Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Ngati Mayi Kapena Bambo Anga Amwalira?

Kodi Ndingatani Ngati Mayi Kapena Bambo Anga Amwalira?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Ngati Mayi Kapena Bambo Anga Amwalira?

“Mayi anga atamwalira, ndinali ndi chisoni chachikulu. Iwo ndi amene ankachititsa kuti banja lathu likhale logwirizana.”—Anatero Karyn. *

IMFA ya bambo kapena mayi ndi yopweteka kwambiri chifukwa mumakhala kuti mwataya munthu wofunika kwambiri komanso tsogolo lanu lonse limasintha.

Mwina munkayembekezera kuti mayi kapena bambo anu adzakhala ali ndi moyo n’kuona inuyo mukukhoza mayeso oyendetsa galimoto, mukumaliza sukulu, kapena mukukwatira. Koma iwo amwalira ndipo zonse zimene mumayembekezera sizidzachitika. Panopa muli ndi chisoni chachikulu. Kodi mungatani ngati muli ndi chisoni chifukwa chakuti mayi kapena bambo anu amwalira?

‘Kodi Ndili Bwinobwino?’

Pamene mayi kapena bambo anu amwalira, mungamaganize zinthu zambiri zimene poyamba simunkaganiza. Brian, yemwe bambo ake anamwalira ndi matenda a mtima iye ali ndi zaka 13, anati: “Tsiku limene bambo anamwalira, ndinkangolira.” Koma Natalie, yemwe bambo ake anamwalira ndi matenda a khansa iye ali ndi zaka 10, anati: “Sizinandikhudze ngakhale pang’ono. Ndipo ndinkangoona ngati palibe chimene chachitika.”

Imfa imakhudza anthu mosiyanasiyana. Baibulo limanena kuti ‘aliyense amadziwa yekha chisoni chake.’ (2 Mbiri 6:29) Choncho, inuyo panokha muyenera kuganizira mmene imfa ya makolo anu yakukhudzirani. Lembani pansipa (1) mmene munamvera mayi kapena bambo anu atamwalira (2) mmene mukumvera panopa. *

(1) ․․․․․

(2) ․․․․․

Mwina zimene mwayankha zikusonyeza kuti chisoni chanu chikutha. Zimenezi n’zimene zimachitika ndipo sizitanthauza kuti mwaiwala makolo anu. Kapena zimene mwayankha zikusonyeza kuti chisoni chanu sichikutha. Kapenanso zikusonyeza kuti chisoni chanu chili ngati mafunde, chimayamba kapena kutha mosayembekezereka. Zimenezi zimachitikanso ngakhale ngati papita zaka zambiri kuchokera pamene makolo anu anamwalira. Komabe, funso ndi lakuti, Kodi mungatani ngati muli ndi chisoni chifukwa chakuti mayi kapena bambo anu amwalira?

Zimene Mungachite

Musaope Kulira. Kulira kumathandiza kuti muchepetse nkhawa. Komabe, mwina mungamve ngati Alicia, yemwe mayi ake anamwalira iye ali ndi zaka 19. Iye anati: “Ndinkaona kuti ndikasonyeza chisoni kwambiri, anthu ena aganiza kuti ndilibe chikhulupiriro.” Taganizirani izi: Yesu Khristu anali munthu wangwiro amene ankakhulupirira kwambiri Mulungu. Komabe, iye “anagwetsa misozi” mnzake wapamtima Lazaro atamwalira. (Yohane 11:35) Choncho, musamaope kulira. Kulira sikusonyeza kuti mulibe chikhulupiriro. Alicia anati: “M’kupita kwa nthawi ndinkalira kwambiri tsiku lililonse.” *

Musamadziimbe Mlandu. Karyn, amene mayi ake anamwalira iye ali ndi zaka 13, anati: “Tsiku lililonse ndisanagone, ndinkapita kuchipinda kwa mayi anga ndi kuwapsompsona. Koma tsiku lina sindinachite zimenezi. M’mawa mwake mayi anamwalira. Ndimadziimba mlandu chifukwa chosapita kuchipinda kwawo patsikuli komanso chifukwa cha zinthu zina zimene zinachitika m’mawa mwake. Bambo anga anapita kukagwira ntchito kwinakwake ndipo pochoka anauza ineyo ndi mchemwali wanga kuti tiwasamalire amayi. Koma ifeyo tinagona mochedwa ndipo m’mawa mwake sitinakawaone. Kenako nditapita kuchipinda kwawo, ndinapeza kuti sakupuma. Ndinachita mantha kwambiri chifukwa nthawi imene bambo amachoka anawasiya amayi asakudwala kwambiri.”

