Ndinathawa Nkhondo Ndipo Ndinapeza Moyo
Ndinathawa Nkhondo Ndipo Ndinapeza Moyo
Yosimbidwa ndi Sam Tan
Ndinathawa kwathu ku Cambodia pamodzi ndi anthu okwana 2,000, ndipo kenako tinafika pamtsinje umene uli m’malire a dziko la Cambodia ndi Thailand. Ine ndi anthu ena a m’banja lathu, tinayesetsa kukwera nawo maboti amene ankaolotsa anthu othawa ku Cambodia. Boti lomaliza litangonyamuka, gulu la asilikali oukira boma la Khmer Rouge linafika n’kuyamba kuwombera.
MWAMWAYI tonse tinakafika bwinobwino ku Thailand. Aliyense anali wosangalala kupatulapo banja lathu chifukwa miyezi ingapo zimenezi zisanachitike, bambo ndi amalume anga anagwidwa, moti mayi ankangolira. Koma ndisanafotokoze zambiri, dikirani ndikuuzeni kaye za moyo wanga.
Ndili Mwana, Ndinali M’buda
Ndinabadwira ku Cambodia mu 1960, ndipo m’banja mwathu tinalipo ana atatu. Ndili ndi zaka 9, ineyo ndi makolo anga tinagwirizana kuti ndizikatumikira m’kachisi wachibuda. Ndipo zimenezi sizinali zachilendo chifukwa mabanja ambiri ankatumizako ana awo. Wansembe aliyense amayamba ntchito 6 koloko m’mawa, ndipo amachoka pakachisi n’kumakapempha chakudya khomo ndi khomo. Ineyo zinkandivuta kuchita zimenezi chifukwa anthu ambiri amene tinkawapempha anali osauka. Tikatero, ife amene tinali achinyamata tinkaphikira chakudya ansembe achikulire ndipo tinkadya iwo akamaliza.
Madzulo alionse 6 koloko, ansembe onse achikulire ankapempherera pamodzi. Ndipo ankapemphera m’chinenero chimene anthu ambiri, kapena kuti ena onse, sankamva. Patatha zaka ziwiri ndinakhala wansembe wamng’ono ndipo ndinkachita nawo zinthu zina zimene ansembe aakulu ankachita. Ndinkaloledwanso kupemphera nawo limodzi. Panthawi yonseyi ndinkaganiza kuti padziko lonse panali chipembedzo chimodzi chokha cha Chibuda.
Ndinathawa ku Cambodia
Kukhala pakachisi sikunkandisangalatsa ndipo ndili ndi zaka 14, ndinabwerera kunyumba. Patangopita nthawi yochepa, dziko la Cambodia linayamba kulamulidwa ndi mtsogoleri wa chipani cha Khmer Rouge, dzina lake Pol Pot. Chipanichi chinalamulira kuyambira m’chaka cha 1975 mpaka 1979, ndipo chinathamangitsa anthu m’tawuni kuti azikakhala kumidzi n’cholinga choti dzikoli likhale lachikomyunizimu. Ndipo banja lathunso linasamutsidwa. Kenako anthu a chipani cha Khmer Rouge anagwira bambo ndi amalume anga, ndipo kuyambira nthawi imeneyi sitinawaonenso. Nthawi imene chipani cha Khmer Rouge chinkalamulira, anthu a ku Cambodia pafupifupi 1.7 miliyoni anaphedwa ndipo ena anafa chifukwa chogwira ntchito yakalavula gaga, kudwala kapena chifukwa cha njala.
Zimenezi zinachititsa kuti anthu 2,000 tithawe monga mmene ndinanenera kumayambiriro kwa nkhani ino. Tinayenda ulendo woopsa wa masiku atatu, kudutsa m’mapiri kuti tikafike kumalire a dziko la Cambodia ndi Thailand. Tonse, kuphatikizapo mwana wamwamuna amene anabadwira m’njira, tinakafika bwinobwino. Ambirife tinathawa ndi ndalama koma tinangozitaya chifukwa panthawiyi ndalama za ku Cambodia zinali zopanda mphamvu ku Thailand.
Mmene Tinkakhalira ku Thailand
Banja lathu linayamba kukhala ndi achibale athu ku Thailand ndipo ineyo ndinayamba ntchito
yopha nsomba. Nthawi zambiri bwato lathu linkadutsa malire n’kufika ku Cambodia komwe kunali nsomba zambiri komanso kunkapezeka maboti a anthu olondera a chipani cha Khmer Rouge. Akangokugwira ankakulanda bwato n’kukupha. Kawiri konse akanatigwira, moti anthu ena anagwidwa, kuphatikizapo munthu amene ndinayandikana naye nyumba. Munthuyu atamugwira anamudula mutu. Imfa yake inandikhudza kwambiri, komabe ndinapitiriza kupha nsomba ku Cambodia chifukwa ndikanapanda kutero, ndiye kuti anthu a m’banja mwathu akanafa ndi njala.Chifukwa choti ndinkaopa kuti akandipha anthu a m’banja mwathu adzavutika, ndinaganiza zopita ku malo osungirako anthu othawa nkhondo ku Thailand. Ndipo ndinapempha abale anga kuti ndipite dziko lina n’cholinga choti ndikapeze ntchito n’kumawatumizira ndalama. Nditawauza zimenezi iwo anandikaniza, komabe ndinaumirira.
