Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Mukhale Wolemera?

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Mukhale Wolemera?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Mukhale Wolemera?

“Mulungu wandidalitsa, ndipo ndatsala pang’ono kulemera.”

“Ndikufuna kulemera ndipo Mulungu, ngakhalenso angelo onse, akufuna kuti ndilemere.”

“Mulungu amatipatsa mphamvu zopezera chuma.”

“Ndikulemera chifukwa cha Baibulo.”

ANTHU a zipembedzo zosiyanasiyana amene amaganiza kuti kulemera ndi umboni wakuti Mulungu akuwadalitsa, ndi amene amakonda kunena mawu ali pamwambawa. Iwo amanena kuti munthu akamachita zimene Mulungu amakondwera nazo, amapatsidwa chuma panopo komanso amadzadalitsidwa m’tsogolo. Anthu ambiri amakhulupirira zimenezi, ndipo mabuku amene amanena zoterezi amayenda malonda kwambiri. Koma kodi chiphunzitso chimenechi n’chogwirizana ndi zimene Baibulo limanena?

Mlengi wathu, yemwe Baibulo limati ndi “Mulungu wa chisangalalo,” amafuna kuti tizisangalala ndiponso kuti zinthu zizitiyendera bwino pamoyo wathu. (1 Timoteyo 1:11; Salmo 1:1-3) Iye amadalitsa anthu amene amamukonda. (Miyambo 10:22) Komabe, kodi masiku ano Mulungu amatidalitsa potipatsa chuma? Tingapeze yankho lolondola ngati titadziwa bwino nthawi imene tikukhala komanso cholinga cha Mulungu.

Kodi Ino Ndi Nthawi Yoti Mulemere?

Kalekale Yehova Mulungu ankadalitsa atumiki ake ena powapatsa chuma. Mwachitsanzo, Mulungu anapatsa chuma Yobu ndiponso Mfumu Solomo. (1 Mafumu 10:23; Yobu 42:12) Komabe panalinso anthu ena oopa Mulungu amene analibe chuma, monga Yohane Mbatizi ndiponso Yesu Khristu. (Maliko 1:6; Luka 9:58) Kodi pamenepa pali mfundo yotani? Monga mmene Baibulo limanenera, Mulungu amagwiritsa ntchito atumiki ake mogwirizana ndi cholinga chake panthawi imeneyo. (Mlaliki 3:1) Kodi mfundo imeneyi ikutikhudza bwanji ifeyo masiku ano?

Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti tikukhala m’nthawi ya “mapeto a dongosolo lino la zinthu” kapena kuti “m’masiku otsiriza.” Baibulo limati nthawi imeneyi kudzakhala nkhondo, matenda, njala, zivomerezi, ndiponso kusokonezeka kwa makhalidwe abwino. Zinthu zimenezi zakhala zikuchitika kwambiri kuyambira mu 1914. (Mateyo 24:3; 2 Timoteyo 3:1-5; Luka 21:10, 11; Chivumbulutso 6:3-8) Mwachidule, dzikoli lili ngati sitima imene yatsala pang’ono kumira. Choncho, kodi zingakhale zomveka kuti Mulungu adalitse atumiki ake onse panthawi imeneyi powapatsa chuma?

Yesu Khristu anayerekezera nthawi yathu ino ndi masiku a Nowa. Iye anati: “M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa, amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa mu chombo; ndipo sanazindikire kanthu mpaka chigumula chinafika ndi kuwaseseratu onsewo, zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu [Yesu].” (Mateyo 24:37-39) Yesu anayerekezeranso nthawi yathu ndi nthawi ya Loti. Anthu ambiri amene ankakhala ndi Loti mumzinda wa Sodomu ndi Gomora anali ‘kudya, kumwa, kugula, kugulitsa, kubzala, ndi kumanga.’ Yesu anatinso: “Koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu, kumwamba kunagwa moto ndi sulufule ngati mvula ndi kuwononga anthu onse. Zidzakhalanso momwemo pa tsikulo pamene Mwana wa munthu adzaonekera.”—Luka 17:28-30.

