Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Akumwa Mankhwala Mwachisawawa

Anthu Akumwa Mankhwala Mwachisawawa

Anthu Akumwa Mankhwala Mwachisawawa

MAYI wina dzina lake Lena * anati: “Ndinayamba kumwa mankhwala akuchipatala mwachisawawa ndili ndi zaka 14. Ndinkafuna kukhala wochepa thupi kuti ndizioneka bwino. Choncho ndinapita kwa adokotala ndipo anandilembera mankhwala ochepetsa thupi. Koma mankhwalawa sanandithandize kwenikweni, anangochititsa kuti anyamata ayambe kundisirira. Kenako ndinayamba kumwa mankhwala ozunguza bongo ndiponso kuchita zachiwerewere. Nthawi zonse ndinkamwa mankhwala ambiri kuti ndiledzere.”

Mayi wina dzina lake Myra ankadwala mutu waching’alang’ala, choncho adokotala anamupatsa mankhwala oletsa ululu. Kenako mankhwalawa anamulowerera ndipo anayamba kuwamwa nthawi zonse ngakhale asakudwala mutu. Anayambanso kumwa mankhwala amene anthu ena a m’banja lake ankalandira kuchipatala.

Malipoti akusonyeza kuti achinyamata ambiri ngakhalenso achikulire akumwa mwachisawawa mankhwala olandira kuchipatala n’cholinga choti athetse nkhawa, achepe thupi, akhale ndi mphamvu, aledzere kapenanso kuti azimva bwino. Mankhwala ambiri amene anthu akumwa mwachisawawa ndi amene amawasunga m’nyumba zawo monga oletsa ululu, ogonetsa, opatsa mphamvu ndi othandiza wodwala kuti afatse. * Mankhwala enanso omwe anthu amamwa mwachisawawa ndi amene amagula kusitolo monga othandiza kugona, a chifuwa ndi chimfine, ndiponso oletsa kuyabwa.

Vutoli lili paliponse ndipo likuwonjezereka. Mwachitsanzo, m’mayiko ena mu Africa, ku Ulaya ndi ku South Asia, chiwerengero cha anthu amene akumwa mwachisawawa mankhwala olandira kuchipatala n’chachikulu kuposa cha anthu omwa mankhwala osokoneza bongo. Ndipo ku United States, chiwerengero cha anthu amene amamwa mankhwala otere chimaposa cha anthu onse amene amagwiritsa ntchito mankhwala onse osokoneza bongo, kupatulapo chamba. Nyuzipepala ina posachedwapa inayerekezera mmene achinyamata a zaka zapakati pa 12 ndi 17 amamwera mankhwala akuchipatala ndi mankhwala osokoneza bongo a kokeni, heroini ndi a methamphetamine. Nyuzipepalayi inati achinyamatawa “amamwa kwambiri mankhwala akuchipatala kuposa mankhwala osokoneza bongo atatu onsewa.” Popeza anthu ambiri akugwiritsa ntchito mankhwala oterewa, zachititsa kuti malonda a mankhwala achinyengo achuluke.

Kodi mungathandize bwanji banja lanu kuti lisamagwiritse ntchito molakwika mankhwala akuchipatala ndiponso osokoneza bongo? Nkhani zotsatira ziyankha funso limeneli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha mayina m’nkhanizi.

^ ndime 4 Mfundo zambiri m’nkhanizi zikukhudzanso mankhwala osokoneza bongo ndi kumwa mowa mwauchidakwa.

[Bokosi patsamba 3]

Buku lina la zamankhwala linati: “Munthu amene mankhwala anamulowerera amangomwa mankhwala ngakhale asakudwala, ndipo amapitirizabe kumwa ngakhale ngati mankhwalawo akumubweretsera vuto linalake.” (Physicians’ Desk Reference) Munthu amene ali ndi vutoli, sangakhale osamwa mankhwala.

Pali mankhwala ena amene amatha kumulowerera kwambiri munthu n’kufika poti amangodalira mankhwalawo, moti akapanda kumwa samva bwino. Zimenezi zimachitikira munthu aliyense amene akumwa mankhwala otere.

Thupi likazolowera mankhwala, munthu amawonjezera mlingo wamankhwalawo kuti azimva kuti wamwadi mankhwala.