Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Abusa Ndi Apamwamba Kuposa Anthu Ena Mumpingo?

Kodi Abusa Ndi Apamwamba Kuposa Anthu Ena Mumpingo?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Abusa Ndi Apamwamba Kuposa Anthu Ena Mumpingo?

Abusa, Abambo, Bambo Mfumu, Ambuye, Atsogoleri. Amenewa ndi ena mwa maina aulemu amene amalekanitsa anthu audindo mumpingo ndi anthu wamba. Zipembedzo zambiri zimachita zimenezi, koma kodi n’zimene Mulungu amafuna kapena ndi zofuna za anthu?

KATSWIRI wina wa maphunziro a zaubusa, dzina lake Cletus Wessels, anati: “Mabuku a Chipangano Chatsopano sasonyeza kuti panali kusiyana pakati pa atsogoleri a mpingo ndi anthu ena. Ndipo palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti Akhristu m’nthawi ya atumwi ankatchulana maina aulemu.” Koma buku lina lofotokoza zachikhristu limati: “Patapita nthawi anthu amene anali ndi udindo mumpingo anayamba kuonedwa kuti ndi apamwamba kwambiri kuposa anthu ena . . . Ndipo anthu wamba mumpingo ankatengedwa kuti ndi anthu osadziwa Mulungu ndi Baibulo.” Zimenezi zinafala kwambiri patapita zaka zoposa 200 kuchokera pamene Yesu Khristu anafa.

Popeza kuti anthu audindo mumpingo sankaonedwa kuti ndi apamwamba m’nthawi ya atumwi, kodi pali cholakwika chilichonse kuwatchula maina aulemu panopa? Malinga ndi zimene Baibulo limanena, zimenezi n’zolakwika. N’zolakwika chifukwa chiyani?

“Nonsenu Ndinu Abale”

Mawu a Mulungu amatiuza kuti tonse ndife atumiki a Mulungu ndipo palibe aliyense amene ali wapamwamba kuposa mnzake. (2 Akorinto 3:5, 6) Katswiri wina wolemba mabuku achipembedzo, dzina lake Alexandre Faivre, anati: “Akhristu oyambirira sankafuna kuti anthu ena akhale apamwamba ndipo ena otsika.” Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene Yesu anauza ophunzira ake, kuti: “Nonsenu ndinu abale.”—Mateyo 23:8.

N’zoona kuti Akhristu ena okhwima mwauzimu ankakhala ndi udindo monga kuphunzitsa ndi kuyang’anira nkhosa za Mulungu. (Machitidwe 20:28) Komabe, anthu amenewa sankalipidwa. Ambiri mwa anthu amenewa ankagwira ntchito zawo ndipo anali ndi akazi komanso ana. Ndiponso, iwo ankapatsidwa udindo osati chifukwa cha maphunziro a zaubusa amene anachita koma chifukwa chakuti ankalimbikira kuphunzira Mawu a Mulungu, komanso ankayesetsa kukhala ndi makhalidwe achikhristu. Munthu amene angapatsidwe udindo mumpingo ayenera kukhala “wodziletsa m’zizolowezi zake, woganiza bwino, wadongosolo, wochereza alendo, wokhoza kuphunzitsa. . . . wololera. Asakhale waukali, kapena wokonda ndalama. Akhale mwamuna woyang’anira bwino banja lake.”—1 Timoteyo 3:1-7.

Ndi Bwino Kutsatira Baibulo

Baibulo limati: “Musapitirire zinthu zolembedwa.” (1 Akorinto 4:6) N’zomvetsa chisoni kuti anthu amene satsatira lamulo limeneli amawononga ubwenzi wawo ndi Mulungu, ndipo zimenezi n’zimene zimachitika anthu audindo mumpingo akamaonedwa kuti ndi apamwamba kuposa ena. Tikutero chifukwa cha mfundo 6 zotsatirazi:

1. Ngati anthu audindo mumpingo akuonedwa kuti ndi apamwamba kuposa ena, zingasonyeze kuti anthuwo anasankhidwa mwapadera kuti akhale atumiki a Mulungu. Koma Baibulo limanena kuti Akhristu onse oona angathe kutamanda Mulungu ndi kukhala atumiki ake. (Aroma 10:9, 10) Komanso amuna onse Achikhristu amapatsidwa mwayi wokhala ndi udindo mumpingo ndipo zimenezi n’zimene Mboni za Yehova zimachita.—1 Timoteyo 3:1.

