Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Matenda Ovutika Maganizo Ndi Otani?

Kodi Matenda Ovutika Maganizo Ndi Otani?

Kodi Matenda Ovutika Maganizo Ndi Otani?

JAMES * anati: “Tsiku lina m’mawa, ndili ndi zaka 12, ndinadzuka ndi kukhala pabedi ndipo ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi lero sindifa?’” James anali ndi matenda ovutika maganizo. Patapita zaka 30, iye anati: “Ndakhala ndikulimbana ndi matendawa tsiku lililonse.” James ali mwana ankadziona kuti ndi wosafunika moti tsiku lina anang’amba zithunzi zake. Iye anati: “Sindinkaona kuti zithunzi zimenezi n’zofunika kumazikumbukira.”

Popeza kuti tonsefe timakhumudwa nthawi zina, tingaganize kuti timawadziwa bwino matenda ovutika maganizo. Koma kodi matendawa ndi otani kwenikweni?

Matendawa Ndi Osautsa

Munthu akakhumudwa kwa nthawi yochepa sikuti akudwala matenda ovutika maganizo. Munthu amene ali ndi matendawa amakhumudwa pafupipafupi komanso kwa nthawi yaitali, ndipo nthawi zambiri amalephera kugwira ntchito zake za tsiku ndi tsiku.

Mwachitsanzo, Álvaro wakhala akudwala matenda ovutika maganizo kwa zaka zopitirira 40. Nthawi zambiri iye “amakhala ndi mantha, amasokonezeka maganizo, amamva ululu, ndiponso amakhala ndi chisoni chachikulu.” Iye anati: “Matenda ovutika maganizo ankandichititsa kuti ndizikhumudwa kwambiri ndi zimene ena anena. Ndipo nthawi zonse zinthu zikalakwika ndinkaona kuti vuto ndi ineyo.” Iye anafotokozanso kuti, munthu amene ali ndi matenda ovutika maganizo “amamva ululu kwambiri koma sadziwa chimene chikuchititsa, amachita mantha kwambiri koma sadziwa chimene chikumuchititsa mantha, ndipo vuto lalikulu ndi lakuti safuna ngakhale pang’ono kuuza ena zimenezi.” Panopa Álvaro anadziwa chimene chimayambitsa matendawa ndipo zimenezi zamuthandiza. Iye ananenanso kuti: “Kudziwa kuti anthu ena amavutikanso ndi matendawa kwandithandiza kupezako mpumulo.”

Mayi wina wa zaka 49 wa ku Brazil, dzina lake Maria, ankadwala matenda ovutika maganizo ndipo matendawa ankamuchititsa kuti azisowa tulo, azimva ululu, asamachedwe kukwiya, komanso kuti “azikhala wokhumudwa nthawi zonse.” Madokotala atamuyeza n’kumuuza vuto lake, Maria anasangalala kudziwa kuti matenda ake ndi odziwika bwino. Iye anati: “Komabe ndinayamba kuda nkhawa kwambiri chifukwa anthu ambiri sawadziwa matendawa ndipo munthu wodwala matendawa amamusala.”

Kodi Ndi Matenda Odetsa Nkhawa?

Ngakhale kuti nthawi zina chimene chimayambitsa matenda ovutika maganizo chimadziwika, nthawi zambiri matendawa amayamba mosayembekezereka. Richard wa ku South Africa, ananena kuti ukayamba kudwala matendawa, “umada nkhawa mosayembekezereka ndiponso popanda chifukwa chenicheni. Pamakhala kuti palibe wamwalira ndipo palibe chokhumudwitsa chilichonse chimene chachitika, koma umakhalabe wosasangalala. Ndipo umaona kuti palibe chingathetse vuto limeneli. Umakhala wokhumudwa kwambiri koma sudziwa chimene chikuchititsa.”

Matenda ovutika maganizo si ochititsa manyazi. Koma mtsikana wina wa ku Brazil, dzina lake Ana, anachita manyazi kwambiri atamupeza ndi matenda amenewa. Iye anati: “Ngakhale kuti patha zaka 8 chindipezereni ndi matendawa, ndimachitabe manyazi.” Iye amasowa mtendere chifukwa nthawi zonse amakhala wokhumudwa ndipo anati: “Nthawi zina vutoli limakula kwambiri moti ndimamva ululu waukulu. Thupi langa lonse limapweteka.” Zikatere, ngakhale kudzuka pabedi kumamuvuta. Ndipo nthawi zina Ana amangokhalira kulira. Iye anati: “Ndimalira kwambiri, ndimatopa kwambiri komanso ndimamva ngati magazi anga asiya kuyenda.”

Baibulo limanena kuti anthu angakhale ndi chisoni chachikulu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ankadera nkhawa munthu winawake kuti “angamezedwe kotheratu ndi chisoni chake chopitirira malire.” (2 Akorinto 2:7) Anthu ena amene ali ndi matenda ovutika maganizo amamva chisoni kwambiri moti amangofuna atafa. Ambiri amamva ngati mmene anamvera mneneri Yona, yemwe anati: “Kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ayi.”—Yona 4:3.

Kodi anthu amene akudwala matenda ovutika maganizo angatani kuti alimbane ndi vutoli?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Maina m’nkhanizi asinthidwa.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

“Umada nkhawa mosayembekezereka ndiponso popanda chifukwa chenicheni”