Kodi Mungadziwe Bwanji Kuti Muli ndi Matenda a Chithokomiro?
Kodi Mungadziwe Bwanji Kuti Muli ndi Matenda a Chithokomiro?
YOLEMBEDWA KU BRAZIL
SARA anali ndi pakati pa miyezi itatu ndipo anadandaula kwambiri atapita padera. Patapita chaka chimodzi anapitanso padera. Madokotala anamuyeza kangapo koma sanapeze vuto lililonse. Patapita zaka zina zingapo, Sara anayamba kunenepa, ngakhale kuti ankapewa kudya zakudya zonenepetsa komanso ankachita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse. Miyendo yake inkamupweteka komanso ankadwaladwala chimfine. Kenako madokotala atapima magazi ake komanso atamuunika ndi makina, anapeza kuti anali ndi matenda a chithokomiro a Hashimoto. N’kutheka kuti matendawa ndi amene ankachititsa kuti azipita padera. *
Sara sankada nkhawa kwambiri ndi matendawa,
monga mmene amachitira anthu ambiri. Koma atayamba kudwala kwambiri, anadziwa kuti matenda a chithokomiro ndi oopsa.Kodi Chithokomiro N’chiyani?
Chithokomiro ndi kachiwalo kakang’ono kooneka ngati gulugufe komwe kamakhala pakhosi, pansi pa nkhwiko. Kachiwaloka kali ndi mbali ziwiri zomwe zinakhala mozungulira kholingo ndipo sikafika magalamu 30 kulemera kwake. Chithokomiro ndi chimodzi mwa ziwalo zimene zimatulutsa timadzi timene timapita m’magazi tothandiza kuti thupi lizigwira bwino ntchito.
Chithokomiro chili ndi timatumba ting’onoting’ono tambiri m’mene mumakhala timadzi timeneti. M’timadziti mumakhala ayodini wambiri. Pafupifupi 80 peresenti ya ayodini wa m’thupi mwathu amakhala mu chithokomiro. Ngati munthu amadya zakudya zopanda ayodini wokwanira amatupa chithokomiro. Ana aang’ono akamasowa ayodini m’thupi, amalephera kukula ndiponso amakhala ndi nzeru zochepa.
Ntchito ya Chithokomiro
Timadzi ta m’chithokomiro tilipo ta mitundu itatu, ndipo mayina ake ndi T3, RT3, ndi T4. * Mitundu iwiriyi, ya T3 ndi RT3, imapangidwa kuchokera ku T4 ndipo zimenezi zimachitikira kunja kwa chithokomiro. Choncho thupi likafuna timadzi tambiri, chithokomiro chimatulutsa timadzi ta mtundu wa T4 kupita m’magazi, ndipo kenako timadzi ta T4 ndi mitundu inayo timatumizidwa m’thupi lonse.
Timadzi ta mu chithokomiro timathandiza thupi kupanga maselo atsopano komanso timathandiza munthu kukhala ndi mphamvu zokwanira. Timadziti timathandizanso kuti mtima uzigunda moyenerera, maselo azichuluka, komanso kubwezeretsa maselo amene awonongeka. Timathandizanso kuti thupi lathu lizitentha moyenera.
Timadzi timene chithokomiro chimatulutsa timagwiranso ntchito zina zofunika kwambiri. Mwachitsanzo, timathandiza kuti chiwindi chizichotsa mafuta osafunikira m’magazi. Kenako mafutawo amapita mu ndulu ndipo akachoka mmenemo amatuluka ndi chimbudzi. Ngati chithokomiro sichikutulutsa timadzi tokwanira, thupi limakhala ndi mafuta ambiri osafunika ndipo mafuta ofunika amakhala ochepa.
Timadziti timathandiza matumbo kutulutsa madzi enaake amene amachititsa kuti chakudya chizigayika komanso kuti matumbowo azitha kufinya chakudyacho pochigaya. Choncho, timadziti tikachuluka timachititsa munthu kumangopitapita ku chimbudzi, koma timadziti tikachepa, munthu amadzimbidwa.
N’chiyani Chimachititsa Chithokomiro Kuti Chizigwira Bwino Ntchito?
Pali mbali ina ya ubongo imene imathandiza kuti chithokomiro chizigwira bwino ntchito. Thupi likafuna timadzi ta m’chithokomiro, mbali ya ubongo imeneyi imatumiza uthenga ku kachiwalo kenakake kamene kamakhala m’munsi mwa ubongo. Kenako kachiwaloko kamatulutsa madzi otchedwa TSH amene amadzera m’magazi kukafika ku chithokomiro ndipo tsopano chithokomirocho chimayamba kutulutsa timadzi take.
