Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumatha Kusunga Zinthu Zanu Mwachinsinsi?

Kodi Mumatha Kusunga Zinthu Zanu Mwachinsinsi?

Kodi Mumatha Kusunga Zinthu Zanu Mwachinsinsi?

Kodi munayamba mwagulapo zinthu pa Intaneti kapena kugwiritsa ntchito khadi potenga ndalama kubanki? Ngati munachitapo zimenezi ndiye kuti mukudziwa bwino kufunika kosunga chinsinsi.

KALE, manambala kapena zilembo zachinsinsi zinkagwiritsidwa ntchito ndi boma, akazembe, akazitape ndi asilikali basi. Koma masiku ano zinthu zasintha. Chifukwa cha kubwera kwa makompyuta ndi Intaneti, zinthu zambiri zimasungidwa pogwiritsa ntchito manambala kapena zilembo zachinsinsi. Choncho, kusunga manambala kapena zilembo zimenezi mosamala n’kofunika kwambiri.

Mwina mungadzifunse kuti, Kodi zinthu zanga n’zotetezeka? Kodi ndingatani kuti zikhale zotetezeka? Mukuganizira mafunso amenewa, dziwani kuti kuyambira kale kwambiri anthu opanga manambala kapena zilembo zachinsinsi akhala akulimbana ndi akuba amene amatulukira zinsinsi zimenezi.

Kubisa Zimene Talemba

Njira imodzi yosungira chinsinsi yomwe ndi yakale kwambiri ndi yobisa zimene talemba kuti anthu ena asazione. Katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Herodotus, analemba kuti munthu wina wa ku Girisi yemwe anathamangitsidwa n’kukakhala kunja kwa dzikolo, anazindikira kuti dziko la Perisiya likufuna kumenyana ndi dziko lake. Pofuna kuchenjeza anthu a m’dziko lake, iye analemba mauthenga pamatabwa n’kupaka phula kuti anthu ena asaone zimene analembazo. Malinga ndi zimene Herodotus ananena, zimene munthuyo analemba zinathandiza anthu a ku Girisi kudziwa chiwembu chimene Mfumu Sasta ankafuna kuchita, ndipo chifukwa cha zimenezi asilikali a Sasta anagonjetsedwa. Aroma ankagwiritsanso ntchito njira imeneyi.

Masiku ano pali njira zambiri zobisira zinthu zimene talemba kapena zithunzi kuti ena asazione komanso kuzikopera. Panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse anthu ankagwiritsa ntchito njira imeneyi ndipo chithunzi chachikulu ankatha kuchichepetsa n’kumaoneka ngati kadontho. Munthu amene watumiziridwa chithunzicho ankachikulitsa kuti athe kuchiona. Masiku ano anthu amene amagulitsa zithunzi zolaula amatsatira njira ngati imeneyi pogwiritsa ntchito makompyuta.

Popeza zinthu zimene zalembedwa zimakhala kuti sizikuoneka, munthu amene watumidwa kuti atumize kapena kulandira uthengawo sachita nawo chidwi. Komabe ngati anthu ena atatulukira chinsinsicho, angathe kuwerenga uthengawo, pokhapokha ngati uthengawo mutaulemba mwanjira yakuti munthu asamve tanthauzo lake.

Kubisa Tanthauzo la Zimene Talemba

Njira ina yosungira chinsinsi ndi yolemba zinthu mwanjira yakuti anthu ena asathe kuziwerenga. Ngakhale kuti anthu ena angaone zimene talembazo, iwo sangadziwe tanthauzo lake, pokhapokha ngati titawauza chinsinsi chathu.

