Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchotsa Mimba Si njira yabwino

Kuchotsa Mimba Si njira yabwino

Kuchotsa Mimba Si njira yabwino

BILL anakula akukhulupirira kuti kuchotsa mimba ndi tchimo lalikulu lofanana ndi kupha munthu. Koma maganizo amenewa anasintha m’chaka cha 1975 pamene iye anapereka mimba kwa mtsikana yemwe anali naye pachibwenzi, dzina lake Victoria. Panthawiyo Bill anali asanakonzekere kukwatira ndiponso kusamalira mwana. Iye anati: “Nthawi yomweyo ndinaganizira za njira yachidule. Ndinauza Victoria kuti angochotsa mimbayo.”

Kuchotsa mimba, komwe Bill anaganiza kuti ndi njira yachidule, n’kofala masiku ano. M’chaka cha 2007, lipoti lina linanena kuti m’chaka cha 2003, anthu 42 miliyoni padziko lonse anachotsa mimba. Akazi amene amachotsa mimba amakhala ochokera m’mayiko osiyanasiyana, zipembedzo zosiyanasiyana, olemera kapena osauka, ophunzira kapena osaphunzira, ndiponso a zaka zosiyanasiyana. Kodi inuyo mungatani mutatenga mimba yosakonzekera? Kodi n’chifukwa chiyani ambiri amaganiza zongochotsa mimba?

‘Sindikanachitira Mwina’

Mayi wina wazaka 35 anati: “Ndinavutika kwambiri ndi mimba komanso kubadwa kwa mwana, ndipo tinali ndi mavuto a zachuma komanso tinkavutika kusamalira banja. Patangopita masabata 6 mwana wathu atabadwa, ndinakhalanso ndi mimba ina. Choncho tinaganiza zongochotsa mimbayo. Ndinkadziwa kuti kuchita zimenezi n’kulakwa, koma sindikanachitira mwina.”

Akazi ambiri amachotsa mimba pazifukwa zosiyanasiyana. Zifukwa zina ndi mavuto azachuma ndiponso kusayenda bwino kwa banja, kumene kumapangitsa kuti mkaziyo asafunenso kukhala ndi mwamuna amene wapereka mimbayo. Enanso amaganiza zochotsa mimba ngati mkazi kapena onse awiri sanakonzekere mimbayo.

Nthawi zina, anthu amachotsa mimba chifukwa choopa kuchita manyazi. Dr. Susan Wicklund analemba nkhani yotereyi m’buku lake lonena za kuchotsa mimba. (This Common Secret—My Journey as an Abortion Doctor) Wodwala wina amene anabwera kwa iye kuti achotse mimba anamuuza kuti: “Makolo anga ndi anthu opemphera kwambiri. . . . Choncho ngati nditakhala ndi mwana wapathengo, ndingawachititse manyazi kwambiri. Anzawo onse angaone kuti mwana wawo wachita tchimo.”

Kenako Dr. Wicklund anamufunsa mtsikanayo kuti: “Ukunena kuti iwo angaone kuti wachita tchimo, koma kodi makolo akowo angamve bwanji utachotsa mimba?” Mtsikanayo anayankha kuti: “Kuchotsa mimba? Sangandikhululukire n’komwe. Koma kuchita zimenezi kuli bwinoko chifukwa anzawo a kutchalitchi sangadziwe.”

Munthu asanafike pochotsa mimba, amakhala atavutika maganizo. Ndiponso kuchotsa mimba kumabweretsa mavuto aakulu zedi.

Mavuto Ake

Kafukufuku wina amene anachitika m’chaka cha 2004, anasonyeza kuti amayi 331 a ku Russia ndiponso amayi 217 a ku America amene anachotsa mimba, anayamba kuona kuti alakwitsa. Pafupifupi theka la amayi a ku Russia ndiponso 80 peresenti ya amayi a ku America amenewo ankadziimba mlandu. Amayi a ku America oposa 60 peresenti ‘analephera kudzikhululukira.’ Popeza kuti anthu ambiri ochotsa mimba, ngakhale amene sapemphera, amadziimba mlandu, kodi n’chifukwa chiyani atsikana ambiri amachotsabe mimba?

Ambiri amachita zimenezi chifukwa makolo, mwamuna wawo kapena anzawo amawakakamiza. Iwo amati kuchotsa mimba yosakonzekera n’kwabwino kusiyana ndi kubereka. Zimenezi zingachititse kuti mtsikana achite zinthu mopupuluma. Koma Dr. Priscilla Coleman anati: “Atsikanawa akaganiza kwa nthawi yaitali kuti achotse mimba ndipo kenako n’kuchotsadi, amazindikira kuti alakwitsa kwambiri ndipo amadziimba mlandu komanso amamva chisoni.”

Amamva chisoni akazindikira kuti anapha munthu. Lipoti la bungwe lina lofufuza za nkhani imeneyi (South Dakota Task Force to Study Abortion) linanena kuti amayi ambiri omwe anachotsa mimba, “anatero chifukwa sankadziwa kuti kuchotsa mimba n’chimodzimodzi ndi kupha munthu, ndipo amati sakanachita zimenezi akanauzidwa zolondola.”

Ofufuzawa ataunika nkhani zomvetsa chisoni za amayi 1,940 amene anachotsa mimba, ananena kuti: “Ambiri mwa iwo anamva chisoni atazindikira kuti anapha mwana chifukwa chosauzidwa zolondola.” Ananenanso kuti amayiwa “amavutika kwambiri maganizo akaganizira kuti anapha mwana wawo.”

Kodi zoona zake n’zotani? Kodi kuchotsa mimba n’chimodzimodzidi ndi kupha munthu?

[Bokosi/Zithunzi patsamba 4]

NDI BWINO KUBEREKA M’MALO MOCHOTSA MIMBA

Mu 2006, akatswiri ena anachita kafukufuku wokhudza akazi amene anatenga pakati asanakwanitse zaka 20. Theka la iwo anabereka ndipo enawo anachotsa mimba. Akatswiriwa anapeza kuti “amene anaberekawo anali osangalalako, amagona tulo tabwinopo, ndipo ambiri sankasuta chamba kusiyana ndi amene anachotsa mimba.”—Journal of Youth and Adolescence.

Akatswiri enanso anafotokoza “zotsatira za kafukufuku amene anachitika padziko lonse.” Ndipo iwo anapeza kuti “akazi amene anachotsa mimba ankavutika maganizo kwambiri kusiyana ndi amene sanachotse mimbawo.”—Report of the South Dakota Task Force to Study Abortion—2005.