Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Umboni Wosonyeza Kuti Nkhani za M’baibulo N’zoona

Umboni Wosonyeza Kuti Nkhani za M’baibulo N’zoona

Umboni Wosonyeza Kuti Nkhani za M’baibulo N’zoona

▪ M’chaka cha 1870, pafupi ndi mzinda wa Baghdad ku Iraq, kunapezeka phale lalikulu masentimita 5.5. Pulofesa wina wa pa yunivesite ya Vienna ku Austria, dzina lake Michael Jursa, anapeza phale limeneli mu 2007, akufufuza zinthu kumalo osungira zinthu zakale ku Britain. Phaleli linali ndi dzina lakuti Sarisekimu ndipo Jursa anazindikira kuti dzinali linali la mkulu wina wogwira ntchito ya boma ku Babulo, yemwe anatchulidwa m’Baibulo pa lemba la Yeremiya 39:3. *

Nebo-sarisekimu anali mkulu wankhondo wa Mfumu Nebukadinezara, ndipo phaleli linasonyeza kuti anali “mkulu wa adindo” pamene asilikali a ku Babulo analanda mzinda wa Yerusalemu mu 607 B.C.E. Ndipo dzina lakuti mkulu wa adindo linkapatsidwa kwa munthu mmodzi yekha panthawi imodzi. Umenewu ndi umboni wakuti Sarisekimu amene analembedwa pa phaleli ndi yemweyo amene anatchulidwa m’Baibulo.

Phaleli limatchula za golide amene Sarisekimu anapereka ku kachisi wa Merodake, mulungu wamkulu wa ku Babulo, yemwe anatchulidwanso m’Baibulo. (Yeremiya 50:2) Paphaleli panali deti la chaka cha 10, mwezi wa 11, ndi tsiku la 18 la ulamuliro wa Nebukadinezara. Komabe, kuperekedwa kwa golideyu n’kosakhudzana ndi kuwonongedwa kwa Yerusalemu komwe kunachitika zaka zingapo pambuyo pake. (2 Mafumu 25:8-10, 13-15) Pulofesa Jursa anati: “N’zochititsa chidwi kupeza phale lolembedwa dzina la munthu yemwe anatchulidwa m’Baibulo, akupereka golide ku kachisi wa ku Babulo, lomwenso lili ndi deti lenileni.” Nyuzipepala ina ya ku Britain inanena kuti phaleli ndi limodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zimene akatswiri ofufuza zinthu zakale zokhudzana ndi Baibulo apeza. Inatinso phaleli ndi “umboni wotsimikizira kuti zimene mabuku a Chipangano Chakale amanena ndi zoona.”—Telegraph.

Komabe kulondola kwa Baibulo sikudalira zimene akatswiri ofufuza zinthu zakale apeza. Umboni wamphamvu wotsimikizira kuti Baibulo ndi lolondola ndi zimene Baibulo limanena, makamaka ulosi wake. (2 Petulo 1:21) Mwachitsanzo, Yehova kudzera mwa mneneri wake Yesaya analosera kuti chuma chonse cha Yerusalemu ‘chidzatengedwa kunka ku Babulo,’ ndipo ananeneratu zimenezi patatsala zaka zoposa 100 kuti zichitike. (Yesaya 39:6, 7) Yehova analoseranso kudzera mwa mneneri wake Yeremiya kuti: “Ndidzapereka chuma chonse cha mudzi uwu [Yerusalemu], . . . m’manja mwa adani awo, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babulo.”—Yeremiya 20:4, 5.

Nebo-sarisekimu anali mmodzi wa adani amenewo ndipo anaona ndi maso ake kukwaniritsidwa kwa ulosi wa m’Baibulo umenewo. Kaya iye ankadziwa kapena ayi, anakwaniritsa nawo ulosi umenewo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Baibulo la Dziko la Tsopano pa Yeremiya 39:3, pali mawu akuti, “Samugari-nebo, Sarisekimu, Rabisarisi,” ndipo linatsatira malemba a Chiheberi olembedwa ndi Amasorete. Koma akanatsatira kalembedwe ka Chiheberi, mawuwa akanalembedwa kuti, “Samugari, Nebo-sarisekimu m’Rabusarisi [kapena kuti Mkulu wa Adindo],” ndipo zimenezi zimagwirizana ndi mawu olembedwa m’mapale.

[Mawu a Chithunzi patsamba 11]

Copyright The Trustees of the British Museum