Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muyenera Kuopa Anthu Akufa?

Kodi Muyenera Kuopa Anthu Akufa?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Muyenera Kuopa Anthu Akufa?

Anthu a mtundu wa Annang ku Nigeria amakhulupirira kuti munthu amene wafa akapanda kulemekezedwa poikidwa m’manda, munthuyo amatha kuvutitsa kapena kupha achibale. Anthu enanso a ku China amakhulupirira kuti ngati satsatira miyambo yawo poika munthu m’manda, munthu wakufayo amavutitsa anthu amoyo, ngakhale kuwapha kumene.

ANTHU ambiri padziko lonse amakhulupirira kuti munthu akafa, amakakhala ndi moyo kwinakwake. Ndipo ambiri amakhulupiriranso kuti munthuyo amatha kuthandiza kapena kuvutitsa achibale kapena anzake.

Koma kodi n’zoona kuti munthu akafa, amakakhala ndi moyo kwinakwake? Ndipo kodi iye angavutitse anthu amoyo? Kodi Baibulo limati chiyani pankhani imeneyi?

Kodi Akufa Amadziwa Chilichonse?

Baibulo limanena kuti akufa “sadziwa kanthu bi.” Limanenanso kuti ‘sakhalanso ndi moyo.’ (Mlaliki 9:5; Yesaya 26:14) Pofotokoza zimene zimachitika munthu akafa, Baibulo silinena zinthu zovuta kumva. Limanena kuti akufa ‘akugona tulo ta imfa.’ (Salmo 13:3) Nthawi ina Yesu ananena za mtsikana wa zaka 12 kuti: “Sanamwalire ayi, koma akugona.” Koma anthu “anayamba kumuseka monyodola, chifukwa anali kudziwa kuti wamwalira.” Koma Baibulo limafotokoza kuti Yesu anadzutsa mtsikanayo ku tulo ta imfa.—Luka 8:51-54.

Chimodzimodzinso Lazaro atafa, Yesu anauza ophunzira ake kuti akupita kwa Lazaroyo “kukam’dzutsa ku tulo take.” Ophunzira ake sanamvetse zimene iye ankatanthauza, choncho “Yesu tsopano anawauza mosapita m’mbali kuti: ‘Lazaro wamwalira.’” Mtumwi Paulo ananenanso za anthu amene ‘akugona mu imfa’ kuti panthawi imene Mulungu adzafune, adzaukitsidwa.—Yohane 11:11-14; 1 Atesalonika 4:13-15.

Baibulo silinena kuti munthu akamwalira amakakhalabe ndi moyo kwinakwake. Choncho palibe chifukwa choopera anthu akufa. Nanga n’chiyani chimachititsa anthu ambiri kukhulupirira kuti munthu akafa amakakhala ndi moyo kwinakwake?

Bodza Ndiponso Chinyengo

Zipembedzo zonyenga ndi zimene zimaphunzitsa kuti munthu akafa amakakhalabe ndi moyo kwinakwake. Chiphunzitso chimenechi chinayamba kale kwambiri ndipo chinali chofala kalelo. N’chifukwa chake olamulira ena akamwalira, monga mafumu a ku Iguputo, akapolo awo ankaphedwa kuti azikawatumikira kumene akupitako.

Anthu ambiri amakhulupirira kuti mizimu ya akufa imawavutitsa. Iwo amati, mizimu imeneyi ndi ya achibale awo amene anamwalira ndipo imachita zimenezi akaikwiyitsa. Koma Malemba amasonyeza kuti zimenezi si zoona. Mizimu yosaoneka imene imatchedwa ziwanda ndi yomwe imavutitsa ndi kuopseza anthu.—Luka 9:37-43; Aefeso 6:11, 12.

Malemba amanenanso kuti Satana ndi “tate wake wa bodza,” ndipo “amadzisandutsa mngelo wa kuwala.” Iyeyo ndiponso ziwanda zake “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Yohane 8:44; 2 Akorinto 11:14; Chivumbulutso 12:9) Choncho, Satana ndi amene amachititsa anthu kukhulupirira kuti munthu akafa amakakhala ndi moyo kwinakwake n’kumavutitsa anthu amoyo.

Koma anthu amene amakhulupirira Baibulo amadziwa kuti limeneli ndi bodza. Iwo amadziwanso kuti Satana ndi amene amanyenga anthu ndi kuwachititsa kukhulupirira kuti anthu akufa angathe kulankhula ndi amoyo. Amakhulupiriranso zimene Baibulo limanena kuti: “Amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) M’Mawu a Mulungu timapezamo choonadi chimene chingatimasule ku bodza la Satana lonena za anthu akufa.—Yohane 8:32.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi akufa amadziwa chilichonse?—Mlaliki 9:5; Yesaya 26:14.

▪ Kodi n’chiyani chimachititsa kuti anthu azikhulupirira kuti munthu akamwalira amakakhala ndi moyo kwinakwake?—Yohane 8:44.

▪ Kodi ndi kuti kumene tingapeze choonadi cha zimene zimachitika munthu akafa?—Yohane 8:32; 17:17.

[Mawu Otsindika patsamba 23]

Anthu amoyo amavutitsidwa ndi ziwanda, osati ndi anthu akufa