Kanyama Kaulesi
Kanyama Kaulesi
TSIKU lina tikuyenda m’thengo, ndinangoona kanyama kenakake kobiriwira. Nthawi yomweyo ndinaitana mlongo wanga n’kumuuza kuti: “Fulumira, tabweretsa kamera.” Koma tinaseka kwambiri titazindikira kuti panalibe chifukwa chothamangira. Kanyamaka kamayenda pang’onopang’ono ndipo n’kamodzi ka nyama zaulesi kwambiri padziko lonse.
Kuti ndidziwe zambiri za kanyamaka, ndinapita kumalo usungirako nyama otchedwa Zoo Ave, ku Alajuela, m’dziko la Costa Rica. Kumaloku amasamalirako nyama zimene zavulala ndipo kenako amazibwezeranso m’thengo. Ndili kumeneku, ndinakumana ndi mayi Shirley Ramírez, yemwe ndi mkulu wofufuza za nyama kumaloku. Iye anakandionetsa kanyama kofanana ndi kamene ndinaona kaja, komwe anakapatsa dzina la Chisipanishi lakuti Pelota. Dzinali limatanthauza “mpira.” Mwina kanyamaka anakapatsa dzina limeneli chifukwa chakuti, pogona kamadzipinda kwambiri n’kumaoneka ngati mpira. Pelota ali ndi zala ziwiri kumwendo uliwonse ndipo ndi wamkulu ngati kamwana ka galu. Alinso ndi ubweya wosalala, mphuno yaifupi yoyang’ana m’mwamba, ndiponso maso akuluakulu abulauni.
Nditafufuza ndinapeza kuti kanyamaka kamakonda kukhala kokha ndipo kamabereka mwana mmodzi chaka chilichonse. Kamwanako kamadziphatika ku mimba ya mayi ake kwa milungu 4 kapena 6 yoyambirira mpaka katasiya kuyamwa. Ngakhale kasiye kuyamwa, amakaberekabe kwa miyezi 5 kapena 8. Panthawi imeneyi mayiyo amakadyetsa kamwanako masamba ofewa a mitengo. Kenako kamwanako kamathyola kokha masamba a mitengo katanyamulidwa ndi mayi ake. Panthawiyinso mayiyo amayenda ndi kamwanaka m’malo osiyanasiyana a m’nkhalango kuti kawazolowere.
Tilipo Tamitundumitundu
Kanyama kamene ndinakaona kaja kanali ndi zala zitatu kumwendo uliwonse. Kanali kakuda kumaso kwake, kanali ndi mchira waufupi, ubweya wambiri, miyendo yake ya kutsogolo inali yaitali kuposa yakumbuyo, komanso kanali ndi mawanga achikasu m’mapewa ake. Kanyama kotere kamakhala ndi mafupa 9 pakhosi pake, zimene zimathandiza kuti kazitha kupinda mutu wake kwambiri kakamathyola masamba, omwe ndi chakudya chimene kamachikonda kwambiri. Kodi n’chifukwa chiyani kamaoneka kobiriwira? Shirley anandiuza kuti, “Kamaoneka kobiriwira chifukwa chakuti ubweya wake umamera ndere.”
Kanyama kena ka mtunduwu kamakhala ndi zala ziwiri kumwendo uliwonse. Ndipo miyendo yake yonse, yakutsogolo ndiponso kumbuyo, imakhala yofanana kutalika kwake. Ubweya wake ndi wautali, wooneka wagolide, komanso wofewa kwambiri.
Nthawi zambiri kanyamaka kamakhala kunsonga kwa mitengo kuti kaziwothera dzuwa. Kutentha kwa thupi lake kumasinthasintha kwambiri, litha kuzizira kufika madigiri 24 kapena kutentha kwambiri kufika madigiri 33. Thupi la nyama zina silisintha kwambiri choncho. Kanyama kameneka kalibe mnofu wambiri ndipo n’chifukwa chake kamagona modzipinda kwambiri kuti kazimva kutentha. Komanso kali ndi ubweya wofewa, womwe umakathandizanso kuti kazimva kutentha. Kanyamaka n’kaulesi kwambiri moti patsiku kamagona maola 20.
Kamadya Pang’onopang’ono
Popeza kuti chakudya chimagayika bwino thupi likamatentha, chakudya chimene kanyamaka kamadya sichigayika msanga chifukwa chakuti thupi lake silitentha kwambiri. Chakudya chimatenga mwezi wathunthu kuti chigayike. M’nthawi yozizira, kanyama kameneka kakhoza kufa ndi njala ngakhale katakhala ndi zakudya m’mimba mwake. Shirley anati: “Kutentha kwa dzuwa kumathandiza kwambiri kuti chakudya chizigayika msanga m’thupi mwa kanyamaka.”
Shirley ananenanso kuti: “Ndimakonda kwambiri nyamazi chifukwa sizivuta kusamalira. Zimachita chimbudzi komanso kukodza kamodzi kokha pamlungu. Zikafuna kuchita chimbudzi, zimatsika mumtengo n’kukumba pansi, ndipo zikatha zimakwirira. Popanda zimenezi, nyamazi sizitsika mumtengo.”
Kamakhala Chagada
Pafupifupi zonse zimene kanyamaka kamachita, monga kudya, kugona, ndiponso kubereka, kamazichita kali chagada. Kanyama kameneka kanalengedwa modabwitsa kwambiri kuti kazikhala chagada nthawi zonse. Kamazendewera mitengo ndi zala zake, zomwe zimakhala zazitali masentimita 7. Ubweya wake umamera kuyambira pamimba kupita kumsana ndipo zimenezi zimathandiza kuti kasamanyowe kukamabwera mvula. Izi n’zosiyana kwambiri ndi mmene nyama zina zinalengedwera. Ngakhale kuti kanyamaka kamayenda mwaulesi kakakhala pansi, kakakhala mumtengo kamayenda monyada kwambiri. Komanso n’zodabwitsa kuti kanyama kameneka kamadziwa kusambira kwambiri.
Ndinaphunziranso zinthu ziwiri zokhudza kanyamaka. Choyamba, sikachedwa kuchira kakavulala ndiponso sikafa wamba kakadya zinthu zapoizoni. Ngakhale katakhala ndi bala lalikulu bwanji, balalo silichedwa kupola chifukwa sililowa tizilombo chisawawa. Choncho kudziwa mmene kanyamaka kamadzitetezera ku matenda kungathandize kwambiri akatswiri ofufuza zamankhwala. Chachiwiri, kanyamaka kamachita zinthu mofatsa, moti anthu amene amachita zinthu mopupuluma ndiponso mopanikizika, angachite bwino kutengera kanyamaka.—Nkhaniyi tachita kutumiziridwa.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 15]
KAMAMERA NDERE
Kanyamaka ndi kobiriwira chifukwa chakuti ubweya wake umamera ndere. Nderezo zimapeza malo okhala ndipo kanyamaka kamapezerapo mwayi wodya nderezo. Mtundu wobiriwira wa nderezo umachititsa kuti kanyamaka kasamaoneke kakakhala mumtengo chifukwa kamafanana ndi masamba. Ndipo kakamakula, m’pamenenso kamakhala kobiriwira kwambiri.
[Mawu a Chithunzi]
Top right: © Michael and Patricia Fogden; bottom: © Jan Ševčík