Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chifukwa Chake Sitinachotse Mimba

Chifukwa Chake Sitinachotse Mimba

Chifukwa Chake Sitinachotse Mimba

VICTORIA, yemwe tinamutchula mu nkhani yoyambirira uja anauza mwamuna wake Bill kuti sachotsa mimba. Iye anati: “Ndinkaona kuti ndanyamula moyo wa munthu. Ndipo nditazindikira kuti Bill sazindisamalira panthawi imene ndinali ndi mimbayo, tinasiyana.”

Kenako Bill anasintha maganizo ndipo anauza Victoria kuti akwatirane. Koma kusamalira mwana wawoyo chinali chintchito. Victoria anadandaula kuti: “Tinalibe ndalama, galimoto ndiponso zovala. Mwina tingoti tinali ndi zinthu zochepa. Komanso Bill sankalandira ndalama zambiri ku ntchito, ndipo tinkakhala m’kanyumba kakang’ono, koma tinapirirabe.”

Anthu enanso ambiri avutikapo chifukwa chokhala ndi pakati posakonzekera, koma sanachotse mimbayo. Kodi chinawathandiza n’chiyani kuti asachotse komanso kuti alere mwana amene sankamuyembekezerayo? Chinsinsi chake ndi kutsatira mfundo za m’Baibulo.

Musapupulume

Baibulo limanena mawu anzeru awa: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphawi.”Miyambo 21:5.

Mayi wina dzina lake Connie anali ndi ana atatu aamuna, ndipo mmodzi anali wolumala. Ndipo atapezekanso kuti ali ndi pakati, anadandaula kwambiri. Iye anati: “Tinalibe ndalama zosamalirira mwana wina. Choncho ine ndi mwamuna wanga tinaganiza zongochotsa mimbayo.” Koma asanachite zimenezi, iye anafotokozera mnzake wina wogwira naye ntchito, dzina lake Kay. Mnzakeyo anamuthandiza kuona kuti mwana wosabadwayo ndi munthu. Ndipo Connie anasintha maganizo.

Komabe panafunikira munthu wina woti azimuthandiza Connie panthawiyo komanso mwanayo atabadwa. Popeza kuti Connie anali ndi mayi ake aakulu m’dera limene ankakhala, Kay anamuuza kuti akawafotokozere nkhaniyi. Iwo anamuthandiza kwambiri. Komanso mwamuna wa Connie anayamba kugwiranso ntchito zina, ndiponso banjali linasamukira m’nyumba yotsika mtengo. Choncho iwo anatha kusamalira mwanayo atabadwa.

Kay anathandizanso Connie kupeza mabungwe amene amathandiza anthu amene ali ndi pakati posakonzekera. Mabungwe amenewa amapezeka m’mayiko ambiri ndipo amathandizanso akazi amene abereka asanakonzekere. Malo ambiri obwereketsa mabuku amakhala ndi Intaneti komanso manambala a foni amene angakuthandizeni kupeza mabungwe amenewa. Kuti mupeze thandizo limeneli ndi chintchito, koma kumbukirani kuti “zoganizira za wakhama” n’zimene zimapindulitsa.

Dziwani Kuti Mwanyamula Moyo wa Munthu

Baibulo limati: “Wanzeru maso ake ali m’mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima.”—Mlaliki 2:14.

Mayi wanzeru satseka maso kuti asaone zenizeni zimene zikuchitika ‘n’kumayenda mumdima.’ Amagwiritsa ntchito ‘maso a m’mutu wake’ zomwe zikutanthauza kuti amaganiza bwino. Zimenezi zimamuthandiza kuti asankhe zinthu mwanzeru. Choncho, mosiyana ndi mayi amene watseka maso ake kuti asaone zenizeni zimene zikuchitika m’mimba mwake, mayi wanzeru amasonyeza chifundo kwa mwana wake wosabadwa.

Mtsikana wina yemwe anali ndi pakati pa miyezi iwiri, dzina lake Stephanie, ankaganiza zochotsa mimba, koma anasintha maganizo dokotala atamuonetsa chithunzi cha mwana wosabadwayo. Iye anati: “Nditamuona, ndinalira kwambiri. Ndinadzifunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ndimafuna kupha mwana wabwinobwinoyu?’”

Mtsikana winanso wosakwatiwa dzina lake Denise anali ndi pakati ndipo anazindikira kuti kuchotsa mimba si bwino. Chibwenzi chake chitamupatsa ndalama n’kumuuza kuti “dziwa nayo chochita,” Denise anayankha kuti: “Ukufuna kuti ndichotse mimba? Sindingachite zimenezo.” Iye anakaniratu kupha mwana wakeyo.

Si Bwino Kuopa Anthu

Ngati ena atakuuzani kuti muchotse mimba, mungachite bwino kuganizira mawu anzeru a m’Baibulo akuti: “Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.”Miyambo 29:25.

Mtsikana wina wa zaka 17, dzina lake Monica, anapatsidwa mimba ndi chibwenzi chake atatsala pang’ono kuyamba sukulu yophunzitsa zamalonda. Mayi ake, omwe anali mkazi wamasiye wa ana asanu, anakhumudwa kwambiri. Iwo ankafuna kuti mwana wawoyo aphunzire ntchito inayake n’cholinga choti adzawagwire dzanja. Chifukwa chothedwa nzeru, mayiwo anauza Monica kuti achotse mimbayo. Monica anati: “Adokotala atandifunsa ngati ndinkafunadi kuchotsa mimba, ndinayankha mwamphamvu kuti ‘Ayi!’”

Mayiwo ataona kuti tsogolo la Monica lawonongeka komanso akhala ndi ntchito yosamalira mwana wina, anamuthamangitsa pakhomo pawo. Monica anakakhala ndi mayi ake aakulu. Patapita milungu ingapo, mayi ake anamukhululukira ndipo iye anabwereranso kunyumba. Monica anabereka mwana, dzina lake Leon, ndipo mayi ake anamuthandiza kulera mwanayo. Patapita nthawi anayamba kum’konda kwambiri mdzukulu wawoyo.

Mayi wina wa pabanja dzina lake Robin anauzidwa ndi dokotola kuti achotse mimba. Iye anati: “Dokotala anandipatsa mankhwala a matenda a impso. Koma atadziwa kuti ndinali ndi pakati, anandiuza kuti ndikhoza kubereka mwana wozerezeka. Choncho dokotalayo anandiuza kuti ndingochotsa mimbayo. Atanena zimenezi, ndinamufotokozera zimene Baibulo limanena zokhudza moyo wa munthu. Ndinamutsimikizira kuti sindingachotse mimbayo.”

Ngakhale kuti zimene ananena dokotalazi zinali zomveka, Robin anabereka bwinobwino. * Robin anati: “Mwana wanga atabadwa, anapezeka kuti vuto lake silinali lalikulu kwambiri. Iye amatha kuchita zinthu bwinobwino. Panopa ali ndi zaka 15 ndipo amayesetsa kuwerenga bwino. Ndimamukonda kwambiri ndipo tsiku lililonse ndimathokoza Yehova chifukwa chondipatsa mwana wamkazi ameneyu.”

Kukhala Paubwenzi ndi Mulungu N’kothandiza

Baibulo limati: “Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye.”Salmo 25:14.

Anthu ambiri amakana kuchotsa mimba chifukwa amadziwa kuti Mlengi sasangalala ndi zimenezi. Amaona kuti kukhala paubwenzi ndi Mulungu ndiponso kuchita zimene iye amakondwera nazo, n’kofunika kwambiri. Zimenezi n’zimene zinachititsa Victoria, amene tamutchula kale uja, kuti akane kuchotsa mimba. Iye anati: “Ndinkakhulupirira kwambiri kuti Mulungu ndi amene amapereka moyo, choncho ndinaona kuti ineyo ndinalibe mphamvu zochotsera moyo wa mwana amene Iye anandipatsa.”

Victoria atayamba kuphunzira Baibulo ndi mtima wonse, ubwenzi wake ndi Mulungu unakula. Iye anati: “Nditasankha zoti ndisachotse moyo wa mwana wanga, ubwenzi wanga ndi Mulungu unalimba ndipo ndinkafuna kuti ndizimusangalatsa nthawi zonse. Ndikapemphera, iye ankandiyankha.”

Kukhala paubwenzi ndi Mulungu, yemwe ndi chitsime cha moyo wathu, kumatithandiza kulemekeza moyo wa mwana wosabadwa. (Salmo 36:9) Ndiponso Mulungu amapereka “mphamvu yoposa yachibadwa” imene imathandiza mayi ndi banja lake kuchita zinthu mwanzeru akakhala ndi mimba yosakonzekera. (2 Akorinto 4:7) Kodi anthu amene sanachotse mimba chifukwa chomvera Mulungu pankhani yolemekeza moyo wa mwana wosabadwa, amamva bwanji akaganizira zimene anasankha kuchita?