Anthu akale a mumzinda wa Sparta ku Girisi ankachita zimenezi pogwiritsa ntchito makina enaake. Munthu wolemba uthengawo ankakulungakulunga chikopa pandodo, n’kuyamba kulemba uthengawo m’lifupi mwa chikopacho. Akachitambasula chikopacho, zimene zalembedwazo sizimawerengeka. Koma munthu amene walandira uthengawo akakulunga chikopacho pandodo yofanana ndi imene anagwiritsa ntchito polemba ija, amawerenga uthengawo mosavuta. Nthawi zinanso uthengawo unkabisidwa povala chikopacho mu mchiuno.

Akuti Kaisara Juliyo anabisa mauthenga ake ankhondo mwakusemphanitsa zilembo. Mwachitsanzo, m’malo molemba a ankalemba d, ndipo m’malo mwa b ankalemba e. 

Mayiko a ku Ulaya atayamba kutukuka, anthu anapeza njira zina zotsogola zobisira tanthauzo la zinthu zimene ankalemba. Kazembe wina wa dziko la France, dzina lake Blaise de Vigenère yemwe anabadwa m’chaka cha 1523, ndiye anapititsa patsogolo kwambiri luso limeneli. Vigenère anapeza njira yobisira tanthauzo la mawu pogwiritsa ntchito zilembo za afabeti pozilemba mwa ndondomeko inayake. Anthu ankaganiza kuti palibe amene angathe kutulukira njira yowerengera zinthu imeneyi. Komabe, pamene luso lolemba zinthu mobisa lapita patsogolo, anthu akuba nawonso akutulukira njira zatsopano zobera.

Mwachitsanzo, akatswiri a maphunziro achisilamu atafufuza zilembo za m’Korani, ya chinenero cha Chiarabu, anapeza kuti zilembo zina zimapezeka kambirimbiri kuposa zina ndipo akuti zimenezi zimachitikanso m’zinenero zambiri. Zimene anatulukirazi zathandiza kwambiri kuti anthu azitha kutulukira zinthu zimene zalembedwa mwachinsinsi. Kuti adziwe zimene chizindikiro chilichonse chikuimira, iwo amawerenga kuchuluka kwa chizindikirocho mu nkhani imene yalembedwa mobisayo. Ndipo kenako amatha kuwerenga uthengawo mosavuta.

Pofika m’zaka za m’ma 1400, akazembe ambiri kumayiko a ku Ulaya ankagwiritsa ntchito kwambiri njira yobisa zinthu imeneyi. Komabe, nthawi zina anthu ena ankatha kuwerenga zimene akazembewo ankalemba. Mwachitsanzo, munthu wina wa ku France, dzina lake François Viète, anatha kutulukira njira imene khoti lalikulu la ku Spain linkalembera zinthu. Iye ankatha kuwerenga bwinobwino zinthu zimene khotilo limaona kuti palibe angakwanitse kuziwerenga. Mfumu Philip yachiwiri ya ku Spain inaganiza kuti Viète amagwiritsa ntchito mphamvu za Satana ndipo iye atagwidwa, mfumuyi inalamula kuti aweruzidwe m’khoti la Akatolika.

Luso Losunga Zinthu Mwachinsinsi

M’zaka za m’ma 1900, makamaka panthawi ya nkhondo ziwiri za padziko lonse, anthu anayamba kugwiritsa ntchito makina polemba zinthu mobisa. Mwachitsanzo, ku Germany anthu ena anapanga makina ooneka ngati taipilaita amene anawakonza kuti azisintha zilembo. Munthu akamalemba, makinawo ankasintha zimene zimalembedwazo n’kutulutsa zinthu zimene anthu ena sangathe kuwerenga. Komabe, nthawi zina anthu amene ankagwiritsa ntchito makinawo akapanda kusamala, ankalemba zinthu zimene zimaulula chinsinsi chawo. Choncho anthu ena anayamba kudziwa zimene amalembazo.

Kubwera kwa makompyuta kwachititsa kuti anthu ambiri azigwiritsa ntchito manambala kapena zilembo zachinsinsi. Mwachitsanzo, manambala achinsinsi amafunika potenga kapena kuika ndalama kubanki, komanso posunga chinsinsi cha odwala kuchipatala ndiponso chinsinsi cha boma.

