Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ndimaopa Kuuza Ena za Chikhulupiriro Changa?

N’chifukwa Chiyani Ndimaopa Kuuza Ena za Chikhulupiriro Changa?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

N’chifukwa Chiyani Ndimaopa Kuuza Ena za Chikhulupiriro Changa?

“Nthawi zina kusukulu ndimakhala ndi mpata wofotokoza za chikhulupiriro changa. Koma sindimaugwiritsa ntchito.”—Anatero Kaleb. *

“Tsiku lina aphunzitsi anatifunsa kuti tifotokoze maganizo athu pankhani yakuti zinthu zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Ndinadziwa kuti umenewu ndi mwayi wabwino woti ndifotokoze chikhulupiriro changa. Koma ndinali ndi mantha kwambiri moti sindinafotokoze chilichonse. Kenako ndinaona kuti sindinachite bwino.”—Anatero Jasmine.

NGATI ndinu Mkhristu wachinyamata, mwina munakumanapo ndi zimene zinachitikira Kaleb ndi Jasmine. Mwina nanunso mumakonda choonadi cha m’Baibulo, ndipo mumafunitsitsa kuuza ena choonadicho. Koma mwina mumaopa kuchita zimenezi. Kodi mungatani kuti muzilimba mtima? Mukapita kusukulu, kayesetseni kugwiritsa ntchito mfundo zotsatirazi:

1. Lembani zimene mumaopa. Mukamachita mantha kuuza ena chikhulupiriro chanu, muziganizira zinthu zonse zimene anzanuwo angakuchitireni. Nthawi zina mantha anuwo angathe, ngati mutalemba chilichonse chimene mukuchita nacho mantha.

Malizani chiganizo chotsatirachi.

▪ Ngati ndingafotokozere ena za chikhulupiriro changa kusukulu, zingachitike ndi izi:

․․․․․

Mungalimbikitsidwe kudziwa kuti achinyamata anzanu achikhristu amachita mantha ndi zinthu zimene inunso mumachita nazo mantha. Mwachitsanzo, mnyamata wina wa zaka 14, dzina lake Christopher, anati: “Ndimaopa kuti anzanga andiseka ndiponso kundiona kuti ndine wotsalira.” Ndiponso Kaleb amene tamutchula kale uja, anati: “Ndimaopa kuti mwina andifunsa funso limene sindingathe kuyankha.”

2. Dziwani kuti si onse amene angagwirizane nanu. Kodi palibe chifukwa chilichonse chochitira mantha? Dziwani kuti nthawi zina m’pomveka kuchita mantha. Ashley anati: “Anzanga ena ankakhala ngati akufuna kudziwa zimene ndimakhulupirira, koma kenako ananditembenukira, n’kuyamba kundiseka pagulu chifukwa cha zimene ndinanena.” Mtsikana wina wa zaka 17, dzina lake Nicole, anati: “Mnyamata wina anayerekezera vesi linalake m’Baibulo lake ndi langa, ndipo anaona kuti mawu ake anali osiyana. Iye anandiuza kuti Baibulo langa linasinthidwa. Zimenezi zinandikhumudwitsa kwambiri moti ndinasowa chonena.” *

Zinthu ngati zimenezi zingakuchititseni mantha. Koma m’malo mozipewa, muziziona kuti ndi zinthu zimene Mkhristu ayenera kukumana nazo pamoyo wake. (2 Timoteyo 3:12) Matthew wa zaka 13, anati: “Yesu ananena kuti otsatira ake adzazunzidwa, choncho sitingayembekezere kuti aliyense azitikonda kapena kusangalala ndi zimene timakhulupirira.”—Yohane 15:20.

3. Ganizirani ubwino wake. Kodi kunyozedwa ndi anzanu kuli ndi ubwino uliwonse? Amber, yemwe ali ndi zaka 21, anati: “N’zovuta kufotokoza chikhulupiriro chako kwa anthu amene sakonda Baibulo. Komabe zimenezi zimakuthandiza kumvetsa zimene umakhulupirira.”—Aroma 12:2.

Onaninso zimene mwanena pa mfundo 1. Ganizirani zinthu ziwiri zabwino zimene zingachitike ndipo zilembeni m’munsimu.

1 ․․․․․

2 ․․․․․

Zokuthandizani: Kodi kuuza anzanu za chikhulupiriro chanu kungakuthandizeni bwanji kuti iwo asamakuvutitseni? Kodi kuchita zimenezi kungakuthandizeni bwanji kuti muzilimba mtima? Nanga zingakhudze bwanji mmene mumaonera Yehova Mulungu, komanso mmene iye amakuonerani?—Miyambo 23:15.

4. Muzikonzekera. Lemba la Miyambo 15:28 limati: “Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe.” Kuwonjezera pa kuganizira zimene munganene, muziganiziranso mafunso amene ena angafunse. Fufuzani mayankho ake ndikuona mmene mungakawafotokozere. Onani tchati chakuti  “Konzekerani Zimene Mungayankhe,” patsamba 25.

