Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kamvuluvulu Wapanyanja

Kamvuluvulu Wapanyanja

Kamvuluvulu Wapanyanja

▪ Kodi munayamba mwaonapo kamvuluvulu wapanyanja? Kamvuluvulu wotere anachitikapo ku Tahiti, pa December 25, 2005. Anayamba chifukwa cha chimphepo chachikulu chimene chinawomba panyanja n’kupanga kamvuluvulu amene anali wamtali kwambiri ngati chipilala chachikulu, choyambira pamwamba pa nyanja mpaka kukafika kumitambo. Kamvuluvuluyu anatha patapita mphindi 30.

Ena amaganiza kuti kamvuluvulu ngati ameneyu, amayamba chifukwa cha mphepo yamkuntho, koma zoona zake n’zakuti mphepo imene imayambitsa kamvuluvuluyu imakhala yocheperapo mphamvu poyerekeza ndi mphepo yamkuntho. Nthawi zambiri kamvuluvuluyu amangochitika kwa mphindi 10 ngakhale kuti nthawi zina amapitirira mpaka kufika ola limodzi. Popeza kuti kamvuluvuluyu amachitika panyanja, nthawi zambiri zimakhala zovuta kuti akatswiri a zanyengo amujambule. Ichi n’chifukwa chake akatswiriwa sadziwa zambiri zokhudza kamvuluvuluyu. Anthu ena amene anamuonapo akuti amabwera ndi chimkokomo chachikulu ngati chimene chimamveka sitima ikamabwera.

Nthawi ina wolemba masalmo anali ndi chisoni chachikulu mumtima mwake ndipo iye anafotokoza mmene ankamvera. Iye anati: “Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya, pa mkokomo wa mathithi anu: Mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.” (Salmo 42:7) Sitikudziwa ngati wolemba masalmo ameneyu amanena za kamvuluvuluyu palembali, komabe zimene ananena n’zofanana ndi zimene kamvuluvuluyu amachita. Iye ananena kuti anali ndi chisoni chachikulu ndipo ‘anazingwa m’kati mwake.’ Komabe, iye anapeza chitonthozo kwa Mulungu, chifukwa anadziuza yekha kuti: “Yembekeza Mulungu: Pakuti ndidzam’lemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.”—Salmo 42:11.

Mofanana ndi wolemba masalmoyu, ifenso tingakumane ndi mavuto ofanana ndi kamvuluvulu wapanyanja. Zikatere ndi bwino kuyembekezera Mulungu, ndipo iye adzatipulumutsa.