Mukalemba nambala kapena zilembo zachinsinsi, kompyuta imene mukugwiritsa ntchito imasintha yokha zimenezi n’kukhala mawani komanso mazilo okhaokha. Dziwaninso kuti nambala yanu yachinsinsi ikakhala ndi zilembo zambiri, anthu akuba zingawavute kuti aitulukire. Mwachitsanzo, ngati nambala yanu yachinsinsi ili ndi zilembo 8, munthu wakuba angafunikire kuyeserera manambala 256 kuti atulukire nambala yanuyo. Koma ngati nambala yanu yachinsinsi itakhala ya zilembo 56, munthu wakuba angafunikire kuyeserera manambala osiyanasiyana okwana 72 kwadililiyoni kuti atulukire nambala yanuyo. Masiku ano manambala achinsinsi amene amagwiritsidwa ntchito pobisa zinthu pa Intaneti amakhala ndi zilembo 128. Kuti akuba atulukire mambala imeneyi angafunikre kuyeserera manambala ochuluka 4.7 sekisitiliyoni kuposa amene angayeserere ndi nambala ya zilembo 56. *

Komabe anthu akuba amatha kutulukira manambala achinsinsi amenewa. Mwachitsanzo, m’chaka cha 2008 anthu okwana 11 anamangidwa ku United States chifukwa cha umbava woterewu. Anthuwa ankatha kudziwa manambala a anthu osiyanasiyana omwe amagulira zinthu, pogwiritsa ntchito makompyuta ndi Intaneti.

Kodi Zinthu Zanu N’zotetezeka?

Kunena zoona, n’zovuta kuti akuba adziwe nambala yanu ya khadi la kubanki. Komabe, ngati simusamala n’zotheka kukuberani. Baibulo limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” (Miyambo 22:3) Anthu sangakubereni ngati ‘mutabisala’ pochita zinthu zotsatirazi:

▪ Ikani mu kompyuta mwanu pulogalamu yoteteza kuti musalowe vailasi.

▪ Ikani mu kompyuta mwanu pulogalamu yokudziwitsani kuti anthu ena akutsegula kompyuta yanuyo mwachinsinsi kudzera pa Intaneti.

▪ Ikani mu kompyuta mwanu pulogalamu yoletsa anthu ena kutsegula kompyuta yanu.

▪ Onetsetsani kuti mapulogalamu onsewa akugwira ntchito bwinobwino.

▪ Muzisamala ndi mauthenga a pa Intaneti ochokera kwa anthu osawadziwa bwino ndipo musapereke nambala yanu yachinsinsi kwa anthu okayikitsa.

▪ Potumiza zinthu zachinsinsi monga nambala ya kubanki, gwiritsani ntchito njira yachinsinsi yotumizira nambalayo ndipo mukamaliza mutseke bwinobwino adiresi yanu ya pa Intaneti.

▪ Gwiritsani ntchito nambala yachinsinsi yoti anthu ena sangathe kuidziwa ndipo itetezeni.

▪ Musagwiritse ntchito mapulogalamu amene achokera kwa anthu osawadziwa.

▪ Mukamasunga zinthu mu kompyuta, onetsetsani kuti zina mukuzisunga pamalo ena otetezeka.

Ngati mutatsatira malangizo amenewa, anthu ena sangathe kuona zinthu zanu zachinsinsi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Kwadililiyoni ndi nambala imene imatsatiridwa ndi maziro 15. Sekisitiliyoni ndi nambala imene imatsatiridwa ndi maziro 21.

[Chithunzi patsamba 26]

Chikopa cha ku Sparta

[Chithunzi patsamba 26]

Makina a ku Germany a zaka za m’ma 1900

[Chithunzi patsamba 26]

Masiku ano, manambala achinsinsi amateteza zinthu zanu