Mofanana ndi Karyn, mwina inunso mumadziimba mlandu chifukwa cha zimene zinachitika panthawi imene bambo kapena mayi anu anamwalira. Mwina nthawi zonse mumaganiza kuti “Ndikanatere, sakanamwalira.” ‘Mwina ndikanaitana dokotala, mwina ndinakapita kuchipinda chawo mofulumira.’ Ngati nthawi zambiri mumakhala ndi maganizo amenewa, kumbukirani izi: ‘Si kulakwa kuganiza kuti zinthu zikanakhala bwino ngati mukanayesetsa kuchita chinachake. Koma mfundo ndi yakuti, simumadziwa zimene zichitike. Choncho, palibe chifukwa chodziimbira mlandu. Inuyo simunachititse kuti mayi kapena bambo anu amwalire. *

Uzani ena mmene mukumvera. Lemba la Miyambo 12:25 limati: ‘Mawu abwino amakondweretsa.’ Ngati simuuza ena mmene mukumvera, nkhawa yanu imakula kwambiri. Koma kuuza anthu amene mumawakhulupirira kumathandiza kuti iwo akuuzeni ‘mawu okondweretsa’ komanso olimbikitsa. Choncho, mungachite bwino kutsatira malangizo awa:

Kambiranani ndi kholo lanu limene latsala. Ngakhale kuti kholo lanu limene latsala lingakhale ndi chisoni chachikulu, lingafunebe kukuthandizani. Choncho uzani kholo lanu limene latsala mmene mukumvera. Zimene mungakambirane zingakuthandizeni kwambiri kuti muthetse nkhawa zina zimene mungakhale nazo komanso zingachititse kuti muzigwirizana.

Kuti muyambe kukambirana mungachite izi: Ganizirani zinthu ziwiri kapena zitatu zimene mukufuna kudziwa zokhudza kholo lanu limene lamwalira ndiyeno pemphani kholo lanu linalo kuti mukufuna kukambirana chimodzi cha zinthu zimenezo. *

․․․․․

Uzani Anzanu Apamtima. Baibulo limanena kuti anzathu apamtima ‘anabadwira kuti atithandize pooneka tsoka.’ (Miyambo 17:17) Alicia anati: “Munthu amene sumamuganizira n’komwe ndi amene amakuthandiza. Choncho, musamachite mantha kuuza ena mmene mukumvera.” N’zoona kuti nthawi zina zimenezi zingakhale zovuta, chifukwa mwina inuyo ndi munthu winayo mungakhale ndi chisoni chachikulu. Komabe ndi bwino kuti m’kupita kwa nthawi mudzauze ena mmene mukumvera. David, yemwe bambo ake anamwalira ndi matenda a mtima iye ali ndi zaka 9, anati: “Sindinkauza wina aliyense mmene ndinkamvera. Koma ndikuona kuti ndikanauzako ena, chisoni changa chikanachepa.”

Pempherani kwa Mulungu. Mungamvenso bwino ngati ‘mutatsanulira mtima wanu’ kwa Mulungu. (Salmo 62:8) Mukamapemphera mumakhala mukupempha “Mulungu wa chitonthozo chonse, amene amatitonthoza m’masautso athu onse.”—2 Akorinto 1:3, 4.

Njira ina imene Mulungu amatitonthozera ndiyo kutipatsa mzimu wake woyera. Mzimu woyera umatithandiza kuti tikhale ndi “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tipirire panthawi ya chisoni. (2 Akorinto 4:7) Mulungu amatipatsanso “chitonthozo cha m’Malemba.” (Aroma 15:4) Choncho, mungachite bwino kupempha Mulungu kuti akupatseni mzimu wake ndipo muziwerenga uthenga wolimbikitsa wopezeka m’Mawu ake, Baibulo. (2 Atesalonika 2:16, 17) Zimathandiza kusunga malemba angapo amene mukuona kuti amakutonthozani. *

Kodi Imfa Idzatha?

Chisoni sichitha lero ndi lero. Brianne, yemwe mayi ake anamwalira iye ali ndi zaka 16, anati: “Chisoni chimatenga nthawi kuti chithe. Masiku ena ndinkalira usiku wonse. Panopa, ndimayesetsa kuganizira za malonjezo a Yehova amene adzawakwaniritse m’tsogolo, m’malo moganizira za chisoni changa. Ndimaganizira za nthawi imene ndidzakhale ndi mayi anga m’paradaiso.”

Baibulo limatitsimikizira kuti m’paradaiso “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Inunso mungaone kuti kuganizira kwambiri za paradaiso kungakuthandizeni kuti muiwale imfa ya mayi kapena bambo anu.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Ngati mukulephera kuyankha mafunsowa panopa, mungadzawayankhe nthawi ina.

^ ndime 8 M’nkhaniyi maina asinthidwa.