Kumeneko kunkabwera anthu olankhula Chingelezi ndipo ankati ndi Akhristu. Nditacheza nawo ndinazindikira kuti palinso zipembedzo zina osati Chibuda chokha. Ine ndi mnzanga wina amene ndinam’peza komweko, dzina lake Teng Hann, tinayamba kupita kutchalitchi cha Akhristuwo ndipo anatisonyeza Baibulo ndiponso ankatipatsa chakudya. Ndinakhala kumeneko chaka chimodzi kenako ndinapempha kuti ndisamukire ku New Zealand.
Ndinasamukira ku New Zealand
Mu May 1979, anandisamutsira kumalo osungirako anthu othawa kwawo ku Auckland. Munthu wina anandipezera ntchito kufakitale ina m’tawuni ya Wellington. Nditapita kumeneko ndinagwira ntchito mwakhama ndipo ndinkatumiza ndalama kunyumba monga mmene ndinalonjezera.
Chifukwa choti ndinkafuna kulowa Chikhristu, ndinayamba kupita ku matchalitchi awiri a Chipulotesitanti. Kumeneko sankanena zambiri za Baibulo. Popeza ndinkafuna nditadziwa kupemphera, mnzanga wina anandiphunzitsa Pemphero la Ambuye. (Mateyo 6:9-13) Koma palibe aliyense amene ankadziwa zimene pempherolo limatanthauza. Choncho ndinkangobwerezabwereza mawu a m’pempherolo popanda kuwamvetsa, ngati mmenenso ndinkachitira ndi mapemphero a Chibuda.
Banja Langa Silinkayenda Bwino
Ndinakwatira mu 1981. Patatha chaka chimodzi tili m’banja, ine ndi mkazi wanga tinabatizidwa. Ubatizo wake unali wongowaza madzi pamutu. Panthawiyi zinthu zinkandiyendera kusiyana ndi ku Cambodia chifukwa ndinkagwira ntchito ziwiri, ndinali ndi nyumba yabwino komanso moyo wabwino. Komabe sindinkasangalala chifukwa ndinali ndi mavuto m’banja langa. Kupita kutchalitchi sikunathandize kuthetsa mavutowo, komanso sikunandithandize kusiya khalidwe langa loipa lotchova njuga, kusuta, kumwa mowa mwauchidakwa ndiponso chiwerewere. Chikumbumtima changa chinkandivutitsa ndipo ndinkaona kuti sindidzapita kumwamba, kumene ndinauzidwa kuti anthu onse abwino amapita akamwalira.
Mu 1987, ndinaitana mayi anga ndi mlongo wanga kuti abwere tizidzakhala limodzi ku New Zealand, ndipo anakhala nafe kwa kanthawi. Atachoka, ndinasiya mkazi wanga n’kuwatsatira ndipo atatufe tinakakhala kudera lina la ku Auckland.
Ndinayamba Kuphunzira Baibulo
Ndikuchokera kwa mnzanga wina, ndinakumana ndi amuna awiri amene ankayenda nyumba ndi nyumba. Mmodzi wa amunawo, dzina lake Bill, anandifunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti mudzapita kuti mukadzafa?” Ndipo ine ndinayankha kuti, “Kumwamba.” Kenako anandisonyeza m’Baibulo kuti anthu 144,000 okha ndi amene adzapite kumwamba ndipo adzakhala mafumu amene adzalamulire dziko lapansi. Anandiuzanso kuti padziko lapansi padzakhala anthu mamiliyoni ambiri oopa Mulungu ndipo dzikolo lidzakhala paradaiso. (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 4; 21:3, 4) Poyamba sindinasangalale ndi zimene ankandiuzazo chifukwa zinkatsutsana ndi zimene ndinaphunzira. Komabe ndinachita chidwi ndi mmene anthuwo ankafotokozera Malemba mofatsa. Ndipo ndinadandaula kuti sindinawafunse dzina la chipembedzo chawo.
Patapita milungu ingapo, ndinapita kwa mnzanga wina yemwe ana ake ankaphunzira Baibulo ndi banja la Dick ndi Stephanie. Ankaphunzira kabuku kakuti Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Nditayamba kukawerenga, ndinaona kuti kanali ndi mfundo zabwino. Ndinazindikira kuti banjalo linali la Mboni za Yehova. Kenako ndinazindikiranso kuti anthu awiri amene ndinakumana nawo poyamba aja analinso a Mboni za Yehova, chifukwa zimene ankalankhula zinkagwirizana ndi zimene zinali m’kabukuko.
