Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Ku Russia, zinthu zosiyanasiyana zokwana 160,000 zasowa m’malo osungirako zinthu zakale.”—RIA NOVOSTI, RUSSIA.

“Kachipangizo kamene bungwe loona za kuthambo la NASA anakatumiza ku pulaneti la Mars kanapeza kuti m’mitambo ya papulanetili munkagwa chipale chofewa.”—NASA MISSION NEWS, U.S.A.

“65 peresenti ya anthu okwera ndi oyendetsa galimoto amene amafa pangozi ku Greece amakhala kuti sanamange malamba kapena kuvala zipewa zodzitetezera.”—EIKONES, GREECE.

Katundu Wotayika

Katundu wambiri amatayika pamaulendo a pandege. Nyuzipepala ina ya ku Paris inanena kuti mu 2007, “zikwama 42 miliyoni zinasowa ndipo chiwerengero chimenechi chikuposa chiwerengero cha 2006 ndi 25 peresenti.” Zambiri mwa zikwamazi zinatumizidwa kwa eniake pasanathe masiku awiri, koma zikwama zoposa 1 miliyoni zinasoweratu. Zimenezi zikutanthauza kuti mwa anthu 2,000 aliwonse amene amayenda pa ulendo wa pandege, mmodzi chikwama chake chimasoweratu.” M’chaka cha 2007, makampani a ndege anawononga ndalama zokwana madola 3.8 biliyoni kulipira katundu wotayika. Zina mwa zinthu zimene zimachititsa kuti katundu azisowa ndi “kuchuluka kwa anthu apaulendo, kuchepa kwa nthawi imene ndege zimakhala pabwalo la ndege,” kusasamala, komanso kulakwitsa polemba zizindikiro.—International Herald Tribune.

Akatolika Ambiri Akumakhalira Limodzi Popanda Dongosolo la Ukwati

Ofufuza ena a ku France, anapeza kuti “kuchepa mphamvu kwa chipembedzo” n’kumene kukuchititsa kuti anthu asakhale ndi makhalidwe abwino. (Population & Sociétés) Mwachitsanzo, 88 peresenti ya achinyamata a zaka zoyambira 18 mpaka 24 ku France amanena kuti ndi Achikatolika, koma 80 peresenti ya achinyamata amenewa, sapita ku tchalitchi. Amangopita kukakhala ukwati, ubatizo kapena maliro. Mabanja ambiri akusonyeza kuti chikhalidwe chasokonekera. Panopa mabanja 9 pa 10 aliwonse amakhala limodzi popanda dongosolo lililonse la ukwati, pamene zaka 40 zapitazo, banja limodzi lokha pa 10 aliwonse ankakhala limodzi popanda dongosolo lililonse la ukwati. Anapezanso kuti “Akatolika 75 pa 100 aliwonse ankakhala limodzi popanda dongosolo lililonse la ukwati.”

Alimi Ambiri ku India Akudzipha

Nyuzipepala ya Hindu inanena kuti kuyambira mu 2002, alimi oposa 17,000 a ku India adzipha ndipo ambiri anachita zimenezi pomwa mankhwala ophera tizilombo. Alimiwa amakumana ndi mavuto ambiri monga chilala, kutsika kwa mitengo yogulitsira mbewu zawo, kudula kwa zipangizo za ulimi, komanso kulephera kupeza ngongole m’mabanki. Chifukwa cha zimenezi alimi ambiri amabwereka ndalama kwa anthu wamba amene amafuna chiwongola dzanja chachikulu. Kuti abweze ngongolezi alimi ena amagulitsa ziwalo za thupi lawo. Akalephera kubweza ngongole zawo, njira yachidule imangokhala kudzipha.

Ana a Ng’ona za mu Nile Amalankhulana Asanatuluke M’mazira

Nyuzipepala ya Times inanena kuti: “Ana a ng’ona amalankhulana ali m’mazira akamabadwa.” Anthu ena anajambula phokoso limene ana a ng’onawa amapanga asanabadwe. Kenako phokosolo anakalibwereza pafupi ndi mazira ena. Tiana ta ng’ona tomwe tinali m’mazirato timayankha ndipo mazirawo ankagwederagwedera. Nyuzipepalayi inati: “Ana amene anamva phokoso la anzawo anayamba kutuluka m’mazira pasanathe mphindi 10.” Ana a m’mazira amene sanamve kuliraku kapena amene anawaika pamalo aphokoso lina, sanatuluke panthawi imeneyi.