Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata a Katolika Anauzidwa Kuti Azilalikira

Achinyamata a Katolika Anauzidwa Kuti Azilalikira

Achinyamata a Katolika Anauzidwa Kuti Azilalikira

YOLEMBEDWA KU AUSTRALIA

MWEZI wa July 2008, Akatolika ochokera m’mayiko osiyanasiyana anasonkhana mu mzinda wa Sydney ku Australia, pokondwerera mwambo wa Tsiku la Achinyamata Padziko Lonse, womwe umakonzedwa ndi tchalitchi cha Katolika.

Anthu ochokera ku mayiko 170 anaima m’misewu ndipo ankakuwa, kuimba ndiponso kuvina, uku akukupiza mbendera. Khwimbi la anthu linkadikirira pa doko la Sydney kuti aone Papa Benedict XVI akubwera. Iye anabwera pa boti lomwe linatsogozana ndi maboti enanso 12 okongola kwambiri. Padziko lonse, anthu enanso okwana 500 miliyoni ankaonera mwambowu pa TV.

Anthu okwana 400,000, kuphatikizapo akuluakulu a tchalitchi cha Katolika okwana 4,000 komanso atolankhani okwana 2,000, anaonerera mwambo wa Misa, womwe unachitika pomalizira, pabwalo la zamasewera la Sydney. Pamwambo umenewu panafika anthu ambiri zedi kuposa anthu amene anayamba asonkhanapo pabwalo limodzi ku Australia. Anthuwa anaposa ngakhale anthu amene anabwera kudzaonera masewera a Olympic amene anachitikira pabwalo la Sydney m’chaka cha 2000.

Kodi cholinga cha mwambo wa Tsiku la Achinyamata Padziko Lonse n’chiyani? Kodi patsikuli pamachitika zinthu zotani? Kodi mwambo wa ku Sydney umenewu unasonyeza chiyani za chikhulupiriro cha achinyamata?

“Chikhulupiriro Chikutha”

Tsiku la Achinyamata Padziko Lonse ndi mwambo umene umachitika chaka chilichonse polimbikitsa achinyamata a Katolika kuti azikhalabe ndi chikhulupiriro. Nthawi zambiri Akatolika amachitira mwambo umenewu ku dayosisi ya kwawo. Koma pazaka ziwiri kapena zitatu zilizonse, achinyamata a Katolika padziko lonse amasonkhana m’mizinda ikuluikulu kuti achite mwambo umenewu. Misonkhano yotereyi imachitika m’mizinda 10, m’zigawo zisanu za padziko lonse, ndipo anthu mamiliyoni ambiri aonerapo mwambowu.

Koma monga mmene akuluakulu a tchalitchi cha Katolika amanenera, cholinga china cha mwambowu ndi kulimbikitsa anthu kuti asasiye Chikatolika. Mkulu wina wa tchalitchi cha Katolika ku Australia, dzina lake Kadinala George Pell, anati: “Vuto lalikulu limene tikukumana nalo ndi lakuti, anthu ambiri akusiya tchalitchi cha Katolika ndipo tingati chikhulupiriro chawo chikutha. Cholinga cha mwambowu ndi kuyesetsa kuthetsa vuto limeneli.”

Malinga ndi lipoti la ku Vatican, chiwerengero cha ansembe chikutsika kwambiri padziko lonse. Zaka zaposachedwapa, anthu ambirimbiri asiya unsembe ndi cholinga choti akwatire. Chiwerengero cha anthu amene akuphunzira za unsembe chatsika ndi 70 peresenti m’zaka 30 zapitazi. Avereji ya zaka za ansembe ku dayosisi yaikulu kwambiri ku Australia ndi 60, pamene mu 1977 avereji inali 40.

Chiwerengero cha anthu amene amapita ku tchalitchi chatsikanso m’mayiko ambiri. Pafupifupi anthu 25 pa 100 aliwonse ku Australia amati ndi Akatolika, koma ndi anthu 14 pa 100 aliwonse amene amapita ku tchalitchi nthawi zonse. Achinyamata a Katolika osakwana 10 pa 100 aliwonse ndi amene amapita ku tchalitchi. Ndipo Akatolika ambiri satsatira zimene amaphunzira pankhani za kugonana, njira zakulera, ndiponso kusudzulana. Ena amakhumudwa ndi zinthu zoipa zimene ansembe awo amachita monga khalidwe logona ana.

Nyuzipepala ina ya ku Australia inanena kuti cholinga cha Tsiku la Achinyamata Padziko Lonse ndicho “kuyesayesa kuti tchalitchi chisachite kugweratu. Atsogoleri a tchalitchichi ku Australia ndi ku Rome akuyesetsa kupeza njira yolimbikitsira tchalitchi pothandiza achinyamata.” (The Sydney Morning Herald) Kodi atsogoleriwa akuchita chiyani kuti akwaniritse cholinga chimenechi?

