Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
Zinachitikira Kuti?
1. Kodi thanthwe limene Mose anamenya kuti atulutsire Aisiraeli madzi linali kuti?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Numeri 20:1-8.
Lembani mzere wozungulira yankho lanu pamapupo.
Kadesi
Refidimu
Phiri la Sinai (Horebe)
▪ Kodi Mose ndi Aroni analakwitsa chiyani, ndipo analandira chilango chotani?
․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Numeri 20:9-13; Salmo 106:32, 33.
KAMBIRANANI:
Kodi mukuganiza kuti Mose anakwiyira Aisiraeli chifukwa chiyani? N’chifukwa chiyani muyenera kupewa kupsa mtima msanga?
Kuchokera M’magazini Ino
Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.
TSAMBA 7 Kodi mayanjano oipa amawononga chiyani? 1 Akorinto 15:․․․
TSAMBA 8 Kodi osangalala ndi amene amazindikira chiyani? Mateyo 5:․․․
TSAMBA 13 Kodi moyo wathu uyenera kukhala wosakonda chiyani? Aheberi 13:․․․
TSAMBA 18 Kodi chikondi sichichita chiyani? 1 Akorinto 13:․․․
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
Kodi Mumadziwa Chiyani za Aneneri?
Werengani Amosi 7:10-17, ndiyeno yankhani mafunso otsatirawa.
2. ․․․․․
Kodi wansembe Amaziya anadzudzula Amosi chifukwa chiyani?
3. ․․․․․
Kodi ndi makhalidwe awiri ati amene Amosi anasonyeza poyankha mawu achipongwe a Amaziya?
KAMBIRANANI:
Kodi mungaleke kunena za Yehova chifukwa chakuti ena akukunyozani? N’chifukwa chiyani mwayankha choncho?
▪ Mayankho ali pa tsamba 11
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
1. Kadesi.
▪ Mose analankhula mokalipa, ndipo iye ndi Aroni sanayeretse dzina la Yehova, choncho sanaloledwe kulowa Dziko Lolonjezedwa.
2. Anachitira mfumu chiwembu.
3. Kudzichepetsa ndiponso kulimba mtima.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Map: Based on maps copyrighted by Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel