Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Khalani Maso”

“Khalani Maso”

Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova Wakuti:

“Khalani Maso”

▪ Msonkhano wa masiku atatu umene uyambe pa May 22 mpaka 24 ku United States, udzachitika padziko lonse lapansi m’malo ambiri osiyanasiyana m’miyezi ikubwerayi. Ku United States msonkhanowu uzidzayamba ndi nyimbo nthawi ya 9:20 m’mawa tsiku lililonse. Nkhani ya tsiku Lachisanu yatengedwa pa Mateyo 24:44 ndipo ili ndi mutu wakuti “Khalani Okonzeka.” Tcheyamani akadzamaliza kulankhula, padzabwera nkhani yakuti “Misonkhano Yachigawo Imatithandiza Kukhala Maso” ndiponso yakuti “Yehova ndi Mulungu wa Nthawi ndi Nyengo.” Kenako padzabwera nkhani yosiyirana ya mutu wakuti “Tsanzirani Anthu Okhulupirika Amene Anakhalabe Maso.” Nkhaniyi idzasonyeza mmene Nowa, Mose, ndiponso Yeremiya anakhalira maso. Chigawo cha m’mawa chidzatha ndi nkhani yaikulu ya mutu wakuti, “Mmene Yehova Amatithandizira ‘Kukhalabe Maso.’”

Nkhani yoyamba m’chigawo cha masana idzakhala ya mutu wakuti, “Mayankho a Mafunso Okhudza ‘Masiku Otsiriza.’” Kenako padzabwera nkhani yakuti “Chifukwa Chake Simukudziwa ‘Tsiku Kapena Ola Lake’” ndiponso yakuti “Dziwani Kuti Mapeto Ayandikira.” Ndiyeno padzabwera nkhani yosiyirana ya mutu wakuti “Mabanja Achikhristu Afunika ‘Kukhala Maso.’” Mbali zitatu zoyambirira zidzakhala zokhudza amuna, akazi ndiponso ana. Ndipo zitatu zotsatira zidzakhala zakuti, “Khalani ndi Diso Lolunjika Chimodzi,” “Pitirizani Kukhala ndi Zolinga Zauzimu,” ndiponso “Pitirizani Kuchita Kulambira kwa Pabanja.” Chigawo cha masana chidzatha ndi nkhani yakuti, “Mavesi Amene Amatithandiza Kuti Tikhale ‘Osamala Kwambiri.’”

Mutu wa tsiku Loweruka watengedwa pa 1 Petulo 5:8 ndipo ndi wakuti, “Sungani Maganizo Anu, Khalani Maso.” Nkhani yosiyirana yakuti “Thandizani Anthu Kuti ‘Adzuke Kutulo,’” ili ndi mbali zisanu izi: “Chifukwa Chiyani Utumiki Wathu Uli Wofunika Kwambiri,” “Khalani Maso mu Utumiki,” “Yesetsani Kuwonjezera Luso Lanu,” “Musayiwale Achibale Anu,” ndi “Pitirizani Kukhala Achangu.” Kenako padzabwera nkhani zakuti “Tsanzirani Yesu Yemwe Anakhala Maso,” “Khalani Maso Kuti Musanyalanyaze Kupemphera.” Chigawochi chidzatha ndi nkhani ya ubatizo, ndipo pambuyo pake anthu amene akuyenerera ubatizo adzapita kokabatizidwa.

Loweruka masana kudzakhala nkhani yosiyirana ya mbali zisanu ya mutu wakuti: “Samalani ndi Misampha ya Satana.” Mbali zake ndi izi: “Moto,” “Dzenje,” “Msampha,” “Msampha Umene Umatsamwitsa,” ndi “Msampha Umene Umangopheratu.” Kenako padzabwera sewero la mawu okha la mutu wakuti, “Mpaka Kufa Ine Sindidzataya Umphumphu Wanga.” Chigawochi chidzatha ndi nkhani zakuti “Musayang’ane ‘Zinthu za M’mbuyo’” ndi “Tsatirani Chitsanzo cha Atumwi a Yesu Pankhani Yokhala Maso.”

Mutu wa tsiku Lamlungu wachokera pa Habakuku 2:3, ndipo ndi wakuti “Uwalindirire . . . Sadzazengereza.” Pambuyo pa nkhani yonena za mutu wa nkhaniyi, padzabwera nkhani yosiyirana ya mutu wakuti “Ikani Maso pa Zinthu Zosaoneka.” Nkhaniyi idzakhala ndi mbali zakuti: “Nyanga Khumi . . . Zidzadana Naye Mkazi Wachiwerewere,” “Mitundu Idzadziwa Yehova,” “‘Maufumu Onse’ Adzaphwanyidwa,” “Mdyerekezi ‘Adzamangidwa Zaka 1000,’” “Adzamanga Nyumba ndi Kulima Minda ya Mpesa,” “Mmbulu ndi Mwana wa Nkhosa . . . Zidzadyera Pamodzi,” “[Mulungu] Adzapukuta Msozi Uliwonse,” “Onse Ali M’manda a Chikumbutso Adzatuluka,” ndi “Mulungu Adzakhala ‘Zinthu Zonse kwa Aliyense.’” Chigawo cha m’mawa chidzatha ndi nkhani ya mutu wakuti “Kodi Mungatani Kuti Mudzapulumuke Mapeto a Dzikoli?”

Lamlungu masana kudzakhala sewero losangalatsa la mutu wakuti “M’bale Wakoyu Anali Wakufa Ndipo Tsopano Ali ndi Moyo,” yochokera pa fanizo la Yesu la mwana wolowerera. Kenako padzabwera chidule cha phunziro la mlungu ndi mlungu la Nsanja ya Olonda. Ndiyeno msonkhanowu udzatha ndi nkhani yakuti “Khalani Maso Poyembekezera Tsiku la Yehova.”

Yambani kukonzekera kuti mudzapezekeko. Kuti mudziwe malo amene kudzachitikire msonkhano wa pafupi ndi kwanuko, kafunseni ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kapena lemberani kalata ofalitsa a magazini ino. M’madera ena mudzachitikira msonkhano wa mayiko wa masiku anayi. Nsanja ya Olonda ya March 1, yomwenso imafalitsidwa ndi Mboni za Yehova ili ndi ndandanda ya malo amene kudzachitikire msonkhanowu m’madera osiyanasiyana.