Ana Ambiri Akumapanikizika
Ana Ambiri Akumapanikizika
▪ Mnyamata wina wa ku Spain wazaka 8, dzina lake Pablo, atafunsidwa ndi aphunzitsi ake za homuweki, anati: “Ndinalibe nthawi yokwanira, ndiponso ndatopa.” Mofanana ndi Pablo, ana ambiri amatopa kwambiri chifukwa amatha maola 12 kapena kuposa pamenepa akuphunzira ndiponso kuchita homuweki. N’chifukwa chiyani amatha nthawi yochuluka chonchi?
Makolo ena amalipirira ana awo sukulu yoti akaweruka azikhalabe kusukulu komweko mpaka iwo ataweruka kuntchito n’kukawatenga. Enanso amapanikiza ana awo ndi zinthu zambirimbiri kuti anawo azikhoza bwino m’kalasi n’cholinga choti adzapeze ntchito yapamwamba. Kuti zimenezi zitheke, makolo ambiri m’dziko la South Korea amatumiza ana awo kusukulu komwe amaphunzira zinthu zambirimbiri, kuyambira 7:30 m’mawa mpaka pakati pa usiku, kwa mlungu wonse wathunthu. Nyuzipepala ya New York Times inati: “Makolo amachita chilichonse chimene angathe kuti ana awo akhoze bwino n’kupita ku yunivesite zapamwamba.”
Magazini ina ya ku Spain inati: “Makolo ena amafunira ana awo zabwino, koma amawapanikiza pofuna kuti anawo azikhoza kwambiri.” Kuti akwanitse zimene makolo awo akufuna, anawo amapanikizika chifukwa sapuma. Mkulu wa bungwe lina la ku Spain loona za anthu opanikizika, dzina lake Antonio Cano, anati: “Taona kuti ana ambiri amapatsidwa zochita zochuluka.” Pulofesa wina wa zamaphunziro ananenanso kuti ana 40 pa 100 alionse a ku Spain, a zaka zosakwana 15, amapanikizika kwambiri. Ana otere, zinthu siziwayendera bwino ndipo amatha kudzipha. Mwachitsanzo, nyuzipepala ya New York Times inanena kuti ku South Korea, “kupatula pa ngozi za pamsewu, ana ambiri a zaka 10 mpaka 19 amafa chifukwa chodzipha.”
N’zoona kuti ana ayenera kulimbikira sukulu ndipo makolo afunika kuwathandiza mmene angathere chifukwa akadutsa msinkhu umenewu, adutsa basi. Koma mphunzitsi wina dzina lake Irene Arrimadas anati: “Ana ndi ana, sangakwanitse kuchita zinthu zambiri nthawi imodzi ngati munthu wamkulu.” N’chifukwa chake makolo achikondi amaonetsetsa kuti ana awo akupuma mokwanira komanso akuchita zinthu zina zosangalatsa pamodzi ndi makolo awo. Nthawi ina, mfumu yanzeru Solomo inasonyeza kuti pamafunika kuganiza bwino. Mfumuyi inalemba kuti: “Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti tho pali vuto ndi kungosautsa mtima.”—Mlaliki 4:6. *
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Kuti mumve zambiri zokhudza zinthu zimene zimapanikiza ana, werengani Galamukani! ya April 2009, yakuti “Mungatani Ngati Mumapanikizika ndi Sukulu Ndiponso Zinthu Zina?”