Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugwiritsa Ntchito Mankhwala Koyenera ndi Kosayenera

Kugwiritsa Ntchito Mankhwala Koyenera ndi Kosayenera

Kugwiritsa Ntchito Mankhwala Koyenera ndi Kosayenera

MTSIKANA wina dzina lake Angie, anamva makolo ake akunena kuti mankhwala amene mchimwene wake amamwa akumuchititsa kuti asamafune kudya. Popeza kuti Angie ankafuna kuchepa thupi, anayamba kuba mankhwala a mchimwene wakeyo. Koma kuti makolo ake asadziwe, iye anapempha mnzake amene amamwanso mankhwala ngati omwewo kuti azimugawira. *

N’chifukwa chiyani anthu ambiri sagwiritsa ntchito moyenera mankhwala akuchipatala? Chifukwa chimodzi n’chakuti mankhwalawa sasowa, amatha kupezeka ngakhale m’nyumba zawo. Chifukwa chachiwiri n’chakuti achinyamata ambiri amaganiza molakwa kuti akamamwa mankhwala akuchipatala asakudwala, sakuphwanya lamulo lililonse. Ndipo chifukwa chachitatu n’chakuti, mankhwala akuchipatala amaoneka kuti si oopsa kwambiri ngati mankhwala ozunguza bongo. Achinyamata ena amaganiza kuti, ‘Ngati mankhwalawa amamwa ndi ana omwe, ndiye kuti si oopsa.’

Komabe mankhwala akuchipatala akagwiritsidwa ntchito moyenera, amathandiza munthu kukhala ndi thanzi ndi moyo wabwino ndiponso angapulumutse moyo. Koma akagwiritsidwa ntchito mosayenera, amakhala oopsa ngati mankhwala osokoneza bongo. Mwachitsanzo, ngati munthu amagwiritsa ntchito mosayenera mankhwala opatsa mphamvu, angayambe kudwala matenda a mtima kapena kumangonjenjemera. Mankhwala ena angapangitse munthu kuvutika kupuma mwinanso mpaka kufa kumene. Mankhwala angathenso kuyambitsa mavuto ngati munthu atawaphatikiza ndi mankhwala ena kapena mowa. Nyuzipepala ina ya ku Arizona inanena kuti kumayambiriro kwa chaka cha 2008, katswiri wina wotchuka wochita masewera anafa “atamwa nthawi imodzi mankhwala ogonetsa, ochepetsa ululu ndiponso mitundu 6 ya mankhwala ochititsa munthu kufatsa.”—Arizona Republic.

Vuto linanso ndi lakuti mungafike polephera kusiya kumwa mankhwalawa. Mankhwala ena munthu akawamwa mopitirira muyeso kapena pachifukwa cholakwika, ubongo wake umafika powazolowera ndipo iye amangofunabe kuwamwa, ngati mmene zimachitikira ndi mankhwala ozunguza bongo. M’malo mothandiza munthu kuti aiwale mavuto, mankhwalawa amangochititsa kuti mavutowo akule kwambiri. Nthawi zina amachititsa kuti munthu akhale ndi nkhawa kwambiri, azivutika maganizo, azidwaladwala ndiponso asamaganize bwino. N’chifukwa chake anthu amene amagwiritsa ntchito mankhwalawa amakhala ndi mavuto kunyumba, kusukulu kapena kuntchito. Koma kodi tingadziwe bwanji kuti tikugwiritsa ntchito moyenera mankhwala akuchipatala kapena ayi?

Kugwiritsa Ntchito Koyenera ndi Kosayenera

Mukamamwa mankhwala motsatira malangizo ochokera kwa dokotala yemwe akudziwa bwino matenda anu, ndiye kuti mukuwagwiritsa ntchito moyenera. Muyenera kumwa mankhwala okwanira panthawi yoyenera ndiponso mogwirizana ndi matenda amene mukudwala. Komabe, ngakhale mutamamwa mankhwalawo moyenera, nthawi zina angabweretsebe mavuto. Zimenezi zikakuchitikirani, muzipita kuchipatala mwamsanga. Kuchipatalako angakusinthireni mankhwala kapena kukuuzani kuti musiye kuwamwa. N’chimodzimodzinso ndi mankhwala ogula kusitolo. Mankhwala amenewanso muziwagwiritsa ntchito ngati pali zifukwa zomveka ndipo muzitsatira mosamala malangizo ake.

Kumwa mankhwala pazifukwa zolakwika, kumwa mankhwala mosatsatira malangizo kapena kumwa mankhwala a munthu wina, n’koopsa. Mwachitsanzo, mapilisi ena amafunika kuti munthu angowameza athunthu n’cholinga choti azisungunuka pang’onopang’ono m’thupi. Koma anthu ena amakonda kutafuna mapilisi, kumwa opera, kupera n’kuwasuta, kapena kuwasungunula m’madzi n’kudzibaya. Zimenezi zingachititse kuti munthu amve bwino, koma vuto ndi lakuti angawazolowere mpaka kulephera kuwasiya, ndiponso angathe kufa nawo.

