Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Moyo wa Munthu Umayamba Liti?

Kodi Moyo wa Munthu Umayamba Liti?

Kodi Moyo wa Munthu Umayamba Liti?

“MTSIKANA wina, dzina lake Gianna, anati: “Pamene mayi anga anali ndi zaka 17 n’kuti ali ndi pakati pa miyezi 7 ndi theka, ndipo anaganiza zochotsa mimbayo pogwiritsa ntchito mankhwala enaake. * Mwana amene ankafuna kuchotsayo ndi ineyo. Sindinafe, ndinapulumuka.”

Gianna, anapereka umboni umenewu m’bwalo la milandu la ku America mu 1996. Panthawiyi n’kuti ali ndi zaka 19. Nthawi yomwe Gianna anali ndi miyezi 7 ndi theka m’mimba mwa mayi ake n’kuti ali ndi ziwalo zonse. Apa mungaone kuti panthawiyi Gianna anali munthu ndithu, chifukwa anapitirizabe kukhala ndi moyo mpaka kukula.

Nanga bwanji nthawi yomwe Gianna anali ndi milungu isanu yokha m’mimba mwa mayi ake? N’zoona kuti ziwalo za thupi lake zinali zisanathe kupangidwa, koma ubongo wake unali utapangidwa. Mtima wake unali utayamba kugwira ntchito moti pa mphindi imodzi unkagunda ka 80, zomwe zinkathandiza kuti magazi aziyenda bwino m’thupi mwake. Choncho, ngati Gianna anali munthu ndithu ali ndi miyezi 7 ndi theka m’mimba mwa mayi ake, kodi sitinganenenso kuti anali munthu ali ndi milungu isanu, ngakhale kuti ziwalo zina zinali zisanakule?

Khanda Limakula Modabwitsa

Kukula kwa khanda kumayamba pamene dzira la mayi likumana ndi umuna. Pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono, masiku ano asayansi amatha kuona mmene mwana akukulira m’mimba mwa mayi ake kuyambira pa selo limodzi limene limayamba dzira ndi umuna zikakumana. Panthawi imeneyi, zinthu zimene zimapanga DNA ya bambo komanso mayi zimaphatikizana ndipo munthu watsopano amayamba kupangika.

Mu DNA ndi m’mene mumakhala malangizo a mmene munthu adzaonekere. Malangizo onse okhudza kutalika, nkhope, maso, tsitsi ndi ziwalo zonse amakhala m’menemo.

Kenako selo loyamba lija limagawanika n’kupanga maselo osiyanasiyana. Selo lililonse limakhala ndi malangizo ake. Malangizowo amachititsa maselo ena kuti akhale mtima, ubongo, fupa, khungu kapena maso. N’zodabwitsa kwambiri ndipo n’zovuta kumvetsa mmene selo loyamba limasinthira n’kupanga maselo osiyanasiyana.

Wasayansi wina wotchuka, dzina lake Dr. David Fu-Chi Mark, anati: “Selo loyamba limakhala ndi malangizo onse a mmene munthuyo adzaonekere kuyambira ali mwana mpaka kukula. Sitingakayikire ngakhale pang’ono kuti munthu aliyense amasiyana kwambiri ndi munthu wina kuyambira pamene anangoyamba kupangika m’mimba.”

Mwana Wosabadwa Ndi Munthu Ndithu

Kungoyambira nthawi yomwe mayi watenga pakati, mwanayo sakhala ngati chiwalo china cha mayiyo, koma amakhala munthu payekha. Thupi la mayiyo limadziwa kuti lanyamula chinthu chatsopano, moti zikanakhala kuti mwanayo satetezedwa mwapadera, bwenzi thupi la mayiyo likukana kuti mwanayo akhalebe m’mimbamo. Choncho, mwanayo amakhala munthu payekha chifukwa amakhala ndi DNA yakeyake yosiyana ndi ya mayiyo.

Anthu ena amanena kuti popeza kuti mayi amatha kupita padera, sikungakhale kulakwa kuchotsa mimba. Koma dziwani kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa kupita padera ndi kupha khanda mwadala. Mwachitsanzo, m’dziko lina la ku South America, ana 71 mwa ana 1,000 aliwonse amamwalira asanakwanitse chaka chimodzi. Koma kodi zingakhale zoyenera kupha mwana wosakwanitsa chaka chimodzi chifukwa chakuti ana ena otere amamwalira chaka ndi chaka? Ayi, si zoyenera.

N’zochititsa chidwi kuti Baibulo limafotokoza kuti mwana wosabadwa ndi munthu ndithu. Davide analemba kuti: “Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu.” (Sal. 139:16) Davide sanangonena kuti “ndisanaumbidwe,” koma iye anati “ndisanaumbidwe INE.” Zimenezi zikusonyeza kuti moyo wa Davide unayamba mayi ake atangotenga pakati. Mouziridwa ndi Mulungu, Davide analembanso kuti mayi ake atatenga pakati, ziwalo zake zinalembedwa, kapena kuti zimakula motsatira malangizo amene anachititsa kuti iye azioneka mmene ankaonekeramo.

Baibulo limanenanso kuti: “Waima naye mwana.” (Yobu 3:3) Zimene zikusonyezanso kuti panthawi imene mayi watenga pakati, amatenga munthu, osati chinthu chinachake chosadziwika bwino m’mimba mwake. Choncho, nthawi imeneyi ndi pamene moyo wa munthu umayamba.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mankhwala amenewa amawapopera m’chiberekero ndipo mwana wosabadwayo akawamwa amafa, nthawi zambiri pasanapite maola awiri. Ndiyeno pakapita maola 24, mayiyo amabereka mwana wakufa, kapena mwana amene watsala pang’ono kufa.

[Zithunzi pamasamba 6, 7]

Khanda la milungu isanu, limakhala ndi malangizo a mmene ziwalo zake zonse zikulire

(kukula kwake kwenikweni)