“Kodi Mungatani Kuti Mudzapulumuke Mapeto a Dzikoli?”
“Kodi Mungatani Kuti Mudzapulumuke Mapeto a Dzikoli?”
▪ Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamanena za mapeto a dzikoli kapena dongosolo lino la zinthu? Kodi limatanthauza nkhondo yoopsa ya dziko lonse lapansi, imene idzawononge anthu onse? Kapena kodi limatanthauza tsoka lachilengedwe monga kugwa kwa mwala wochokera kumwamba? N’zosangalatsa kuti Baibulo limanena kuti “khamu lalikulu” la anthu lidzapulumuka mapeto a dzikoli. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14) Kodi anthu amenewa ndani? Kodi inuyo mudzakhala m’gulu la anthu opulumukawo?
Mafunso amenewa adzayankhidwa m’nkhani yakuti “Kodi Mungatani Kuti Mudzapulumuke Mapeto a Dzikoli?” Nkhaniyi idzakambidwa pamsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova wakuti “KHALANI MASO.” Msonkhanowu, womwe udzayambe mwezi wa May ku United States, udzachitika padziko lonse lapansi. Tikukuitanani kuti mudzakhale nawo pa msonkhano umene udzachitikire pafupi ndi kwanu. Ngati mukufuna kudziwa zambiri, funsani Mboni za Yehova za m’dera lanu kapena lemberani kalata ofalitsa magaziniyi. Magazini ya Nsanja ya Olonda ya March 1, 2009, ili ndi malo amene kudzachitikire misonkhanoyi ku Malawi ndi ku Mozambique.