^ ndime 13 Si bwino kuganiza kuti muyenera kulira n’cholinga chosonyeza kuti muli ndi chisoni. Dziwani kuti anthu amasonyeza chisoni mosiyanasiyana. Mfundo yofunika ndi yakuti: Mukaona kuti m’maso mwayamba misozi, mwina imeneyo ingakhale “mphindi yakulira.”—Mlaliki 3:4.

^ ndime 15 Ngati mukupitirizabe kudziimba mlandu, uzani kholo limene latsala kapena munthu wina wamkulu za mmene mukumvera. M’kupita kwa nthawi maganizo amenewa adzatha.

^ ndime 18 Ngati munali ndi kholo limodzi lokhalo kapena kholo lanu lina limakhala kutali, mungathe kukambirana ndi munthu wina wachikulire.

^ ndime 22 Ena amatonthozedwa ndi malemba otsatirawa: Salmo 34:18; 102:17; 147:3; Yesaya 25:8; Yohane 5:28, 29.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi mungakonde kugwiritsa ntchito mfundo ziti m’nkhani ino? ․․․․․

▪ Lembani m’munsimu malemba amene angakutonthozeni mukakhala ndi chisoni. ․․․․․

[Bokosi patsamba 11]

KULIRA SI KULAKWA . . . ANTHU ENANSO ANALIRA

Abulahamu—Genesis 23:2.

Yosefe—Genesis 50:1.

Davide—2 Samueli 1:11, 12; 18:33.

Mariya, mlongo wake wa Lazaro—Yohane 11:32, 33.

Yesu—Yohane 11:35.

Mariya Mmagadala—Yohane 20:11.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]

LEMBANI MMENE MUKUMVERA

Kulemba maganizo anu okhudza mayi kapena bambo anu amene anamwalira kungakuthandizeni kwambiri kuti chisoni chanu chichepe. Pali zinthu zambiri zimene mungalembe. Zina ndi izi:

▪ Lembani zinthu zosangalatsa zimene munachita ndi kholo lanulo.

▪ Lembani zinthu zimene mukadakonda kuuza mayi kapena bambo anu asanamwalire.

▪ Ganizirani kuti muli ndi mng’ono wanu amene ali ndi chisoni chachikulu chifukwa cha imfa ya kholo lanu. Lembani zimene munganene kuti mumulimbikitse. Zimenezi zingakuthandizeni kuti chisoni chanu chichepe.

[Bokosi patsamba 13]

ZIMENE KHOLO LOTSALA LIYENERA KUDZIWA

Mkazi kapena mwamuna wanu akamwalira zimakhala zopweteka. Koma zimakhalanso zopweteka kwambiri kwa ana anu. Kodi mungatani kuti muwalimbikitse?

Musabise maganizo anu. Dziwani kuti ana anu aphunzira zinthu zambiri poona zimene inuyo mumachita. Mmene inuyo mukuchitira panthawi ya chisoni imeneyi, zingathandize anawo. Choncho, musabise maganizo anu. Ngati mumabisa maganizo anu, ana anu angachitenso chimodzimodzi. Mukamasonyeza mmene mukumvera, ana anu amaona kuti ndi bwino kusonyeza mmene akumvera kusiyana n’kubisa, ndiponso kuti si kulakwa kusonyeza kuti akhumudwa kapena akwiya.

Limbikitsani ana anu kufotokoza maganizo awo. Ndi bwino kulimbikitsa ana anu kufotokoza maganizo awo kuti mudziwe mmene akumvera. Ngati sakufuna kuti mukambirane nawo, mungaone ngati kuli koyenera kuwerengera nawo limodzi nkhaniyi. Komanso, mungawauze zinthu zosangalatsa zimene munachitira limodzi ndi mkazi kapena mwamuna wanuyo. Auzeni kuti nanunso muli ndi chisoni chachikulu. Ana anu akakuonani mukufotokoza maganizo anu momasuka, iwonso amachita zomwezo.

Pemphani ena kuti akuthandizeni. Tikudziwa kuti mukuyesetsa kwambiri kuthandiza ana anu panthawi yovuta imeneyi. Koma muyenera kukumbukira kuti inunso mwataya mwamuna kapena mkazi amene mumamukonda kwambiri. Ndipo chifukwa cha chisoni, nthawi zina mungalephere kuchita zinthu mwanzeru. (Miyambo 24:10) Choncho, mufunikira kupempha achibale kapena anzanu ena kuti akuthandizeni. Kupempha ena kuti akuthandizeni ndi nzeru, chifukwa lemba la Miyambo 11:2 limati: “Nzeru ili ndi odzichepetsa.”

Komanso dziwani kuti Yehova Mulungu ndi amene angakuthandizeni kwambiri, chifukwa iye amalonjeza anthu amene amamulambira kuti: “Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usawope ndidzakuthandiza iwe.”—Yesaya 41:13.

[Chithunzi patsamba 11]

Chisoni chingakhale ngati mafunde, chimatha kuyamba kapena kutha mosayembekezereka