Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

▪ “Tikukumana ndi mavuto aakulu [a ndale ku Georgia] . . . Mulungu ali nafe ndiponso Virigo Mariya akutiteteza, koma chinthu chimodzi chomwe chikutidetsa nkhawa kwambiri n’chakuti, Akhristu a ku Russia akupha Akhristu a ku Georgia.”—GEORGIAN CATHOLICOS PATRIARCH ILLIA II.

▪ “Chiwerengero cha anthu amene amapita kuchipatala kukafuna mankhwala olera atagonana kale, chawonjezereka katatu m’miyezi 6 yapitayi. Ndipo kuyambira 2004 chiwerengero cha mankhwala amene agulitsidwa chawonjezereka ndi 200 peresenti . . . Anthu ambiri amaimba foni Lolemba kuti afunse za mankhwalawa. Ndipo ambiri mwa anthuwa ndi achinyamata.”—CLARÍN, ARGENTINA.

▪ Mwana aliyense wa zaka za pakati pa 13 ndi 17 ku America amene ali ndi foni yam’manja, “anatumiza kapena kulandira mauthenga okwana 1,742 pamwezi m’chaka cha 2008 m’miyezi ya April, May, ndi June.—THE NEW YORK TIMES, U.S.A.

▪ “Pafupifupi anthu 12 mwa anthu 100 aliwonse padziko lonse amadwala matenda okhudza ubongo.”—WORLD FEDERATION FOR MENTAL HEALTH, U.S.A.

▪ Pafupifupi munthu mmodzi pa anthu asanu aliwonse ku Ulaya, anasutapo chamba.”—EUROPEAN MONITORING CENTRE FOR DRUGS AND DRUG ADDICTION, PORTUGAL.

Akatswiri Anapeza Dzina Lotchulidwa M’Baibulo

Pamene akatswiri a zinthu zakale anafukula malo amene panali Mudzi wa Davide ku Yerusalemu, anapeza chidindo chadothi chokhala ndi dzina lakuti “Gedaliya mwana wa Pusuri.” Chidindochi chinapangidwa zaka 2,600 zapitazo. Dzina la Gedaliya limapezeka m’Baibulo pa Yeremiya 38:1. Palembali palinso dzina lakuti “Yukali [chidule cha Yehukali] mwana wa Selemiya,” lomwe linapezeka pamalo omwewa m’chaka cha 2005. Anthu awiriwa anali nduna za m’nyumba ya mfumu Zedekiya. Nyuzipepala ya The Jerusalem Post inati: “Imeneyi inali nthawi yoyamba m’mbiri ya Isiraeli kuti zidindo ziwiri zokhala ndi mayina awiri a m’Baibulo amene amapezeka pavesi limodzi afukulidwe m’dera limodzi.”

Foni za M’manja Zikuthandiza Pogwira Akuba

Apolisi a ku New York amalandira mafoni ambiri kuchokera kwa anthu a mumzindawo owadziwitsa za akuba. Foni zapamwamba zimene zikupangidwa panopa, zikuthandiza kuti anthu azitumizira apolisi mauthenga a pafoni. Nyuzipepala ya New York Times inati: “Anthu a mumzindawu tsopano akulimbikitsidwa kujambula zithunzi za anthu akuba panthawi imene akuba, n’kuzitumiza kupolisi.” Nyuzipepalayi inanenanso kuti, boma likukonza zoti “apolisi akhale ndi malo olandirirako zithunzizi n’kumazitumiza kwa apolisi amene amayendayenda pagalimoto m’madera osiyanasiyana.”

Mbalame Zimene Zimatha Kudziona Pagalasi

Nyuzipepala ya Reuters inati: “Poyamba anthu ankaganiza kuti anyani akuluakulu, nsomba za dolphin ndiponso njovu zokha ndi zimene zimatha kudziona pagalasi.” Panopa akuti pali mbalame zinazake zotchedwa magpies zimene zimathanso kudziona pagalasi. Akatswiri ena anapaka mbalamezi penti pamalo amene zikanatha kuona pagalasi pokha basi. Akatswiriwa anati: “Mbalamezi zinkadzikandakanda pamalo pamene panali pentipo kusonyeza kuti zinkadziwa kuti zithunzi zomwe zinali pagalasipo zinali zawo.”