Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinamasulira Mabuku Mobisa kwa Zaka 30

Ndinamasulira Mabuku Mobisa kwa Zaka 30

Ndinamasulira Mabuku Mobisa kwa Zaka 30

Yosimbidwa ndi Ona Mockutė

Mu April 1962, ndinapezeka m’khoti la mumzinda wa Klaipeda, ku Lithuania, kukayankha milandu yosokoneza anthu. Izi zisanachitike, mu October 1961, ndinamangidwa ndiponso kuimbidwa mlandu wochita zinthu zachipembedzo zotsutsana ndi boma la Soviet Union. Ndikufuna ndikufotokozereni chimene chinachititsa kuti andigwire n’kunditsekera m’ndende panthawi imene ndinkamasulira mabuku a Mboni za Yehova.

NDINABADWA m’chaka cha 1930, kumadzulo kwa dziko la Lithuania, pafupi ndi nyanja ya Baltic. Mayi anga ali ndi pakati pa ineyo, ankapemphera kuti ndikadzabadwa n’kukula, ndidzakhale sisitere. Koma panthawi ina anandiuza kuti: “Sindingapempherenso kwa Petulo Woyera kapena mafano ena opanda moyo.” Chifukwa chokumbukira zimenezi ndinkapewa kugwadira mafano m’tchalitchi, ngakhale kuti ndikamapita kusukulu ndinkapempherera korona.

Kenako ndinaona anthu akuchitiridwa nkhanza zosaneneka panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, yomwe inayamba mu 1939 n’kutha mu 1945. Zimenezi zinandikhudza kwambiri. Tsiku lina ine ndi mayi anga aang’ono tikuthyola zipatso m’tchire, tinaona maenje awiri akuluakulu opakikapakika magazi. Panthawiyi n’kuti dziko la Germany litalanda dziko la Lithuania. Nditakumbukira kuti Ayuda ambiri, kuphatikizapo anzanga a kusukulu Tese ndi Sara, aphedwa, tinazindikira kuti iwo aponyedwa m’maenjewo. Ndinanena mwachisoni kuti: “Mulungu, ndikudziwa kuti ndinu wabwino. Nanga n’chifukwa chiyani mumalola kuti zinthu zoipa chonchi zizichitika?”

Mu 1949, ndinamaliza maphunziro anga a ku sekondale mumzinda wa Klaipeda, pafupi ndi kunyumba kwathu. Kenako ndinayamba maphunziro a zoimbaimba. Mu 1950, ndinalowa m’gulu la ana a sukulu amene ankafuna kuti zinthu zisinthe pandale, koma pasanapite nthawi ndinaululidwa ndipo ndinamangidwa pamodzi ndi anzanga 12. Ndinatsekeredwa m’ndende ya ku Klaipeda ndipo ndili kumeneko, ndinakumana koyamba ndi munthu wa Mboni za Yehova.

Ndinaphunzira Choonadi

Mayi wina wachitsikana anaponyedwa m’ndende imene munali ineyo ndi atsikana ena 6. Atationa anatimwetulira. Ndinamufunsa kuti: “M’bale wanga, anthu akawaponya muno amalowa ataipitsa nkhope. Kodi n’chifukwa chiyani iweyo ukumwetulira? Kodi walakwa chiyani kuti upezeke muno?”

Iye anandiyankha kuti: “Ndapezeka muno chifukwa cha choonadi.”

Ndinamufunsa kuti: “Kodi choonadi n’chiyani?”

Mayiyu dzina lake linali Lydia Peldszus, ndipo anali wa ku Germany. Iye anamangidwa chifukwa chakuti anali wa Mboni za Yehova. Tinakambirana zambiri za Mulungu. Tili m’ndende, Lydia anatiphunzitsa choonadi cha m’Baibulo chimene chinasintha moyo wanga komanso wa anzanga ena atatu.

Ndinadziwa Zambiri za M’Baibulo

Chifukwa chakuti ndinali m’gulu la ndale lolimbana ndi boma la Soviet Union, ndinalamulidwa kuti ndikhale m’ndende kwa zaka 25 ndiponso zaka zisanu kunja kwa dziko la Lithuania. Ndinadziwa zambiri za m’Baibulo chifukwa chokumana ndi a Mboni za Yehova kundendeko komanso kumalo osiyanasiyana komwe akaidi ankakagwira ntchito ku Siberia. Mofanana ndi Lydia, a Mboni za Yehova amenewa anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo.

Pazaka zomwe ndinali kundende, ndinadziwa zambiri za m’Baibulo komanso ndinkauza ena za chikhulupiro changa. Ngakhale kuti ndinalibe mwayi wobatizidwa posonyeza kuti ndadzipereka kwa Mulungu, akaidi ena komanso oyang’anira ndende ankaona kuti ndine wa Mboni za Yehova. Mu 1958, ndinatulutsidwa m’ndende nditakhalamo zaka 8. Ndinabwerera ku Lithuania ndikudwala, komabe ndinkakhulupirira kwambiri Yehova.

Ndinayamba Kumasulira Mabuku Mobisa

Panthawi imeneyo ku Lithuania kunali a Mboni ochepa. Ndipo ena anali m’ndende komanso ena anathawira ku Siberia. Mu 1959, a Mboni za Yehova awiri anabwera kuchokera ku Siberia ndipo anandipempha kuti ndiyambe kumasulira mabuku onena za m’Baibulo m’Chilituweniya. Ndinavomera kugwira ntchito imeneyi, ndipo ndinkaona kuti ndi mwayi waukulu.

Mwezi wa March 1960, ndinayamba ntchito yomasulira mabuku, ndipo mu July, ndinabatizidwa mobisa mu mtsinje wa Dubysa. Gulu la chitetezo la boma la Soviet Union, lomwe linkadziwika kuti KGB, silinkafuna Mboni za Yehova. Choncho zinali zovuta kuti ndipeze ntchito. Chifukwa cha zimenezi, ndinkakhala ndi makolo anga omwe sankadana ndi chipembedzo changa. Ndinkaweta ng’ombe za bambo anga ndiponso za anthu omwe tinayandikana nawo nyumba. Poweta ng’ombezo, ndinkagwiranso ntchito yomasulira mabuku. Ndinali ndi ofesi yokongola kwambiri. Mpando wake unali chitsa ndipo kapeti yake inali udzu wobiriwira. Denga lake linali mtambo wa buluu, ndipo desiki lake linali bondo.

Koma m’kupita kwa nthawi, ndinaona kuti kugwira ntchito yomasulira pamalo oonekera amenewa kunali koopsa chifukwa gulu la KGB kapena akazitape ena, akanandiona. Choncho nditapeza malo obisika ogwirira ntchitoyi, ndinachoka kunyumba ya bambo anga. Nthawi zambiri pomasulira ndinkakhala m’nyumba yosungira zakudya za ziweto pafupi ndi khola.

Ndinkagwira ntchito masana okhaokha chifukwa panalibe magetsi. Kuti ndisamamveke phokoso ndikamatayipa, pafupi ndi nyumba yosungira zakudya za ziwetoyi tinaika makina oyendera mphepo amene ankachitanso phokoso. Kukada, ndinkapita m’nyumba kukadya chakudya chamadzulo ndipo kenako ndinkabwerera kunyumba yosungira zakudya za ziwetoyi ndipo ndinkagona pa zakudya za ziwetozo.

Mu October 1961, ineyo pamodzi ndi a Mboni ena awiri tinamangidwa chifukwa cha ntchitoyi. Zimenezi ndi zomwe zinachititsa kuti ndipezeke kukhoti mu 1962, monga mmene ndafotokozera poyamba paja. Akuluakulu a khoti analola kuti aliyense adzamvetsere mlandu wathu, ndipo tinasangalala kwambiri kudziwa kuti anthu ambiri adzamva zimene timakhulupirira. (Maliko 13:9) Ndinalamulidwa kuti ndikhale m’ndende zaka zitatu ndipo ndinatumizidwa ku ndende ya Tallinn, ku Estonia. Malinga ndi mmene ndikudziwira, ine ndekha ndi amene ndinatsekeredwa kundendeyi chifukwa cha chipembedzo changa. Akuluakulu a boma ankabwera kudzandiona, ndipo ndinkawauza zimene ndimakhulupirira.

Ndinayambanso Ntchito Yomasulira

Nditatuluka m’ndende ya ku Estonia mu 1964, ndinabwerera ku Lithuania. Kumeneko ndinapitiriza ntchito yomasulira mabuku. Kwenikweni ndinkamasulira kuchoka m’Chirasha kupita m’Chilituweniya. Ndinali ndi ntchito yambiri zedi. Ngakhale kuti ena ankandithandiza, ineyo ndi amene ndinkagwira ntchito yomasulira masiku onse. Nthawi zambiri ndinkagwira ntchito masiku 7 mlungu uliwonse, kuyambira m’mawa mpaka madzulo. Sindikanakwanitsa kuchita zimenezi popanda Yehova kundithandiza.