Ziwonetsero Ndiponso Zisangalalo

Pamwambo wa Tsiku la Achinyamata Padziko Lonse wa 2008, panali ziwonetsero, kukambirana m’magulu, maulendo opita kumalo opatulika, ndiponso chikondwerero cha Misa. Ngakhale kuti zochitika zimenezi zinathandiza kwambiri anthu amene anabwera, ena anaona kuti zinthu zina sizinali bwino. Mtsikana wina wa Katolika dzina lake Alexandra, yemwe anachokera ku United States, ananena kuti mwambowu unali “phwando lalikulu basi.”

Mwambowu unali wa masiku 6, ndipo kunali zochitika zosiyanasiyana zokwana 450, monga nyimbo, mafilimu, zisudzo, ndi zochitika zina. Kunali nyimbo za mitundu yonse, kuyambira nyimbo za zisudzo ndi nyimbo za Chikatolika mpaka nyimbo za heavy metal ndi rap. Nyimbo za Rock n’zimene zinakopa achinyamata ambiri okonda zachisangalalo.

Akatolika ena sanasangalale ndi zochitika za pamwambowu. Wansembe wina dzina lake Peter Scott anauza mtolankhani wa nyuzipepala ya ku Australia ya ABC kuti mwambowu “wangokhala ngati chiphwando chachikulu, nthawi ya kudya ndi kuyimba ndiponso yochita zinthu zosiyanasiyana zadziko. Pamwambowu panali zinthu zochepa zauzimu ndiponso zopatulika.” Ndipotu m’chaka cha 2000, Papa Benedict XVI, yemwe panthawiyo anali Kadinala Ratzinger, anati: “‘Nyimbo za Rock zimasonyeza chikondwerero chakuthupi, ndipo anthu akamaimba kapena kumvera nyimbo zimenezi amakhala akulambira, koma kulambira kumeneku n’kotsutsana ndi Chikhristu.”—The Spirit of the Liturgy.

Koma funso ndi lakuti: “Kodi Tsiku la Achinyamata Padziko Lonse limathandizadi achinyamata?” Wansembe wina wakale dzina lake Paul Collins anati: “Mwina limathandiza achinyamata ochepa kwambiri. Koma achinyamata ambiri akachoka ku mwambowu amakapitiriza moyo wawo wakale. Dziwani kuti munthu sasintha chifukwa choonerera mwambo umodzi wochititsa chidwi. Koma amasintha akaganizira mofatsa za moyo wake, akaganizira bwino za tsogolo lake komanso akafunitsitsa kusiya zimene ankachita kale.”

“Mudzakhala Mboni Zanga”

Atsogoleri ambiri a tchalitchi amadziwa kuti kulalikira n’kofunika. N’chifukwa chake mutu wa Tsiku la Achinyamata Padziko Lonse mu 2008, unali wakuti: “Mudzalandira mphamvu pamene mzimu woyera udzafika pa inu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga.” *

Mabishopu osiyanasiyana analangiza anthu amene anapita ku mwambowu kuti ayenera “kukhala ndi mtima wofunitsitsa kulalikira Uthenga Wabwino.” Papa Benedict XVI, anauza anthu amene anapita ku mwambowu kuti “akhale ndi mtima ngati wa atumwi.” Panthawi ina, iye anawalangizanso anthu kuti azilalikira “Uthenga Wabwino kwa anzawo, achibale awo, ndiponso kwa aliyense amene angakumane naye.”

Anthu ena anakhudzidwa mtima ndi mfundo zimenezi. Mwachitsanzo, mnyamata wina wa zaka 20 wochokera ku United States dzina lake Ramido, anauza mtolankhani wina kuti: “Ndimaona kuti kulalikira n’kofunika kwambiri.” Mtsikana wina wa ku Italy wa zaka 18, dzina lake Beatrice, anati: “Achinyamata masiku ano salankhula za Mulungu. Kulalikira masiku ano n’kovuta kwambiri.” Anthu ambiri amene anabwera kumwambowu anavomereza zimene ananena atsikana ena awiri ochokera ku Texas, U.S.A., kuti: “Kwathu ndi Mboni za Yehova zokha zimene zimalalikira.”

Achinyamata Amene Amalalikira

A Mboni za Yehova, ana ndi akulu omwe, ndi amene amadziwika kuti amalalikira modzipereka. N’chifukwa chiyani amalalikira? Mtsikana wina wa Mboni wa zaka 22 wochokera ku Sydney, dzina lake Sotir, anati iwo amalalikira chifukwa chakuti “amakonda Mulungu, anthu ndiponso Baibulo.”

