Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tsankho Limayamba Bwanji?

Kodi Tsankho Limayamba Bwanji?

Kodi Tsankho Limayamba Bwanji?

“Anthu onse amabadwa ndi ufulu wofanana ndipo ayenera kupatsidwa ulemu. Munthu aliyense ali ndi nzeru ndiponso chikumbumtima ndipo tonse tiyenera kuonana monga pachibale.”—Mfundo yoyamba m’chikalata cha mfundo za ufulu wa anthu.

NGAKHALE kuti anthu ena ali ndi maganizo abwino amenewa, anthu ambiri akupitiriza kuchita tsankho. Zimenezi ndi umboni wakuti anthu si angwiro komanso kuti tikukhala m’masiku oipa. (Salmo 51:5) Komabe, tili ndi chiyembekezo chakuti zinthu zingathe kusintha. N’zoona kuti sitingathetseretu tsankho m’dzikoli, koma tingayesetse kuthetsa maganizo aliwonse atsankho amene tingakhale nawo m’mitima yathu.

Choyamba, tiyenera kupeweratu maganizo akuti ifeyo sitingachite tsankho. Buku lina lonena za tsankho linati: “Mfundo zotsatirazi ndi zofunika kwambiri pothetsa tsankho: (1) palibe munthu amene angakhaliretu wopanda tsankho, (2) munthu aliyense afunika kudzifufuza kuti aone ngati ali ndi maganizo enaake omwe ndi atsankho ndipo ayenera kuyesetsa kuwathetsa, (3) ngati munthu amene ali ndi tsankho atathandizidwa, angathe kuthetsa maganizowo.”—Understanding Prejudice and Discrimination.

Maphunziro amathandiza kwambiri kuthetsa tsankho. Ngati titaphunzitsidwa bwino, tingathe kudziwa zinthu zimene zimayambitsa tsankho, tingamadzifufuze kuti tione ngati tili ndi maganizo alionse atsankho, komanso tingamachite zinthu mwanzeru ngati ena akutisankha.

Zinthu Zimene Zimayambitsa Tsankho

Anthu atsankho amatsutsa kapena kukana mfundo zimene sizikugwirizana ndi maganizo awo. Munthu atha kukhala watsankho chifukwa cha mmene analeredwera kapena chifukwa chotsanzira anthu ena amene amanyoza anthu amitundu ina. Munthu angakhalenso watsankho chifukwa chokonda kwambiri dziko lake kapena chifukwa cha zimene zipembedzo zonyenga zimaphunzitsa. Enanso amachita tsankho chifukwa chonyada. Mukamawerenga mfundo za m’Baibulo zotsatirazi, ganizirani zinthu zimene mungafunikire kusintha.

Anthu ocheza nawo. Mwachibadwa, anthu amakonda kucheza ndipo palibe cholakwika ndi zimenezi. Baibulo limati: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” (Miyambo 18:1, NW) Komabe tiyenera kusankha mwanzeru anthu ocheza nawo, chifukwa ena angatiphunzitse zinthu zoipa. Makolo anzeru ayenera kuonetsetsa kuti ana awo akucheza ndi anthu amakhalidwe abwino. Ofufuza apeza kuti ana azaka zitatu angathe kukhala atsankho chifukwa chotengera anthu ena. Choncho, makolo ayenera kuyesetsa kupewa tsankho, chifukwa zambiri zimene ana amachita amatengera makolo awo.

Zimene Baibulo limanena. “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” (Miyambo 22:6) “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Ngati ndinu kholo, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikuphunzitsa ana anga zinthu zimene Mulungu amaona kuti n’zabwino? Kodi ndimacheza ndi anthu amakhalidwe abwino? Kodi ineyo ndimalimbikitsa ena kuchita zinthu zabwino?’—Miyambo 2:1-9.

Kukonda kwambiri dziko. Munthu amene amakonda kwambiri dziko lake amaona kuti dziko lakelo ndi lapamwamba kwambiri kuposa mayiko ena, ndipo amafuna kuti anthu ena azitsatira chikhalidwe komanso zinthu zimene anthu a m’dziko lake amakonda. Pulofesa wina wa maphunziro andale, dzina lake Ivo Duchacek, anati: “Kukondetsa kwambiri dziko kumagawanitsa anthu. Munthu asanaganize kuti anthu tonsefe ndi amodzi amayamba waganizira za kumene anachokera, kaya ndi ku America, Russia, China, Egypt kapena Peru.” Munthu wina yemwe anali mlembi wamkulu wa bungwe la UN anati: “Mavuto ambiri amene timakumana nawo masiku ano amayamba chifukwa chokhala ndi maganizo olakwika ndipo anthu angakhale ndi maganizo amenewa mosadziwa. Ambiri amene amakhala ndi maganizo olakwikawa ndi amene amakonda kwambiri dziko lawo, ndipo amaliikira kumbuyo ngakhale likuchita zoipa.