5. Mmene mungayambire kukambirana. Kodi mungayambe bwanji kufotokoza za chikhulupiriro chanu? Pali njira zingapo. Kufotokoza za chikhulupiriro chanu kuli ngati kusambira. Ena amalowa m’madzi pang’onopang’ono, pamene ena amangodumphiramo. Inunso mungasankhe kuyamba kukambirana ndi anthu nkhani zomwe si zachipembedzo ndiyeno n’kukambirana nawo nkhani za m’Baibulo. Koma ngati mukuona kuti zimenezi n’zovuta, mungachite bwino kungofikira nkhani za m’Baibulo. (Luka 12:11, 12) Mnyamata wina wa zaka 17, dzina lake Andrew, anati: “Kuganizira zokambirana ndi anthu za chikhulupiriro changa kunkandichititsa mantha kwambiri. Koma ndikangoyamba kukambirana nawo, sizinkandivuta.” *

6. Muziganiza kaye. Munthu wodziwa kusambira sangadumphire mumtsinje mmene muli madzi ochepa. Mofanana ndi zimenezi, muzipewa kulankhula nawo nkhani zopanda phindu. Muzikumbukira kuti pali nthawi yolankhula ndiponso nthawi yokhala chete. (Mlaliki 3:1, 7) Ndipo Yesu nthawi zina sankayankha mafunso. (Mateyo 26:62, 63) Kumbukiraninso mfundo iyi: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”—Miyambo 22:3.

Choncho, winawake akakuuzani mfundo inayake, musafulumire kuyankha. Muziganiza kaye. Mwachitsanzo, ngati mnzanu wa kusukulu wafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani susuta fodya? Mungayankhe kuti, ‘Chifukwa sindifuna kuwononga moyo wanga.’ Malinga ndi zimene anganene, mungaone ngati zili zofunika kum’fotokozera zambiri za chikhulupiriro chanu kapena ayi.

Mfundo zimene tatchulazi, zingakuthandizeni ‘kukhala okonzeka nthawi zonse kuyankha’ aliyense za chikhulupiriro chanu. (1 Petulo 3:15) Komabe, kukonzekera sikutanthauza kuti mantha anu angatheretu. Mtsikana wina wa zaka 18, dzina lake Alana ananena kuti kulimba mtima n’kofunika. Iye anati: “Mukamafotokoza za chikhulupiriro chanu molimba mtima, mumamva bwino. Ndipo mumamvanso bwino kwambiri anthu ena akapanda kukunyozani. Mumasangalala kuti munalimba mtima kulankhula za chikhulupiriro chanu.”

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Maina ena m’nkhani ino tawasintha.

^ ndime 11 Omasulira Baibulo amagwiritsa ntchito mawu osiyanasiyana. Komabe, ena anamasulira bwino Mabaibulo awo potsatira ndendende chinenero choyambirira cha Baibulo.

ZOTI MUGANIZIRE

Kodi mnzanu wina wa kusukulu angakhale kuti akuganiza zotsatirazi?

‘Ndikudziwa kuti ndiwe wa Mboni za Yehova. Mwina ukuganiza kuti ndingakuseke, koma ayi ndimakulemekeza. Kodi n’chifukwa chiyani iweyo sudandaula kwambiri ndi mavuto amene ali padzikoli? Ineyo ndimadandaula. Kodi nkhondo zidzatha padzikoli? Ndimada nkhawa kuti makolo anga angasiyane ukwati? Kodi lero ndiweruka bwinobwino kusukulu popanda kutukwanidwa kapena kumenyedwa? Ndili ndi mafunso ambiri amene amandisokoneza maganizo, koma iweyo umaoneka kuti ukudziwa zimene ukuchita. Kodi n’chifukwa cha chipembedzo chako? Ndingakonde kuti tikambirane nkhaniyi, koma ndikuchita mantha kuiyambitsa. Kodi iweyo ungaiyambitse?’

[Bokosi/Zithunzi patsamba 26]

ZIMENE ANZANU AMANENA

“Anzanga ena ankandiseka ndikawafotokozera za chikhulupiriro changa. Koma akaona kuti zimene akuchitazo sizikundikhudza, ankasiya kundivutitsa.”—Anatero Francesca, Belgium.

“Ukapanda kuuza anzako kuti ndiwe Mkhristu, umaiwala kuti ndiwe wosiyana ndi iwowo ndipo umayamba kuchita zinthu zimene anzakowo akuchita. Si bwino kumangotsatira zilizonse, ndi bwino kuchita zimene zingakuthandize.”—Anatero Samantha, United States.