2. Ngati anthu amene ali ndi udindo mumpingo amapatsidwa maina aulemu, ndiye kuti anthuwo amaonedwa kuti ndi apamwamba kuposa ena. Komabe Yesu anati: “Aliyense wokhala ngati wamng’ono mwa inu nonse ndi amene ali wamkulu.” (Luka 9:48) Mogwirizana ndi mfundo imeneyi Yesu analetsa ophunzira ake kupatsidwa maina aulemu.—Mateyo 23:8-12.

3. Abusa amene amapatsidwa malipiro amakhala mtolo kwa anthu ena mumpingo, makamaka ngati abusawo ali ndi moyo wokonda kuwononga ndalama. Koma oyang’anira achikhristu amagwira ntchito kuti apeze zinthu zofunika pamoyo wawo ndipo mwanjira imeneyi amapereka chitsanzo chabwino kwa anthu ena. *Machitidwe 18:1-3; 20:33, 34; 2 Atesalonika 3:7-10.

4. Popeza kuti abusa amadalira anthu ena kuti awapatse malipiro, nthawi zina iwo anganene zinthu zowakomera anthuwo m’malo mophunzitsa uthenga wa m’Baibulo molimba mtima. Malemba ananeneratu kuti zimenezi zidzachitika m’masiku athu ano. Baibulo limati: “Idzafika nthawi imene anthu sadzafunanso chiphunzitso chopindulitsa, koma mogwirizana ndi zilakolako za iwo eni, adzadzipezera okha aphunzitsi kuti amve zowakomera m’khutu.”—2 Timoteyo 4:3.

5. Abusa akamaonedwa kuti ndi apamwamba kuposa anthu ena mumpingo, anthuwo amawasiyira abusawo zinthu zonse zokhudza kulambira, ndipo iwo amangobwera kutchalitchi mwamwambo chabe. Koma Akhristu onse ayenera kudziwa zosowa zawo zauzimu ndi kuyesetsa kuphunzira Baibulo mwakhama.—Mateyo 4:4; 5:3.

6. Anthu amene sadziwa zambiri za Baibulo, anganamizidwe kapena kudyeredwa masuku pamutu mosavuta ndi abusa awo. Zimenezi si zachilendo chifukwa zakhala zikuchitika kuyambira kale kwambiri. *Machitidwe 20:29, 30.

Mboni za Yehova zimayesetsa kutsatira Baibulo ndipo m’gulu lawo mulibe anthu apamwamba kuposa ena. M’mipingo ya Mboni za Yehova muli abusa achikhristu amene amaweta ndi kuphunzitsa nkhosa za Mulungu popanda kulipidwa. Kuti mudziwe zambiri mungachite bwino kupita ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yomwe muli nayo pafupi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 M’nthawi ya atumwi oyang’anira amene ankayendera mipingo nthawi zina ‘ankapeza zochirikiza moyo mwa uthenga wabwino.’ Iwo ankalandiridwa m’nyumba za anthu ndi kulandira zopereka zimene anthu ankawapatsa mwa kufuna kwawo.—1 Akorinto 9:14.

^ ndime 16 Chitsanzo cha zinthu ngati zimenezi ndi kupereka ndalama kwa ansembe kuti munthu akhululukidwe machimo ake, nkhanza za khoti la tchalitchi cha Katolika, ndiponso kuwotchedwa kwa Mabaibulo ndi azibusa amene sankafuna kuti anthu awo aziwerenga okha Mawu a Mulungu.—Onani Nsanja ya Olonda ya November 15, 2002, tsamba 27.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi anthu onse a Mulungu amaonana bwanji?—Mateyo 23:8.

▪ Kodi chimafunika n’chiyani kuti munthu apatsidwe udindo mumpingo wachikhristu?—1 Timoteyo 3:1-7.

▪ Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu sasangalala ndi zoti anthu ena azionedwa kuti ndi apamwamba kuposa ena mumpingo?—1 Akorinto 4:6.

[Mawu Otsindika patsamba 23]

Mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo, Yesu sankadziona kuti iye ndi wapamwamba kuposa ena