Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ 25 peresenti ya mitundu ina ya nsomba, achule, njoka, mbalame ndiponso zinyama zina inatheratu pazaka 35 zokha, kuyambira 1970 kufika 2005.—SÜDDEUTSCHE ZEITUNG, GERMANY
▪ Polimbana ndi mavuto azachuma, mu August, 2008, boma la Zimbabwe linachotsa mazilo 10 pa ndalama zake. Zimenezi zikutanthauza kuti madola 10 biliyoni azikhala dola imodzi.—AGENCE FRANCE PRESSE, ZIMBABWE
▪ “Anthu opitirira 12,000 anaphedwa ndi mfuti ku U.S.A. m’chaka cha 2005. Koma chiwerengero cha anthu amene anavulala chifukwa chowomberedwa ndi mfuti chinali chachikulu kwambiri chifukwa mu 2006 anthu ovulala ndi mfuti analipo pafupifupi 53,000 m’zipatala.”—THE SEATTLE TIMES, U.S.A.
Zochitika pa Khirisimasi
Nyuzipepala ina ya ku Australia inanena kuti pafupifupi maukwati 20 pa 100 alionse ku Australia amatha panthawi ya chikondwerero cha Khirisimasi ndi chaka chatsopano. (Sunday Telegraph) Loya wina amene amaimira anthu amene akufuna kusudzulana, dzina lake Barry Frakes, anati: “Timaona mabanja ambiri akumenyana komanso kutha tikangoyambanso ntchito kuchokera kutchuti. Anthu amaganiza kuti nyengo ya Khirisimasi ndi yosangalatsa ngati mmene amaisonyezera pa TV. Koma akaona kuti sanakwanitse kuchita zimene anaonera pa TV, amaganiza zothetsa ukwati wawo.” Koma Angela Conway, yemwe ndi mneneri wa bungwe lina loona za mabanja ku Australia, anati: “Kusudzulana sikuthetsa mavuto a m’banja omwe komanso sikubweretsa mtendere umene anthu amaganiza kuti aupeza.” Iye ananenanso kuti: “Ndibwino kuti anthu asamasudzulane koma aziyesetsa kuthetsa mavuto awo.”
Nyumba Zoberekeramo Ana Zikuthandiza Kwambiri
Dziko la Peru likuyesetsa kwambiri kuchepetsa imfa za amayi pobereka. Pofuna kuthandiza anthu okhala kumidzi yakufupi ndi mapiri a Andes kuti asamaberekere kunyumba, zaka 10 zapitazi dziko la Peru lamanga nyumba zokwana 390 zoti amayi aziberekeramo ana. Mayi woyembekezera ndi banja lake amatha kukhala m’nyumba zimenezi zomwe zinamangidwa pafupi ndi zipatala, mpaka mwana kubadwa. Lipoti lina linanena kuti, amayi ambiri akumakonda kupita kunyumba zimenezi chifukwa amathandizidwa “pogwiritsa ntchito njira zamakono komanso zamakolo,” monga “kubereka choimirira,” zomwe “zimathandiza amayi kuti asamamve ululu kwambiri komanso kuti asamatenge nthawi yaitali kwambiri pobereka . . . Zimathandizanso kuti amayi athe kumuona mwana wawo akamabadwa.”
Ndege Zochedwa Nthawi Zonse
Lipoti la 2008 la bungwe loona za maulendo ku U.S.A. linati, pafupifupi ndege 30 mwa ndege 100 zilizonse zimachedwa ndi mphindi 15 kapena kuposerapo. Ndege zimene zimachedwa kwambiri ndi zochokera mumzinda wa Texas kupita ku California, ndipo akuti sizinayambe zafulumirapo.