Ngati munthu akumwa mankhwala akuchipatala moyenera koma waona kuti wayamba kuwazolowera kwambiri, ayenera kupita kuchipatala mwamsanga. Adokotala angadziwe mmene angamuthandizire popanda kunyalanyaza matenda ake oyamba.

Vuto logwiritsa ntchito mankhwala mosayenera ndi lofala kwambiri masiku ano. Mabanja ambiri ali pamavuto ngakhale kuti m’banja ndi mmene munthu amayembekezera kukondedwa ndi kutetezedwa. Makhalidwe abwino ndiponso auzimu akutha chifukwa chakuti anthu alibe ntchito ndi moyo. (2 Timoteyo 3:1-5) Komanso anthu alibe chiyembekezo chilichonse, moti ambiri amaona kuti kutsogoloku kulibe chabwino chilichonse. N’chifukwa chake saganizira za mawa ndipo amachita chilichonse, ngakhale choipa, pofuna kusangalala. Baibulo limati: “Popanda chivumbulutso anthu amasauka.”—Miyambo 29:18.

Ngati ndinu kholo, n’zosakayikitsa kuti mumafuna kuthandiza banja lanu kuti likhale ndi khalidwe labwino komanso kuti likhale paubwenzi wabwino ndi Mulungu. Koma kodi mungachite bwanji zimenezo? Ndipo kodi mungapeze kuti malangizo abwino ndiponso odalirika onena za tsogolo labwino? Mafunso amenewa ayankhidwa mu nkhani zotsatirazi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Zachokera pa Intaneti pa adiresi ya TeensHealth.

[Bokosi patsamba 4]

ANTHU AMACHITA CHILICHONSE KUTI ASANGALALE

Anthu ena amayesetsa kuchita chilichonse kuti asangalale. Amachita zinthu zina zoopsa monga kufwenkha mankhwala ochapira zinthu, mankhwala ochotsera zopaka m’zala, polishi wa mipando, mafuta a galimoto, zomatira, mafuta a nyale, penti ndi zina zotero. Zinthu zimene anthu amafwenkha zimapita nthawi yomweyo ku ubongo.

Khalidwe lina loipa ndi kumwa mosayenera mankhwala ogula kusitolo, monga oledzeretsa kapena ogonetsa. Munthu akawamwa mopitirira muyeso, mankhwalawa amam’chititsa kuti asamaone ndiponso kumva bwino. Amachititsanso kuti munthu asokonezeke maganizo, aziona zilubwelubwe, azimva dzanzi, ndiponso kuti azimva kupweteka m’mimba.

[Bokosi patsamba 5]

“NJIRA ZOPEZERA MANKHWALA”

“Anthu amene mankhwala anawalowerera komanso amene amagwiritsa ntchito mankhwala mwachisawawa, ali ndi njira zosiyanasiyana zopezera mankhwala. Iwo amatha kuimbira foni dokotala mwadzidzidzi kapena kupita kukaonana naye atatsala pang’ono kuweruka. Nthawi zinanso amakana kuyezedwa, kuonana ndi madokotala ena, kapena amanama kuti ataya kapepala ka malangizo a kamwedwe ka mankhwala. Komanso amatha kusintha zimene zalembedwa pakapepalako, kuzengereza kupereka kwa dokotala zikalata za kuchipatala kapena mayina a madokotala ena amene anawathandizapo. Anthuwa amakonda kusintha madokotala n’cholinga choti apatsidwe mankhwala ambiri.”

Mitundu itatu ya mankhwala amene anthu nthawi zambiri amawagwiritsa ntchito mwachisawawa ndi iyi:

▪ Mankhwala ochepetsa ululu

▪ Mankhwala ogonetsa

▪ Mankhwala opatsa munthu mphamvu, omwe kwenikweni amaperekedwa kwa anthu amene zimawavuta kumvetsera, kugona, kapena kwa anthu onenepa kwambiri *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 24 Mfundozi zachokera ku bungwe la NIDA (National Institute on Drug Abuse)

[Bokosi patsamba 6]

MALANGIZO A MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MANKHWALA AKUCHIPATALA

1. Muzitsatira bwinobwino malangizo a kamwedwe ka mankhwala.

2. Musamasinthe kamwedwe ka mankhwala popanda kufunsa dokotala.

3. Musamasiye kumwa mankhwala ngati dokotala sanakuuzeni kuti mutero.

4. Musamabenthule kapena kupera mapilisi ngati dokotala sanakuuzeni kuchita zimenezo.

5. Muzidziwiratu zimene zingachitike ngati mukuyendetsa galimoto kapena kuchita zinthu zina mutamwa mankhwalawo.

6. Muzidziwiratu zimene zingachitike ngati mutasakaniza mankhwalawo ndi mowa kapena mankhwala ena.

7. Dziwitsani dokotala ngati poyamba munali ndi vuto lomwa mankhwala ndiponso mowa molakwika.

8. Musamamwe mankhwala a anthu ena ndiponso musamapatse anthu ena mankhwala anu. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 36 Malangizowa achokera ku bungwe la ku America loona za zakudya ndi mankhwala.