Zimene Baibulo limanena. “Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko [anthu onse] mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu ulionse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Dzifunseni kuti, ‘Ngati Mulungu alibe tsankho ndipo amakonda anthu amitundu yonse kuphatikizapo ineyo, kodi si bwino kuti nanenso nditengere chitsanzo chake?’

Kusankhana mitundu. Buku lina lotanthauzira mawu limati: “Anthu amene amasankhana mitundu ndi amene amakhulupirira kuti mitundu ina ya anthu imakhala yanzeru komanso yodziwa zinthu kuposa mitundu ina.” Koma pa mfundo imeneyi buku linanso linati: “Asayansi sanapeze umboni uliwonse wosonyeza kuti mitundu ina ya anthu ndi yanzeru kuposa ina.” (The World Book Encyclopedia) Choncho kusankhana mitundu kumayambitsa zinthu zopanda chilungamo, monga kuzunza anthu amitundu ina pazifukwa zosamveka.

Zimene Baibulo limanena. “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) “Kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu.” (Machitidwe 17:26) “Yehova saona monga awona munthu; pakuti munthu ayang’ana chowoneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:7) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimaona anthu onse monga mmene Mulungu amawaonera? Kodi ndimayesetsa kucheza ndi anthu amitundu ina kuti ndidziwe zinthu zimene amakonda?’ Tikamacheza ndi anthu amtundu wina timayamba kuwamvetsa bwino ndipo zimenezi zimachititsa kuti tisamawaganizire zoipa.

Chipembedzo. Buku lina lonena za tsankho linati: “Anthu akamagwiritsa ntchito chipembedzo pokwaniritsa zolinga zawo [zadyera] kapena polimbikitsa mfundo za mtundu wawo, zinthu siziyenda bwino. Zikatero chipembedzo chimayambitsa kusankhana mitundu.” (The Nature of Prejudice) Ndipo kenako anthu opembedza amasintha n’kukhala atsankho. Umboni wa zimenezi umaonekera m’matchalitchi ambiri amene amakhala ndi anthu amtundu umodzi, ndipo matchalitchiwa amayambitsa udani, chiwawa ndi uchigawenga.

Zimene Baibulo limanena. “Nzeru yochokera kumwamba . . . ndi yamtendere, yololera, . . . yopanda tsankho.” (Yakobe 3:17) “Olambira oona adzalambira Atate ndi mzimu ndi choonadi, pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.” (Yohane 4:23) ‘Kondani adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.’ (Mateyo 5:44) Dzifunseni kuti: ‘Kodi chipembedzo changa chimalimbikitsa kukonda anthu onse, ngakhale adani anga? Kodi m’chipembedzo changa muli anthu osiyanasiyana posatengera mtundu, chuma, kapena maphunziro?’

Kunyada. Nthawi zina anthu angamachite tsankho chifukwa chonyada. Mwachitsanzo, kunyada kungapangitse munthu kudziona wapamwamba kwambiri, kudana ndi anthu amene si ophunzira kwambiri kapena anthu osauka. Kunyada kungachititsenso munthu kukhulupirira bodza lakuti mtundu kapena fuko linalake ndi lapamwamba kuposa linzake. Mwachitsanzo, Adolf Hitler, yemwe anali mtsogoleri wankhanza wa dziko la Germany, ankalimbikitsa anthu amtundu wake kuti azidziona apamwamba ndipo ankazunza anthu amitundu ina. Ankachita zimenezi n’cholinga choti anthu ambiri azimukonda.

Zimene Baibulo limanena. “Yense wonyada mtima anyansa Yehova.” (Miyambo 16:5) “Musachite kanthu kalikonse ndi mzimu wandewu kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, mukumaona ena kukhala okuposani.” (Afilipi 2:3) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakonda kunena mawu oyamikira mtundu wanga, kapena onyoza anthu amitundu ina? Kodi ndimachitira nsanje anthu amene ali ndi luso linalake, kapena ndimawayamikira?’

Baibulo limatichenjeza kuti: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Choncho, mudziona mtima wanu wophiphiritsa ngati mphatso yamtengo wapatali ndipo musalole china chilichonse kuuwononga. M’malomwake uphunzitseni nzeru yochokera kwa Mulungu. Mukatero, ‘kulingalira kudzakudikirani, Kuzindikira kudzakuchinjirizani; kukupulumutsani ku njira yoipa, kwa anthu onena zokhota.’—Miyambo 2:10-12.

Koma kodi mungatani ngati anthu ena amakusankhani? Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Tikamacheza ndi anthu amtundu wina timayamba kuwamvetsa bwino ndipo timasiya kuwaganizira zoipa