Chikondi Chimathetsa Tsankho
Chikondi Chimathetsa Tsankho
“Kwanthawi yoyamba m’mbiri yonse ya anthu, kunakhazikitsidwa gulu latsopano lachipembedzo lopangidwa ndi anthu a zikhalidwe, mitundu komanso mayiko osiyanasiyana, omwe ankalambira Mulungu mogwirizana.”—Anatero Paul Johnson m’buku lakuti A History of Christianity.
PAMENE Chikhristu choona chinkafalikira m’madera ambiri mu Ufumu wa Roma, anthu anadabwa kwambiri kuona kuti anthu ochokera m’madera osiyanasiyana ankakhala mogwirizana komanso mwamtendere ngati banja limodzi. Anthuwa ankagwirizana chifukwa chakuti ankakondana kwambiri. Chimenechi chinali chikondi chenicheni ndipo anthuwa ankakondana chonchi chifukwa chakuti ankatsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu.
Mfundo zimenezi n’zimene Yesu ankatsatira pamoyo wake, ndipo n’chifukwa chake anthu ena ankamuda komanso kumusala. (1 Petulo 2:21-23) Yesu ankasalidwanso chifukwa chakuti anali wochokera ku Galileya. Anthu a ku Galileya ankanyozedwa ndi atsogoleri achipembedzo chachiyuda ku Yerusalemu chifukwa chakuti ambiri anali alimi ndi asodzi. (Yohane 7:45-52) Yesu anali mphunzitsi waluso, yemwe ankakondedwa komanso kulemekezedwa ndi anthu wamba. Chifukwa cha zimenezi, atsogoleri achipembedzo anayamba kum’chitira nsanje ndipo ankamunamizira zinthu zambiri mpaka kufuna kumupha.—Maliko 15:9, 10; Yohane 9:16, 22; 11:45-53.
Komabe, Yesu ‘sanabwezere choipa pa choipa.’ (Aroma 12:17) Mwachitsanzo, pamene Afarisi ena anafunsa Yesu mafunso, iye anawayankha mwaulemu. (Yohane 3:1-21) Nthawi zina Yesu ankadya ndi Afarisi, moti nthawi ina anadya ndi Mfarisi wina amene anasala Yesuyo. Kodi anamusala bwanji? Panthawiyo mlendo akafika pakhomo anthu ankamusambitsa mapazi, koma Mfarisiyu sanachite zimenezi. Kodi Yesu anamuimba mlandu Mfarisiyu chifukwa chosamusambitsa mapazi? Ayi. M’malomwake anagwiritsa ntchito mpata umenewu kuphunzitsa anthu za kufunika kwa chifundo ndi kukhululukirana.—Luka 7:36-50; 11:37.
Yesu Ankakonda Anthu Onyozeka
Fanizo la Msamariya wachifundo limene Yesu anafotokoza ndi limodzi mwa mafanizo ake odziwika bwino. M’fanizoli, Msamariya wachifundoyu, anasamalira Myuda wina amene anamenyedwa ndi achifwamba. (Luka 10:30-37) Kodi zimene anachita Msamariya ameneyu zinali zofunika chifukwa chiyani? Ayuda ndi Asamariya ankadana kwambiri. Ndipotu Ayuda akatchula munthu kuti “Msamariya” kunali kumunyoza kwambiri. Ngakhale Yesu ananyozedwapo kuti iye ndi “Msamariya.” (Yohane 8:48) Ichi n’chifukwa chake Yesu anagwiritsira ntchito fanizo la Msamariya wachifundo posonyeza kuti tsankho si labwino.
Yesu ankachita zimene ankaphunzitsa. Mwachitsanzo, nthawi ina iye anachiritsa wakhate wina wachisamariya. (Luka 17:11-19) Komanso iye ankalalikira Asamariya, ndipo panthawi ina analalikira mkazi wachisamariya kwanthawi yaitali. (Yohane 4:7-30, 39-42) Zimenezi zinali zodabwitsa chifukwa Arabi achiyuda sankalankhula ndi mkazi wina aliyense pagulu, ngakhale mkaziyo atakhala m’bale wawo. Kulankhula ndi mkazi wachisamariya ndiye sakanayerekeza n’komwe.
Kodi Mulungu amamuona bwanji munthu amene akuyesetsa kuthetsa maganizo atsankho? Baibulo limatiuza mfundo zolimbikitsa kwambiri pankhani imeneyi.
Mulungu Amaleza Nafe Mtima
Potengera chikhalidwe cha nthawi imeneyo, Akhristu achiyuda ankadana ndi anthu ambiri omwe analowa Chikhristu koma sanali Ayuda. Kodi Yehova anatani kuti athetse khalidwe latsankho limeneli? Iye anachita zinthu moleza mtima ndipo ankaphunzitsa mpingo wachikhristu pang’onopang’ono. (Machitidwe 15:1-5) Kuleza mtima kumeneku kunabala zipatso, chifukwa monga mmene taonera kumayambiriro kwa nkhani ino, ‘anthu a zikhalidwe, mitundu komanso mayiko osiyanasiyana ankalambira Mulungu mogwirizana.’ Ichi n’chifukwa chake “mipingo inapitiriza kulimba m’chikhulupiriro ndi kuwonjezeka m’chiwerengero tsiku ndi tsiku.”—Machitidwe 16:5.
Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani? Tikuphunzira kuti ngati ena akutisala, tisataye mtima, koma tipitirize kudalira Mulungu amene amapereka nzeru ndiponso mphamvu kwa onse amene ‘akum’pempha m’chikhulupiriro.’ (Yakobe 1:5, 6) Kodi mukukumbukira nkhani ya Jennifer, Timothy, John, ndi Olga amene tinawatchula m’nkhani yoyambirira ija? Pamene Jennifer amayamba sukulu ya sekondale, anali wolimba mwauzimu ndipo sankakhumudwa anthu akamamusala chifukwa cha mtundu wake kapena msinkhu wake. Ndiyeno, mtsikana winanso atayamba kunyozedwa ndi anzake kusukulu, Jennifer ankamuteteza komanso ankamulimbikitsa kuti asakhumudwe.
Kodi n’chiyani chinathandiza Timothy kuti asamakhumudwe anzake akamamunyoza? Iye anati: “Sindinkakhumudwa chifukwa sindinkafuna kunyozetsa dzina la Yehova Mulungu. Ndinkakumbukiranso kuti tiyenera ‘kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.’”—Aroma 12:21.
Nayenso John anasiya kusala anthu amtundu wachihausa, amene ankaphunzira naye limodzi. Iye anati: “Ndili pasukulu, ndinayamba kucheza ndi ana amtundu wachihausa. Panthawi ina aphunzitsi anandipatsa ntchito yoti ndigwire ndi mmodzi wa anawa ndipo tinayamba kugwirizana kwambiri. Panopa ndikamaona anthu amitundu ina, sindiganizira za mtundu kapena fuko lawo.”
Komanso Olga pamodzi ndi m’mishonale mnzake sankakhumudwa anthu akamawanyoza. Iwo ankapitirizabe ntchito yawo ndipo ankakhulupirira kuti anthu ena adzamvetsera ntchito yawo yolengeza uthenga wa m’Baibulo. Chifukwa cha khama lawo, anthu ambiri anayamba kuphunzira Baibulo. Olga anati: “Patadutsa zaka 50, munthu wina anabwera n’kundipatsa chikwama chokongola kwambiri. M’chikwamamo munali miyala ing’onoing’ono yomwe anailemba mawu akuti, ubwino, kukoma mtima, chikondi, ndi mtendere, omwe ndi makhalidwe achikhristu. Iye anandiuza kuti anali mmodzi wa anyamata amene ankandigenda miyala aja koma panthawiyi anali atakhala m’bale wanga wachikhristu. Iye ndi mkazi wake anandipatsanso maluwa okongola.”
Tsankho Lidzatha
Posachedwapa tsankho lidzatha. Koma kodi lidzatha bwanji? Dziko lapansi lidzalamulidwa ndi Yesu Khristu yemwe anasonyeza kuti “sadzaweruza monga apenya maso.” (Yesaya 11:1-5) Komanso anthu omwe adzalamulidwe ndi Yesu adzatengera chitsanzo chake, chifukwa onse adzakhala ataphunzitsidwa ndi iye ndiponso Atate ake, Yehova Mulungu.—Yesaya 11:9.
Pokonzekeretsa anthu a Mulungu kulowa m’dziko latsopano lopanda tsankho, panopa maphunziro auzimu amenewa akuchitika padziko lonse lapansi. Bwanji osachita nawo maphunziro amenewa mwa kupempha kuti muziphunzira Baibulo? * Kunena zoona, Mulungu alibe tsankho, ndipo cholinga chake n’chakuti anthu amitundu yonse “apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”—1 Timoteyo 2:3, 4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 18 Ngati mukufuna kuphunzira Baibulo kwaulere, panthawi ndi malo amene mungakonde, pitani ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kapena lemberani kalata ofesi ya nthambi pa adiresi yomwe ili patsamba 5. Kapena fufuzani Mboni za Yehova pa Intaneti pogwiritsa ntchito adiresi iyi: www.pr418.com.
[Mawu Otsindika patsamba 8]
Posachedwapa tsankho lidzatha
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 8, 9]
MFUNDO ZA M’BAIBULO ZOTI TIZITSATIRA
▪ “Musabwezere choipa pa choipa . . . Pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” (Aroma 12:17-21) Apa mfundo ndi yakuti anthu ena akatichitira zoipa, ifeyo tiziwachitira zabwino. Anthu “anadana [ndi Yesu] popanda chifukwa,” koma iye sanawabwezere.—Yoh. 15:25.
▪ “Tisakhale odzikuza, . . . ndi ochitirana kaduka.” (Agal. 5:26) Mulungu sasangalala ndi munthu wansanje ndiponso wonyada, chifukwa zimenezi zimayambitsa chidani ndi tsankho.—Maliko 7:20-23.
▪ “Chotero zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.” (Mateyo 7:12) Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimafuna kuti anthu azindichitira chiyani?’ Zimene mukufuna kuti ena akuchitirenizo, inunso muziwachitira zomwezo, mosaganizira msinkhu, khungu, chilankhulo kapena chikhalidwe chawo.
▪ “Landiranani wina ndi mnzake, mmene Khristu anatilandirira, kuti ulemerero upite kwa Mulungu.” (Aroma 15:7) Kodi mumayesetsa kudziwa anthu ochokera m’mayiko ndiponso zikhalidwe zosiyanasiyana, makamaka ngati ali atumiki a Mulungu anzanu?—2 Akorinto 6:11.
▪ “Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya, Yehova adzanditenga.” (Sal. 27:10, NW) Ngakhale anthu ena atakuzunzani, Yehova sadzakusiyani ngati muli okhulupirika kwa iye.
[Chithunzi patsamba 7]
Msamariya wachifundo anathandiza Myuda amene anamenyedwa ndi achifwamba