Sikuti kudya, kumwa, kukwatira, kugula ndi kugulitsa zinthu n’koipa ayi. Koma ngati timatengeka nazo kwambiri zinthu zimenezi n’kulephera kuzindikira kuti tikukhala m’masiku otsiriza, ndiye kuti pali vuto. Choncho, dzifunseni kuti, ‘Kodi tingati Mulungu akutikonda ngati atatipatsa zinthu zimene zingatisokoneze mwauzimu?’ * Mulungu ndi wachikondi ndipo sangachite zimenezo.—1 Timoteyo 6:17; 1 Yohane 4:8.

Ino Ndi Nthawi Yopulumutsa Anthu

Panopo tikukhala m’nthawi yovuta, ndipo anthu a Mulungu ali ndi ntchito yofunika kwambiri yoti achite. Yesu anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.” (Mateyo 24:14) Mboni za Yehova zimaona kuti n’kofunika kwambiri kutsatira mawu amenewa. Choncho, zimalimbikitsa anthu kuphunzira za Ufumu umenewu ndiponso zimene anthu angachite kuti Mulungu adzawapatse moyo wosatha.—Yohane 17:3.

Koma sikuti Mulungu amafuna kuti atumiki ake okhulupirika akhale osauka. Iye amafuna kuti iwo azikhala ndi zinthu zofunika pamoyo n’kumakhutira nazo kuti azitha kum’tumikira ndi mtima wonse. (Mateyo 6:33) Ndipo iye amaonetsetsa kuti atumiki akewo ali ndi zonse zofunika pamoyo. Lemba la Aheberi 13:5, 6 limati: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo panthawiyo. Pakuti [Mulungu] anati: ‘Mulimonse sindidzakusiyani, ngakhale kukutayani konse.’”

Mulungu adzakwaniritsa malonjezo amenewa mochititsa chidwi kwambiri pamene adzapulumutsa “khamu lalikulu” la olambira ake oona pamapeto a dongosolo la zinthu lilipoli n’kuwalowetsa m’dziko latsopano lamtendere ndiponso laulemerero. (Chivumbulutso 7:9, 14) Yesu anati: “Ine ndabwera kuti iwo [otsatira ake okhulupirika] akhale ndi moyo, inde kuti akhale nawo wochuluka.” (Yohane 10:10) ‘Moyo wochuluka’ umenewu sutanthauza kukhala olemera panopa, koma umatanthauza moyo wosatha m’Paradaiso mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.—Luka 23:43.

Anthu asakunamizeni kuti Mulungu amafuna kuti mukhale olemera, chifukwa chiphunzitso chimenechi chingakusokonezeni. Muyenera kutsatira mawu a Yesu omwe ndi achikondi komanso ofunika akuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa ngati msampha.”—Luka 21:34, 35.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Monga mmene zinalili mu nthawi ya atumwi, Akhristu enanso okhulupirika masiku ano ndi olemera. Komabe, Mulungu amawachenjeza Akhristu amenewa kuti asamadalire kwambiri chuma chawocho kapena kulola kuti chiwasokoneze. (Miyambo 11:28; Maliko 10:25; Chivumbulutso 3:17) Anthu onse amafunika kuika maganizo awo onse pakuchita chifuniro cha Mulungu, kaya akhale olemera kapena osauka.—Luka 12:31.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi nthawi ino ndi yoti tichite chiyani?—Mateyo 24:14.

▪ Kodi Yesu anayerekezera nthawi ino ndi nthawi ya anthu ati a m’Baibulo?—Mateyo 24:37-39; Luka 17:28-30.

▪ Kodi tingapewe chiyani kuti tidzalandire moyo wosatha?—Luka 21:34.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

Chiphunzitso chakuti kulemera ndi umboni wakuti Mulungu watidalitsa, chimasokoneza anthu