga Wabwino), buku la Maliko (lomwe lili ndi nkhani zambiri zochititsa chidwi), buku la Luka (lomwe limanena kwambiri za pemphero ndiponso za akazi), kapena buku la Yohane (lomwe lili ndi nkhani zambiri zomwe sizinalembedwe m’mabuku ena a Uthenga Wabwino).

Mungachite izi: Musanayambe kuwerenga, onani mwachidule zinthu zina zokhudza bukulo ndiponso amene analemba kuti mumvetsa mmene bukulo likusiyanira ndi mabuku ena a Uthenga Wabwino.

Sankhani chaputala m’buku la Masalmo. Mwachitsanzo:

Ngati mukusowa anzanu ocheza nawo, werengani Salmo 142.

Ngati mwakhumudwa chifukwa cha zolakwa zanu, werengani Salmo 51.

Ngati mumakaikira phindu la malangizo a Mulungu, werengani Salmo 73.

Mungachite izi: N’zothandiza kulemba mabuku onse a Masalmo amene mwawerenga komanso amene mukuona kuti amakulimbikitsani.

[Chithunzi patsamba 26]

FUFUZANI MOZAMA

Yesani kuchita izi: Onani nthawi yomwe zimene mukuwerengazo zinachitika, malo ndiponso zochitika zokhudza nkhaniyo.

Chitsanzo: Werengani Ezekieli 14:14. Kodi Danieli anali ndi zaka zingati pamene Yehova ananena kuti iye, Nowa komanso Yobu ndi zitsanzo zabwino?

Zokuthandizani: Chaputala 14 cha Ezekieli chinalembedwa patatha zaka zisanu kuchokera pamene Danieli anagwidwa ukapolo n’kupita ku Babulo. Mwina panthawiyi anali asanakwanitse zaka 20.

Mfundo yofunika: Kodi Danieli anali wamng’ono kwambiri moti Yehova sakanatha kuona kukhulupirika kwake? Kodi anatani kuti Mulungu amudalitse? (Danieli 1:8-17) Kodi chitsanzo cha Danieli chingakuthandizeni bwanji inuyo posankha zochita?

Onani mfundo zonse. Nthawi zina pavesi pamakhala mawu amodzi kapena awiri ofunika.

Chitsanzo: Yerekezerani Mateyo 28:7 ndi Maliko 16:7. N’chifukwa chiyani Maliko analemba mfundo yakuti Yesu anaonekera kwa ophunzira ake, “komanso [kwa] Petulo”?

Zokuthandizani: Maliko sanaone ndi maso zinthu zonse zomwe zinachitika; ndipo zikuoneka kuti zimene analembazo anachita kumva kwa Petulo.

Mfundo yofunika: Kodi n’chifukwa chiyani Petulo ayenera kuti analimbikitsidwa atamva kuti Yesu akufunanso kuonana naye? (Maliko 14:66-72) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali mnzake wapamtima wa Petulo? Kodi mungatsanzire bwanji Yesu kuti ena azikuonani kuti ndinu mnzawo weniweni?

Fufuzani m’mabuku ena. Werengani mabuku ofotokoza Baibulo kuti mudziwe zochuluka.

Chitsanzo: Werengani Mateyo 2:7-15. Kodi okhulupirira nyenyezi anapita liti kukaona Yesu?

Zokuthandizani: Onani Nsanja ya Olonda ya January 1, 2008, tsamba 31, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Mfundo yofunika: Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yehova anasamalira Yesu ndi makolo ake mwakuthupi ku Iguputo? Kodi kukhulupirira Yehova kungakuthandizeni bwanji kuchepetsa nkhawa?—Mateyo 6:33, 34.