Nsomba Yochititsa Chidwi
Panagona Luso!
Nsomba Yochititsa Chidwi
Asayansi akufuna kupanga galimoto potengera nsomba inayake yooneka ngati bokosi imene imapezeka m’nyanja za kumadera otentha, m’miyala yokongola kwambiri ya pansi pa nyanja. Galimoto imene apangeyo siizitha kwambiri mafuta, siiziwononga chilengedwe, komanso ndi yoti siingagwe mwachisawawa. Galimoto imeneyi idzakhala yosalemera kwambiri ndiponso yothamanga zedi.
Taganizirani izi: Nsombayi imathamanga kwambiri moti pasekondi iliyonse imayenda ulendo wautali kupitirira ka 6 kutalika kwake. Nsombayi imaoneka ngati bokosi ndipo zimenezi n’zimene zimachititsa kuti izithamanga kwambiri. Ndipotu galimoto imene apangeyo izithamanga kwambiri kuposa magalimoto ena, makamaka kunja kukakhala mphepo.
Khungu la nsombayi limaoneka ngati fupa ndipo zimenezi zimachititsa kuti ikhale yolimba koma yosalemera kwambiri. Nsombayi imayenda bwinobwino ngakhale m’madzi othamanga kwambiri.
Asayansi akukhulupirira kuti nsombayi ithandiza kwambiri anthu popanga magalimoto osatha mafuta, osalemera kwambiri ndiponso oti sangachite ngozi mwachisawawa. Wasayansi wina dzina lake Dr. Thomas Weber anati: “N’zochititsa chidwi kwambiri kuti nsomba yosaoneka bwino imeneyi itithandiza popanga galimoto zothamanga kwambiri komanso zosatha mafuta.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi nsomba yochititsa chidwi imeneyi inakhalako yokha kapena inachita kulengedwa?
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
Boxfish: © Hal Beral/V&W/SeaPics.com; car: Mercedes-Benz USA