Choncho, kuti adokotala adziwe mmene chithokomiro chikugwirira ntchito komanso thanzi la munthu, amayeza magazi kuti adziwe kuchuluka kwa timadzi ta TSH komanso timadzi ta m’chithokomiro. Kuchita zimenezi n’kofunika kuti munthu atetezedwe ku matenda a chithokomiro.
Matenda a Chithokomiro
Munthu angadwale matenda a chithokomiro ngati amadya chakudya chopanda ayodini wokwanira, amapanikizika kwambiri, amakhala ndi * Nthawi zina chizindikiro cha matendawa ndi kutupa chithokomiro. Chithokomiro chonsecho chikhoza kutupa kapena chingakhale ndi timibulu. Ngakhale kuti nthawi zambiri kutupa kwa chithokomiroku si koopsa, munthu afunikirabe kulandira thandizo la mankhwala chifukwa vutoli likhoza kuyambitsa matenda a khansa. *
nkhawa kwambiri, makolo ake ali ndi matendawa, kapena ngati ali ndi matenda enaake amene amachititsa kuti maselo a m’thupi azimenyana, kapenanso matenda amene amayamba chifukwa cha mankhwala a matenda ena.Chithokomiro chimene chili ndi matenda chimatulutsa timadzi tambiri zedi kapena tochepa zedi. Matenda a chithokomiro angayambe pang’onopang’ono popanda munthu kudziwa, choncho munthu amatha kukhala ndi matendawa kwa zaka zambiri asanawatulukire. Mofanana ndi matenda ambiri, zimakhala bwino ngati matendawa atulukiridwa mwamsanga.
Pali mitundu iwiri ya matenda a chithokomiro ofala kwambiri, amodzi anatulukiridwa ndi Hashimoto ndipo enawo anatulukiridwa ndi Graves. Matenda onsewa amachititsa kuti maselo a thupi
aziukirana okhaokha. Matenda a Hashimoto nthawi zambiri amagwira akazi kuwirikiza ka 6 kuposa amuna, ndipo amachititsa kuti chithokomiro chizitulutsa timadzi tochepa. Matenda a Graves amagwira kwambiri akazi kuwirikiza ka 8 kuposa amuna, ndipo amachititsa chithokomiro kutulutsa timadzi tambiri zedi.Madokotala ali ndi maganizo osiyanasiyana pankhani yakuti anthu ayenera kuyezedwa kangati kuti awone ngati ali ndi matenda a chithokomiro, komabe ambiri amaona kuti kuyeza ana pafupipafupi n’kofunika. (Onani bokosi lakuti “Kuyeza Ana Obadwa Kumene N’kofunika.”) Munthu akam’peza kuti chithokomiro chake sichikutulutsa timadzi tambiri, amamuyeza kuti adziwe chimene chikuchititsa kuti chithokomirocho chisamatulutse timadzi tambiri. Koma akamuyeza n’kupeza kuti chithokomiro chake chikutulutsa timadzi tambiri zedi, amachiunika ndi makina malinga ngati munthuyo alibe pakati kapena sakuyamwitsa. Ngati chithokomiro chake chili ndi zotupa, amayeza zotupazo kuti awone ngati ali ndi khansa.
Kodi Mungafunike Thandizo Lotani?
Munthu amene chithokomiro chake chikutulutsa timadzi tambiri zedi, mtima wake umathamanga, amanjenjemera ndiponso amakhala ndi nkhawa kwambiri. Choncho akamalandira mankhwala mavuto amenewa amachepa. Nthawi zina madokotala amapha maselo ena a chithokomiro n’cholinga chakuti chisamatulutse timadzi tambiri. Nthawi zinanso madokotala amachita opaleshoni n’kuchotsa chithokomirocho.
Anthu amene chithokomiro chawo chimatulutsa timadzi tochepa, kapena amene chithokomiro chawo chinachotsedwa, amamwa mankhwala a mtundu wa T4 tsiku lililonse. Madokotala amafunika kumamuyeza munthuyo pafupipafupi kuti adziwe kuchuluka kwa mankhwala amene angamamwe. Munthu amene ali ndi khansa ya chithokomiro, angathandizidwe m’njira zosiyanasiyana monga kumwa mankhwala, kuchita opaleshoni, kuwotcha ndi mankhwala pamene pali vutopo ndi njira zina zambiri.
Sara akupezako bwino chifukwa amamwa mankhwala a T4, komanso amadya chakudya chopatsa thanzi. Anthu amene akudwala matenda a chithokomiro, monga Sara, azindikira kuti chithokomiro n’kachiwalo kakang’ono koma kofunika kwambiri. Choncho, muziyesetsa kudya chakudya chopatsa thanzi chokhala ndi ayodini wambiri, muzipewa kuda nkhawa, komanso muzisamalira thanzi lanu nthawi zonse.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Ngakhale kuti matendawa amatha kuchititsa munthu kuti apite padera, amayi ambiri amene amadwala matendawa amatha kubereka ana athanzi. Komabe, ndi bwino kuti amayi a pakati omwe ali ndi matendawa azilandira mankhwala omwe angawathandize kubereka ana athanzi.
