Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Achinyamata Angapeze Bwanji Thandizo?

Kodi Achinyamata Angapeze Bwanji Thandizo?

Kodi Achinyamata Angapeze Bwanji Thandizo?

Zikanakhala kuti m’dzikoli zinthu zonse zili bwino, bwenzi makolo onse akuphunzitsa ana awo ndi kuwapatsa malangizo abwino. Bwenzi akulankhula nawo bwino, kuwerenga nawo Baibulo, kudya nawo pamodzi ndiponso kuwamvetsa zofuna zawo. Komabe, makolo si anthu angwiro. Baibulo limati: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 3:23.

Ngati ndinu wachinyamata, mwina mumaona kuti kunyumba kwanu kuli mavuto ambiri. Ngati zili choncho, pali zambiri zomwe mungachite kuti muchepetse nkhawa ndiponso kuti muzisangalala. Taonani mmene mfundo za m’Baibulo zingakuthandizireni.

Mfundo Yoyamba

Muzicheza ndi Ena M’malo Mokhala Nokha

Baibulo limati: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” (Miyambo 18:1, NW) Achinyamata ena sakonda kukhala pagulu, m’malomwake amakonda kukhala okhaokha n’kumaonera TV kapena kuchita masewera a pakompyuta. Ena sakonda kukhala pagulu chifukwa chakuti ndi amanyazi kwambiri. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Elizabeth ananena kuti: “Ndimachita manyazi nthawi zonse. Manyazi angawa amandichititsa kuti ndizichita mantha. Ndimaopa kucheza ndi anthu.”

Kodi Elizabeth amatani ndi vuto lakeli? Iye ndi wa Mboni za Yehova, ndipo nthawi zonse amapita kumisonkhano yachikhristu. Elizabeth anati: “Ngakhale kuti ndine wamanyazi, ndimayesetsa kulankhula ndi munthu mmodzi nthawi zonse ndikapita kumisonkhano. Ndikalephera kuchita zimenezi, sindikhumudwa. M’malomwake, ndimasangalala ndi zimene ndachita bwino. Ndikuona kuti kuyesetsa kudziwana bwino ndi anthu kwandithandiza kwambiri.”

Inuyo mungachite bwino kulemba maina a anthu awiri kapena atatu amene mukufuna kuti mudziwane nawo bwinobwino. Mlungu wotsatira yesetsani kudziwana bwino ndi mmodzi mwa anthuwo. Ndiyeno, lembani chinthu chimodzi chabwino chimene mukufuna kuti mudzapangire anthuwo m’mwezi wotsatira ndipo yesetsani kuchitadi zimenezo.—Machitidwe 20:35.

Dziwani kuti munthu amene amapewa kucheza ndi anthu, amakhala ndi nkhawa yaikulu. Baibulo limalangiza kuti: “Musasamale zofuna zanu zokha, koma musamalenso zofuna za ena.” (Afilipi 2:4) Kutsatira malangizo amenewa mukakhala ndi achibale anu komanso anthu ena kungakuthandizeni kuti musamakhale ndi nkhawa yaikulu chifukwa cha mavuto anu ndiponso mungadziwe mmene mungawathetsere.

Mfundo Yachiwiri

Thawani Dama

Baibulo limati: “Thawani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu angachite ndi la kunja kwa thupi lake, koma amene amachita dama amachimwira thupi lake la iye mwini.” (1 Akorinto 6:18) Masiku ano achinyamata ambiri amachita zachiwerewere. Kodi inuyo mungapewe bwanji kuchita zimenezi?

Choyamba, muyenera kuganizira bwinobwino nkhani imeneyi musanakumane ndi vutolo. Baibulo limati: “Wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) Mtsikana wina wa ku South Africa, dzina lake Mbali, anati: “Ndili kusukulu yasekondale, mnyamata wina wa m’kalasi mwathu nthawi zonse ankandiuza kuti ndigone naye. Atsikana ena a m’kalasi mwathu ankandikakamiza kuti ndikhale naye pachibwenzi chifukwa anali wokongola, ankachita zinthu motsogola ndiponso ankasewera bwino mpira. Analidi wokongola, koma ndinali nditatsimikiza kutsatira mfundo za m’Baibulo. Anzangawo ankaona kuti panalibe vuto lililonse kugona naye. Koma ineyo ndinkadziwa kuti kuchita zimenezi n’kulakwa ndipo ndinali nditadziwiratu zochita pankhaniyi.”