Popeza kuti ntchito imene ndinkagwira inali yofunika kwambiri, nthawi zonse ndinkachita zinthu mosamala. Abale ndi alongo achikhristu ankaika moyo wawo ndi wa banja lawo pachiswe, kuti andibise, andipatse chakudya komanso kuti anditeteze. Zimenezi zinathandiza kuti tizigwirizana kwambiri. Ndikamagwira ntchito, banja limene ndinkakhala nalo linkakhala tcheru kuti lione munthu amene akubwera yemwe angakandineneze. Akaona munthu akubwera, ankamenya mapaipi enaake kawiri ndi chitsulo. Ndikamva phokosolo, msangamsanga ndinkabisa chilichonse chomwe chingatigwiritse.

Anthu akayamba kutitulukira, msangamsanga tinkasamukira kumalo ena. Nthawi imeneyo kukhala ndi makina olembera popanda chilolezo unali mlandu waukulu, choncho munthu wina ankandinyamulira makinawo kuwapititsa kumalo atsopanowo. Ndipo ineyo ndinkasamukira ku malowo usiku.

Kunena zoona, Yehova ankanditeteza. Akuluakulu a boma ankadziwa zimene ndinkachita ngakhale kuti analibe umboni uliwonse. Mwachitsanzo, mu 1973, a Mboni za Yehova ena 8 akuimbidwa mlandu, woimira boma pa mlanduwo anandiitana kuti akandifunse mafunso. Iye anandifunsa kuti, “Mockutė, wamasulira mabuku ochuluka bwanji zaka zonsezi?”

Ndinamuuza kuti sindingayankhe funso limenelo. Iye anandifunsanso kuti, “Ungayankhe funso lotani?”

Ndinamuuza kuti, “Ndingayankhe funso lililonse losakhudzana ndi ntchito imeneyi.”

Zinthu Zinayamba Kusintha

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1980, zinthu zinayamba kusintha ku Lithuania. Tinaleka kuchita zinthu mobisa chifukwa choopa boma. Choncho mu 1990, anthu ena anayamba kugwira ntchito yomasulira mabuku. Pa September 1, 1992, ofesi yomasulira mabuku inatsegulidwa ku Klaipeda, ndipo ine ndinakhazikika mumzinda umenewu.

Ndinagwira ntchito yomasulira mabuku kwa zaka 30, m’madera 16 osiyanasiyana. Panthawi yonseyi ndinalibe nyumba yangayanga. Koma ndikusangalala kwambiri kuona kuti ntchitoyi yabala zipatso. Panopa ku Lithuania kuli Mboni za Yehova zokwana 3,000. Ndipo ntchito yomasulira mabuku imene ndinkachita mobisa, panopa ikuchitikira pa ofesi ya nthambi yokongola kwambiri, yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Kaunas.

Ndimakumbukirabe nthawi yomwe ndinakumana ndi wa Mboni za Yehova m’ndende yozizira ya ku Klaipeda pafupifupi zaka 60 zapitazo. Zimene tinakambirana zinasintha moyo wanga. Ndikuthokoza kwambiri Mlengi Wamkulu, Yehova, chifukwa chondithandiza kumudziwa ndiponso kudziwa zolinga zake. Ndimanyadiranso kuti ndinadzipereka kuchita chifuniro chake.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

Tili m’ndende, Lydia anatiphunzitsa choonadi cha m’Baibulo chimene chinasintha moyo wanga komanso wa anzanga ena atatu

[Chithunzi patsamba 12]

Nkhani ya mlandu wanga inalembedwa m’nyuzipepala ya ku Soviet Union mu 1962

[Chithunzi pamasamba 14, 15]

Mabuku ena onena za Baibulo amene ndinamasulira mobisa

[Chithunzi patsamba 15]

Lydia anandiphunzitsa choonadi cha m’Baibulo kundende

[Chithunzi patsamba 15]

Anthu awiri a Mboni (kumanzere) anandiphunzitsa zambiri za Mulungu kundende ya ku Khabarovsk, ku Russia, mu 1956

[Chithunzi patsamba 15]

Makina olembera amene ndinkagwiritsa ntchito nthawi imene ntchito yathu inali yoletsedwa