Sanong’oneza Bondo

Makolo amene sanachotse mimba sadziimba mlandu kapena kumva chisoni ndi zimene anachita. M’kupita kwa nthawi, iwo anaona kuti ana ndi “chipatso cha m’mimba,” kapena kuti dalitso osati temberero. (Salmo 127:3) Connie, yemwe tamutchula kale uja, anazindikira zimenezi patangopita maola awiri kuchokera pamene mwana wake anabadwa. Mosangalala, iye anaimbira foni mnzake wa kuntchito uja, n’kumuuza kuti akufunitsitsa kwambiri kulera kamwana kakeko. Mosangalala Connie anati: “N’zoonadi, Mulungu amadalitsa anthu amene amamumvera.”

Kodi n’chifukwa chiyani kumvera Mulungu pankhani yolemekeza moyo kuli kofunika? Chifukwa chakuti malamulo amene Mulungu, monga Chitsime cha moyo, anatipatsa ndi othandiza komanso ‘okomera ifeyo.’—Deuteronomo 10:13.

Victoria ndi Bill, amene tawatchula m’nkhani ino ndiponso yoyambirira ija, moyo wawo unasintha kwambiri atasankha kuti Victoria asachotse mimba. Iwo anati: “Tinkagwiritsa ntchito kwambiri mankhwala osokoneza bongo ndipo tikanapitiriza, bwenzi pano titafa. Koma chifukwa chofuna kulemekeza moyo wa mwana wathu wosabadwa, tinasiya kugwiritsa ntchito mankhwalawa ndipo tinayamba kuganizira mofatsa za moyo wathu. Mboni za Yehova zinatithandiza kwambiri ndipo tinasintha khalidwe lathu.”

Panopa, mwana wawo Lance ali ndi zaka 34, ndipo wakhala zaka zoposa 12 m’banja. Lance anati: “Kuyambira ndili mwana, makolo anga anandiphunzitsa kutsatira mfundo za m’Baibulo posankha zinthu. Zimenezi zathandiza kwambiri ineyo, mkazi wanga ndiponso mwana wathu kukhala osangalala. Bambo ake a Lance, omwe poyamba ankafuna kuti mkazi wawo, Victoria, achotse mimba anati: “Timachita mantha tikaganiza kuti tinatsala pang’ono kuchotsa mimba ya mwana wathu wokondedwa ameneyu.”

Taganiziraninso za Monica, amene anakana kuchotsa mimba ngakhale kuti mayi ake ankamukakamiza. Iye anati: “Patangopita milungu iwiri mwana wanga atabadwa, ndinakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo anandithandiza kuti ndiyambe kutsatira malamulo a Mulungu pamoyo wanga. Kenako ndinayamba kuphunzitsa mwana wanga Leon kufunika komvera Mulungu ndipo patapita nthawi iye anayamba kukonda kwambiri Mulungu. Panopa Leon ndi mtumiki yemwe amayendera mipingo ya Mboni za Yehova.

Pofotokoza zimene mayi ake anachita, Leon anati: “Ndikudziwa kuti mayi anga anandikonda kwambiri posankha kuti ndikhalebe ndi moyo ngakhale kuti ankauzidwa kuchotsa moyo wanga. Zimenezi zandithandiza kuti ndizichita zinthu mwanzeru pamoyo wanga posonyeza kuti ndimayamikira Mulungu chifukwa cha mphatso ya moyo imene anandipatsa.”

Anthu ambiri amene azindikira malamulo a Mulungu okhudza moyo, sanong’oneza bondo chifukwa choti anakana kuchotsa moyo wa mwana wawo amene panopa amaona kuti ndi wamtengo wapatali. Iwo amanena mosangalala kuti “Tinachita bwino kuti sitinachotse mimba.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Ngati anthu amene akukhudzidwa aona kuti mayi pobereka, iyeyo kapena mwana wake afa, angasankhe kuti achita bwanji. Komabe zimenezi sizichitikachitika masiku ano, chifukwa m’mayiko ambiri njira zachipatala zapita patsogolo kwambiri.

[Chithunzi patsamba 7]

Stephanie anakana kuchotsa mimba ataona chithunzi cha mwana wake wosabadwa wa miyezi iwiri

(mzere wozungulirawo tachita kuika)

[Chithunzi patsamba 8]

Victoria ali ndi mwana wake Lance

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Victoria ndi Bill ali ndi mwana wawo Lance komanso banja lake posachedwapa

[Chithunzi patsamba 9]

Monica ali ndi mwana wake Leon. Iye akusangalala kuti sanachotse moyo wa mwana wakeyo, zaka 36 zapitazo