Panthawi imene mwambowu unkachitika, pafupifupi achinyamata 400 a Mboni za Yehova a ku Sydney, anagwira ntchito yapadera youza achinyamata a Katolika mfundo za m’Baibulo, ngakhale kuti iwo sanapite nawo ku mwambowo. Mnyamata wina wa zaka 25, dzina lake Travas, anati: “Ndinasangalala kwambiri kukumana ndi achinyamata a Katolika okonda zinthu zauzimu amenewa. Ambiri mwa iwo anali ndi mafunso abwino okhudza Baibulo, ndipo ndinasangalala kwambiri kuwauza mayankho ake.”

Mtsikana wina wa zaka 23, dzina lake Tarsha, anati: “Powalalikira, ndinkalankhula nawo momasuka ndiponso mofatsa. Ndinkayamba ndi kuwauza kuti tawalandira ku Sydney ndipo kenako ndimawafunsa zimene amakhulupirira.” Mnyamata wina wa zaka 20, dzina lake Frazer, anati: “Ndikaona kuti ali ndi chidwi, ndinkawapatsa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * monga mphatso. Aliyense amene ndinakumana naye anasangalala kulandira bukuli.”

Alendo ambiri anasangalala kucheza ndi achinyamata a Mboni. Mwachitsanzo, Suzanne wa ku Fiji anafunsa mtsikana wa Mboni wa zaka 19, dzina lake Belinda, chifukwa chimene Mulungu walolera kuti anthu azivutika. Belinda anamuyankha pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Atamaliza kukambirana, Suzanne anati: “Nthawi zambiri anthu amandiuza kuti zochita za Mulungu palibe angazimvetse. Koma lero ndapeza yankho.” Belinda atamupatsa bukulo, Suzanne anati: “Pamene timakambirana, ndimayesetsa kuloweza chilichonse chomwe umanena, sindimadziwa kuti undipatsa bukuli.”

Mlendo wina wochokera ku Philippines anam’pempha mtsikana wina wa Mboni wa zaka 27, dzina lake Marina, kuti amujambule. Kenako anayamba kukambirana za m’Baibulo ndipo Marina anam’patsa mayiyo buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Mayiyo anati: “Usiku wapitawo ndinapempha Mulungu kuti andithandize kumvetsa zimene Baibulo limanena. Mwina bukuli ndi yankho la pemphero langa.”

Mnyamata wina wa Mboni wa zaka 27, dzina lake Levi, anacheza ndi mayi ndi mwana wake wamkazi ochokera ku Panama. Kenako anayamba kukambirana za Mulungu ndipo anakambirana nkhani zambiri za m’Baibulo. Iwo analandira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kenako Levi anawafunsa kuti afotokoze chimene chawasangalatsa kwambiri paulendowo. Mtsikanayo anatenga buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani n’kuyankha kuti: “Tasangalala kwambiri kukumana ndi inuyo.”

Achinyamata ambiri a Katolika ankafunitsitsa kudziwa zambiri za m’Baibulo. Nanga bwanji inuyo? Kodi mukufuna kulimvetsa bwino Baibulo? Ngati mukufuna, pemphani a Mboni za Yehova kuti ayambe kuphunzira nanu Baibulo kwaulere. Iwo adzasangalala kukuthandizani.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Mutuwu unatengedwa pa Machitidwe 1:8.

^ ndime 25 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

“Vuto lalikulu limene tikukumana nalo ndi lakuti, anthu ambiri akusiya tchalitchi cha Katolika ndipo chikhulupiriro chawo chikutha.”—Anatero Kadinala George Pell wa mpingo wa Roma Katolika

[Bokosi/Zithunzi patsamba 25]

ANALIMBIKITSIDWA KUGWIRA NTCHITO ZOSIYANASIYANA ZA TCHALITCHI

Patsiku Lokumbukira Achinyamata Padziko Lonse m’chaka cha 2008 ku Australia, kunachitika ziwonetsero zosiyanasiyana za tchalitchi zomwe sizinachitikepo chiyambire. Nthambi zoposa 100 za tchalitchi cha Katolika zinalimbikitsa achinyamata opitirira 50,000 omwe anabwera ku mwambowu kuti adzakhale ansembe, masisitere kapena adzagwire ntchito zina za tchalitchi cha Katolika.

[Chithunzi patsamba 24, 25]

Alendo ovala zovala zokongola akuyenda m’misewu

[Chithunzi patsamba 26]

Mboni za Yehova zinalalikira alendo amene anabwera mu mzinda wa Sydney

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Getty Images