Ndinali ndi chidwi chofuna kuphunzira zambiri, Salmo 83:18, lomwe limati: “Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, Ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” Lemba limeneli linandikhudza kwambiri ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo mokhazikika. Mtsikana amene ndinkakhala naye limodzi, wa mtundu wa Chilao dzina lake La, nayenso anayamba kuphunzira nawo. Panthawiyi ndinaitananso mchimwene wanga ndi mkazi wake kuti abwere ku New Zealand. Atangofika, nawonso anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.
ndipo ndinauza Dick ndi Stephanie kuti abwere kunyumba kwanga. Atabwera, ndinawafunsa mafunso ambiri a m’Baibulo. Kenako Stephanie anandifunsa ngati ndimadziwa dzina la Mulungu. Ndipo anandisonyeza lemba laPasanapite nthawi yaitali, ine ndi La tinasamuka kukagwira ntchito ku Australia ndipo sitinapitirize kuphunzira Baibulo. Choncho, tsiku lina usiku tinapemphera kwa Yehova kuti atidziwitse kumene kuli anthu ake.
Pemphero Lathu Linayankhidwa
Tsiku lina ndikuchokera kogula zinthu, ndinapeza Mboni ziwiri zili panyumba panga. Ndinathokoza Yehova chamumtima ndipo ine ndi La tinayambiranso kuphunzira Baibulo ndiponso kupita kumisonkhano yachikhristu ku Nyumba ya Ufumu. Pasanapite nthawi yaitali ndinazindikira kuti ndiyenera kusintha moyo wanga kuti ndisangalatse Mulungu. Ndiyeno, ndinasiya makhalidwe anga oipa ndipo ndinameta tsitsi langa, lomwe linali lalitali kwambiri. Anzanga ankandiseka koma ine sindinkadandaula nazo kwenikweni. Ndinkafunikanso kuyendetsa bwino za banja langa chifukwa ine ndi La tinkangokhalira limodzi osakwatirana ndiponso ineyo ndi mkazi wanga woyamba tinali tisanasudzulane. Choncho ine ndi La tinabwerera ku New Zealand mu 1990.
Titangofika, tinaimbira foni Dick ndi Stephanie. Ndipo Stephanie anati: “Sam, ndinkaganiza kuti sitidzaonananso.” Iwo anayambiranso kutiphunzitsa Baibulo. Kenako tinasudzulana ndi mkazi wanga, ndipo ine ndi La tinakwatirana. Tonse tinali osangalala kuti banja lathu ndi lovomerezeka kwa Mulungu. Tinakhalabe ku New Zealand, mpaka tinabatizidwa posonyeza kuti tadzipereka kwa Mulungu. Popeza kuti ndinali ndi chidwi chofuna kuuza ena zimene ndinaphunzira, ndinayamba kuphunzitsa Baibulo anthu angapo ochokera ku Cambodia ndi ku Thailand amene ankakhala ku Auckland ndiponso madera ena apafupi.
Tinabwerera ku Australia
Mu May 1996, Ine ndi La tinabwerera ku Australia ndipo tinakakhala ku Cairns, kumpoto kwa Queensland. Tili kumeneko ndinapatsidwa mwayi woyang’anira ntchito yolalikira anthu a ku Cambodia, Lao ndi ku Thailand amene ankakhala m’deralo.
Ndimalephera kuthokoza Yehova chifukwa cha madalitso amene wandipatsa. Anandipatsa mkazi wabwino ndiponso ana aamuna atatu, Daniel, Michael, ndi Benjamin. Ndikuthokozanso kwambiri Mulungu chifukwa chakuti mayi anga, mlongo wanga, mchimwene wanga, apongozi anga aakazi ndiponso mnzanga Teng Hann, amene ndinakumana naye kumalo osungira anthu othawa kwawo ku Thailand, anaphunzira choonadi cha m’Baibulo. Ine ndi anthu a m’banja lathu timadandaulabe za kusowa kwa bambo anga ndi amalume anga. Komabe sitida nkhawa kwambiri chifukwa timadziwa kuti panthawi ya chiukiriro Mulungu adzathetsa kupanda chilungamo konse ndipo zimenezi “sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.”—Yesaya 65:17; Machitidwe 24:15.
Zaka zingapo zapitazo ndinakumana ndi Bill, pamsonkhano wa Mboni za Yehova. Ndipo ndinamufunsa kuti: “Kodi mukundikumbukira?”
Iye anayankha kuti: “Inde, ndikukukumbukirani. Tinakumana ku New Zealand kale kwambiri ndipo ndinakuuzani kuti anthu 144,000 okha ndi amene adzapite kumwamba.” Bill anandikumbukira ngakhale panali patadutsa zaka zambirimbiri. Monga abale, tinakumbatirana ndipo Bill anandikumbutsa zinthu zambiri zakale.
[Mawu a Chithunzi patsamba 21]
Background: AFP/Getty Images