Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ziwombankhanga Zikuluzikulu Zogwira Nyama M’nkhalango

Ziwombankhanga Zikuluzikulu Zogwira Nyama M’nkhalango

Ziwombankhanga Zikuluzikulu Zogwira Nyama M’nkhalango

YOLEMBEDWA KU ECUADOR

▪ Anthu ofufuza malo oyamba kufika ku South America, anachita chidwi kwambiri ataona ziwombankhanga zikuluzikulu. Iwo anazipatsa dzina la nyama ina yomwe Agiriki ankanena mu nthano zawo. Akuti nyamayi kumutu inkaoneka ngati munthu wamkazi koma thupi ngati mbalame.

Mpaka pano, anthu amachitabe chidwi ndi kukula kwa ziwombankhangazi. Mbalamezi zimapezeka m’nkhalango za ku Central ndi South America ndipo n’zazikulu kwambiri ndiponso zamphamvu. Zimakula mpaka kufika masentimita 91 ndipo mapiko ake amafika mamita awiri. Ziwombankhanga zazikazi n’zimene zimakhala zazikulu kwambiri ndipo zimatha kulemera makilogalamu 9.

Ziwombankhanga zimenezi zimakhala ndi zikhadabo zazitali kwambiri kuposa ziwombankhanga zina zonse, moti zimafika masentimita 13. Ndipo magazini ina inanena kuti ziwombankhanga zimenezi ndi zamphamvu kwambiri moti zingaphwanye “mafupa a anyani, apusi ndi nyama zina za m’nkhalango. Zimati zikagwira nyamazi zimapheratu pomwepo.” Komabe, ngakhale kuti ziwombankhangazi n’zazikulu kwambiri komanso zoopsa, zimauluka mwakachetechete moti zimatha kudutsa osaziona.

Mbalamezi Zikutha

Ngakhale kuti ziwombankhangazi sizipha anthu, anthu akumazipha kwambiri komanso akumawononga malo omwe zimakhala moti zili m’gulu la nyama zimene zikutha padziko lonse. Pofuna kuzipulumutsa, dziko la Panama linaika lamulo loletsa kupha mbalamezi ndipo anthu opezeka akuzipha, amalandira chilango chokhwima.

Dziko la Ecuador likuyesetsanso kuteteza mbalamezi. Wolemba Galamukani! anacheza ndi Dr. Yara Pesantes wa kumalo osungirako nyama a Guayaquil, ndipo anafotokoza kuti ziwombankhangazi zimayamba kubereka zikafika zaka zinayi kapena zisanu. Pazaka ziwiri zilizonse zimabereka mwana mmodzi kapena awiri basi. Zimenezi zikuchititsa kuti mbalamezi zisachuluke msanga. Koma Dr. Pesantes ananena kuti kumalo osungirako nyama kumene iwo amagwira ntchito kuli kamwana ka chiwombankhanga komwe kabadwa kumene.

Posachedwapa, anthu sadzavutikanso kuteteza nyama. Zili choncho chifukwa Mlengi wathu, Yehova Mulungu, adzachotsa amene amawononga dziko lapansi ndipo adzasonyeza kuti sanalenge dzikoli ndi zamoyo zake zonse pachabe.—Salmo 104:5; Yesaya 45:18.

[Chithunzi patsamba 25]

Kuika chiwombankhanga chizindikiro

[Mawu a Chithunzi]

Pete Oxford/Minden Pictures

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Tui De Roy/Roving Tortoise Photos