“Ndili wamng’ono, ndinkangotsatira anzanga. Koma kenako ndinayamba kuona kuti zimene ndimakhulupirira n’zothandiza kwambiri. Nditazindikira zimenezi, ndinayamba kulimba mtima ndipo ndinkanyadira chikhulupiriro changa.”—Anatero Jason, New Zealand.

 [Bokosi patsamba 26]

MMENE MUNGAYAMBIRE KUKAMBIRANA NDI MUNTHU

“Kodi ukuganiza zochita chiyani tikatsekera sukulu?” [Akayankha, mufotokozereni zinthu zauzimu zimene mukufuna kudzachita. Mwachitsanzo, kupita ku msonkhano wachigawo, kapena kuchita upainiya.]

▪ Tchulani nkhani zimene zangochitika kumene, kenako mufunseni kuti: “Kodi unamva nkhani imeneyi? Nanga ukuiona bwanji?

“Kodi ukuona kuti mavuto a zachuma amene akhudza dziko lonse [kapena mavuto ena] adzatha? [Yembekezani ayankhe.] N’chifukwa chiyani ukutero?”

“Kodi umapemphera tchalitchi chanji?”

“Kodi ukuona kuti moyo wako udzakhala bwanji zaka zisanu zikubwerazi?” [Akayankha, muuzeni zinthu zauzimu zimene mukufuna kuchita.]

 [Tchati patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Kukonzekera Zimene Mungayankhe Dulani ndi kusunga tchatichi.

Zimene mungachite: Kambiranani tchatichi ndi makolo anu ndiponso anzanu. Malizitsani kulemba tchatichi. Kenako ganizirani mafunso ena amene anzanu akusukulu angafunse.

funso yankho

Kodi anthu amene Sindimadana nawo, komabe

amagonana amuna ndimaona kuti khalidwe

makhalidwe kapena akazi limeneli si labwino.

okhaokha umawaona

bwanji?

N’chifukwa

kukhala ndi chiyani ulibe Ndikufuna kuti ndikule kaye.

chibwenzi chibwenzi?

N’chifukwa Ndimakonda dziko langa koma

kusachita chiyani sindimalilambira.

zandale sugwadira

mbendera?

Kodi n’chifukwa Timalola kupatsidwa mankhwala

magazi chiyani simulola owonjezera magazi amene

kuikidwa magazi? sangatipatsire edzi. Komanso

Baibulo limanena kuti tizisala

magazi.

Anzako ena

achipembedzo

sankhani chako amachita Timaphunzitsidwa malamulo a

zakutizakuti. Mulungu koma zili kwa munthu

N’chifukwa chiyani aliyense kusankha kuwatsatira

iweyo suchita nawo? kapena ayi.

N’chifukwa chiyani Palibe chifukwa chokhulupirira

simukhulupirira kuti kuti zinthu zinachita kusintha.

chilengedwe zamoyo zinachita Ngakhale asayansi ena

kusintha kuchokera sakhulupirira zimenezi.

ku zinthu zina?

funso lotsatira fufuzani yankho

Kodi maganizo 1 Akorinto 6:9, → Ayi, chifukwa

makhalidwe amenewa si 10; Mayankho a sindigwirizana ndi

olakwika? Zimene kugonana

Achinyamata Amafunsa, kwa mtundu

Buku Lachiwiri, mutu 28. * uliwonse, kuphatikizapo

kugonana kwa amuna

kapena akazi okhaokha.

Kapena n’chifukwa Nyimbo ya Solomo Munthu ukayamba

kukhala ndi cha chipembedzo 8:4; Zimene chibwenzi

chibwenzi chako? Achinyamata Amafunsa, Buku ndiye kuti

Lachiwiri, mutu 1. ukufuna banja. Ineyo

sindinayambe kuganiza

zokhala pabanja.

Ndiye kuti zinthu Yesaya 2:4; Yohane Palibe chifukwa chofera

kusachita zitavuta sungafere 13:35; Kodi Baibulo dziko langa. Chifukwatu

zandale dziko lako? Limaphunzitsa Chiyani Mboni za Yehova

Kwenikweni?, masamba 148-151. * za m’mayiko ena

sizingamenyane ndi

dziko lathu.

Nanga bwanji ngati Machitidwe 5:28, 29; → ․․․․․

watsala pang’ono Aheberi 11:6;

magazi kufa? Kodi Mulungu Baibulo Limaphunzitsa Chiyani,

sangakukhululukire masamba 129-131.

utalandira magazi?

Kodi zimenezi ․․․․․ ․․․․․

sankhani sizikusonyeza kuti

mumayendera

malamulo osiyana?

chilengedwe → ․․․․․ ․․․․․ ․․․․․

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 53 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 55 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 26]

Kuyamba kufotokoza za chikhulupiriro chanu kuli ngati kusambira. Ena amalowa m’madzi pang’onopang’ono, pamene ena amangodumphiramo