^ ndime 9 T3 imaimira triiodothyronine ndipo T4 imaimira thyroxine. Nambala ya 3 ndiponso 4 ikuimira nambala ya ma atomu a ayodini amene amapezeka mu timadzito. Chithokomiro chimatulutsanso timadzi totchedwa calcitonin, tomwe timathandiza magazi kukhala ndi kasiyamu wokwanira.
^ ndime 17 Galamukani! sisankhira anthu mankhwala. Ngati mukuganiza kuti muli ndi vuto la chithokomiro, pitani kuchipatala kuti mukaonane ndi dokotala wodziwa za matendawa.
^ ndime 17 Anthu amene angayambe kudwala khansa ya m’chithokomiro mosavuta ndi amene anaunikidwapo ndi makina pakhosi kapena m’mutu kuchipatala kapenanso amene ali ndi wachibale yemwe anadwalapo matendawa.
[Mawu Otsindika patsamba 27]
Timadzi ta mu chithokomiro timathandiza thupi kupanga maselo atsopano komanso timathandiza munthu kukhala ndi mphamvu zokwanira
[Mawu Otsindika patsamba 29]
Matenda a chithokomiro angayambe pang’onopang’ono popanda munthu kudziwa, choncho munthu amatha kukhala ndi matendawa kwa zaka zambiri asanawatulukire
[Bokosi/Chithunzi patsamba 28]
ZIZINDIKIRO ZA MATENDA A CHITHOKOMIRO
Chithokomiro chikamatulutsa timadzi tambiri zedi, mumaona zizindikiro monga kukhumudwa kwambiri, kuwonda kwambiri, kuthamanga kwa mtima, kupitapita kuchimbudzi, kusamba modumphadumpha, ukali, nkhawa, kusangalala kapena kukwiya mosayembekezereka, kutupa maso, kufooka, kusowa tulo ndiponso kupepeluka tsitsi. *
Chithokomiro chikamatulutsa timadzi tochepa zedi, mumaona zizindikiro monga ulesi, kunenepa kwambiri, kuthothoka tsitsi, kudzimbidwa, kumva kuzizira kwambiri, kusamba modumphadumpha, kuvutika maganizo, kusintha mawu (kusasa mawu kapena kulephera kulankhula mokuwa), kuiwalaiwala ndiponso kutopa.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 36 Matenda ena angachititsenso zina mwa zizindikiro zimenezi, choncho ndi bwino kupita kuchipatala mukaona zizindikirozi.
[Bokosi patsamba 28]
KUYEZA ANA OBADWA KUMENE N’KOFUNIKA
Kuyeza magazi a mwana amene wabadwa kumene kungathandize kudziwa ngati ali ndi vuto la chithokomiro kapena ayi. Magaziwo akasonyeza kuti chithokomiro cha mwanayo chili ndi matendawa, madokotala amatha kumuthandiza. Vutoli limachititsa kuti mwana alephere kukula ndipo amakhala ndi nzeru zochepa. Choncho, nthawi zambiri ana akangobadwa amawayeza.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 29]
KODI MUMADYA ZAKUDYA ZOPATSA THANZI?
Kudya zakudya zopatsa thanzi kungakuthandizeni kupewa matenda a chithokomiro. Zakudya zokhala ndi ayodini n’zofunika kwambiri kuti chithokomiro chizigwira bwino ntchito. Kodi chakudya chimene mumadya chimakhala ndi ayodini wokwanira? Nsomba ndi zakudya zina zochokera m’nyanja zamchere n’zofunika chifukwa zimakhala ndi ayodini wambiri. Ayodini amene amapezeka mu ndiwo zamasamba komanso nyama, amakhala wochepa kapena wambiri mogwirizana ndi nthaka ya kumaloko. Kuti zakudya zizikhala ndi ayodini wokwanira, mayiko ena amaika lamulo lakuti mu mchere muziikidwa ayodini.
Pamafunikanso kudya zakudya zokhala ndi selenium kuti chithokomiro chizigwira bwino ntchito. Selenium amathandizanso kusintha timadzi ta T4 kuti tikhale ta T3. Selenium amene amapezeka mu ndiwo zamasamba, nyama komanso mkaka, amakhala wochepa kapena wambiri mogwirizana ndi nthaka ya kumaloko. Zakudya zochokera m’nyanja zamchere zimakhala ndi selenium wambiri. Komabe, ngati mukuganiza kuti muli ndi matenda a chithokomiro, ndi bwino kupita kuchipatala, m’malo mopeza nokha mankhwala.
[Chithunzi patsamba 28]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Paipi yodutsa mpweya
Kholingo
Chithokomiro
Paipi yodutsa mpweya