Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Pakali pano dziko la Russia lili ndi matani 2 biliyoni a zinyalala zowononga chilengedwe, ndipo akusowa kokazitaya.”—RIA NOVOSTI, RUSSIA.

“Kuyambira chaka cha 2000, chiwerengero cha anthu amene amalanda sitima zapanyanja chachuluka. Mwachitsanzo, m’chaka cha 2007, panachitika ziwembu zoterezi zokwana 263.”—THE WALL STREET JOURNAL, U.S.A.

Si Bwino Kumwa Mowa Muli Woyembekezera

Chaka chilichonse ku Germany, pafupifupi ana 10,000 amabadwa ndi matenda chifukwa chakuti mayi awo ankamwa mowa ali ndi pakati. (Süddeutsche Zeitung) Pafupifupi ana 4,000 mwa ana amenewa amakhala ndi chilema moyo wawo wonse. Mayi wina woona za mavuto okhudzana ndi kumwa mowa, dzina lake Sabine Bätzing, anati: “Mayi woyembekezera sayenera kumwa mowa ngakhale pang’ono. Madokotala, azamba, ndiponso amayi oyembekezera ayenera kudziwa kuti kumwa mowa ngakhale pang’ono kungawononge mwana m’njira zambiri.”

Anthu amene Amalima Amakhala ndi Thanzi Labwino

Magazini ina inati: “Anthu ofufuza apeza kuti kulima nokha zakudya, kaya zikhale zambiri kapena zochepa, kumathandiza kuti mukhale ndi thanzi labwino.” (Psychology Today) Ofufuzawa anapeza kuti munthu akamalima, amapuma mpweya umene umakhala ndi tizilombo tamunthaka, tomwe timathandiza kuti chitetezo cha m’thupi chikhale champhamvu.” Magaziniyi inanenanso kuti: “Mpweya umenewu ndi wothandiza kwambiri pa chitetezo cha m’thupi kuposa masamba kapena zipatso zimene munthu angalime pamalowo.”

Mbalame Zouluka Ulendo Wautali

Asayansi ena ku United States, ananena kuti pali “mbalame zinazake zapamtunda zimene zimauluka ulendo wautali kwambiri osapumira.” Pogwiritsa ntchito setilaiti, asayansiwa anaona mbalamezi zikudutsa panyanja ya Pacific. Magazini ina inanena kuti mbalame imodzi yaikazi inayenda ulendo wautali makilomita 11,650 kwa masiku 8 osapumira, kuchokera ku Alaska kupita ku New Zealand. Mbalamezi zimalemera magalamu 700 koma pomaliza ulendowu, mbalameyi inali itawonda kwambiri moti inkalemera magalamu 350. (The Week) Mbalamezi zikamabwerera ku Alaska kuchokera ku New Zealand zimadutsa ku China, ndipo ulendowu ndi wa makilomita pafupifupi 29,000. Asayansi aja ananena kuti “ngati pa ulendo umodzi mbalamezi zimauluka makilomita 29,000, ndiye kuti pamoyo wawo wonse zingauluke mtunda wa makilomita 463,000.”

Anthu Akuba Zomera Zam’chipululu

Anthu akuba kwambiri zomera zinazake zam’chipululu zofanana ndi nkhadze kumalo ena osamalira zachilengedwe ku Arizona, U.S.A. Mkulu wina wa ku dipatimenti ya zaulimi ku Arizona dzina lake Jim McGinnis, anati: “Aliyense akufuna kukhala ndi zomera zimenezi panyumba pake.” Choncho, si zachilendo kuona galimoto zitanyamula zomerazi kuchokera m’chipululu. Anthu akuba amakonda kuba zomera zazitali kuyambira mita imodzi mpaka mamita awiri, zomwe amatha kuzigulitsa madola 1,000 kapena kuposerapo. Pofuna kugwira akubawa, akuluakulu a boma akuganiza zoika tizipangizo tinatake takompyuta m’zomerazo cholinga choti azitha kudziwa kumene zili pogwiritsa ntchito kompyuta.