Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
Zinachitikira Kuti?
1. Kodi zinthu zotsatirazi zinachitikira mumzinda uti?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Machitidwe 2:1-13.
Pamapu awa lembani mzere wozungulira yankho lanu.
Atene
Yerusalemu
Babulo
▪ Kodi ophunzira ambiri a Yesu anali ochokera kuti?
․․․․․
▪ Kodi n’chifukwa chiyani anthu ena ankanyoza ophunzira a Yesu?
․․․․․
KAMBIRANANI:
Kodi nkhani imeneyi ikufanana ndiponso kusiyana bwanji ndi nkhani ya pa Genesis 11:1-9?
Kuchokera M’magazini Ino
Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowa.
TSAMBA 4 Kodi n’chiyani chingameze munthu? 2 Akorinto 2:․․․
TSAMBA 6 Kodi mtendere wa Mulungu ungakuthandizeni bwanji? Afilipi 4:․․․
TSAMBA 28 Kodi ena amene ali ndi changu cha kwa Mulungu amasowa chiyani? Aroma 10:․․․
TSAMBA 29 Kodi tiyenera kumvera ndani? Machitidwe 5:․․․
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
Kodi n’chiyani chimene mukudziwa chokhudza woweruza Otiniyeli?
Werengani Oweruza 3:7-11. Ndiyeno yankhani mafunso otsatirawa.
2. ․․․․․
Kodi anali wa fuko lanji?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Yoswa 15:17, 20.
3. ․․․․․
Kodi iye anapulumutsa Aisiraeli kwa wolamulira uti?
4. ․․․․․
Zoona kapena zonama? Iye anakhala ndi moyo Mose asanabadwe.
KAMBIRANANI:
Kodi Kalebe yemwe anali malume ake a Otiniyeli anasonyeza chitsanzo chabwino chotani?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Numeri 14:6-9. Tchulani dzina la wachibale wanu aliyense amene mumamusirira, ndipo fotokozani chifukwa chake.
▪ Mayankho ali pa tsamba 11
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
1. Yerusalemu.—Machitidwe 2:5.
▪ Galileya.—Machitidwe 2:7.
▪ Ankaganiza kuti aledzera.—Machitidwe 2:13.
2. Yuda.—Yoswa 15:17, 20.
3. Kusani-Risataimu—Oweruza 3:8.
4. Zonama.