Chachiwiri, muzipemphera kuti Mulungu akuthandizeni kupitiriza kutsatira mfundo za makhalidwe abwino. Mtsikana wina wa ku England, dzina lake Maggie, anati: “Pemphero limandithandiza kwambiri kuti ndithe kukana kuchita zachiwerewere. Ndimaona kuti sindingathe kupewa vuto limeneli popanda thandizo la Mulungu. Ndimakambirananso nkhaniyi ndi makolo anga ndipo nthawi zina ndimakambirana ndi anzanga amene amakonda Mulungu.”

Mfundo Yachitatu

Muzikonda Makolo Anu

Baibulo limati: “Nonsenu mukhale a maganizo amodzi, omverana chisoni, okonda abale, a chifundo chachikulu.” (1 Petulo 3:8) Simungathe kuletsa makolo anu kuti asapatukane kapena kuti onse asamapite kuntchito. Komabe, mungayesetse kuti zimenezi zisawononge ubale womwe ulipo pakati pa inuyo ndi makolo anu. Njira imodzi imene mungachepetsere nkhawa ndiyo kukonda makolo anu ndiponso kumvetsa mavuto amene akukumana nawo.

Mtsikana wina dzina lake Amber amachita zimene tafotokozazi. Iye nthawi zina amasemphana maganizo ndiponso kukhumudwitsana ndi mayi ake. Komabe, iye anati: “Mayi anga apirira zinthu zambiri pamoyo wawo. Akwanitsa kulera ana anayi tonse. Nthawi zonse amaonetsetsa kuti tili ndi malo ogona, chakudya ndi zovala. Ndimasirira kwambiri khama lawo, ndipo ndimafunitsitsa kuti inenso nditengere chitsanzo chawo cha kupirira pokumana ndi mavuto.”

Nanunso mungathe kupirira mavuto anu mukamayesetsa kudziwa ndiponso kumvetsa mavuto amene makolo anu amakumana nawo. Kuchita zimenezi kungakuthandizeninso kuti mudziwe ndiponso kutengera makhalidwe abwino a makolo anu.

Baibulo Lili ndi Malangizo Odalirika

Mfundo zimene tatchulazi ndi zina mwa mfundo zothandiza zimene zimapezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Mukamakonda kuwerenga Baibulo, mudzadziwa kwambiri mfundo zodalirika zimene Baibulo lili nazo. *

Njira ina imene mungadziwire zimene Baibulo limaphunzitsa ndiyo kusonkhana ndi Mboni za Yehova komanso kupempha kuti muziphunzira nawo Baibulo. Anthu amenewa akhoza kukhala mabwenzi anu enieni amene angakuthandizeni mukakumana ndi mavuto. Ndiponso angakuthandizeni kuti muzigwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pamoyo wanu. N’zoona kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo si kophweka. Koma mukachita zimenezi, mudzapindula kwambiri pamoyo wanu.—Yesaya 48:17, 18.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lili ndi mfundo zabwino za m’Baibulo zimene zingathandize achinyamata kuti athane ndi mavuto amene amakumana nawo. Mfundo zina zimapezeka pa Intaneti, pa adiresi iyi: www.pr418.com.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 8, 9]

Zimene Makolo Amafunika Kuchitira Ana Awo

Muzicheza Nawo: Yehova Mulungu anauza makolo achiisiraeli kuti azilankhula ndi ana awo ‘pokhala pansi m’nyumba zawo, ndi poyenda panjira.’ (Deuteronomo 6:6, 7) Zimenezi zimafuna kuti makolo azikhala ndi nthawi yocheza ndi ana awo. Yesu ankaona kuti ana amafunikira nthawi yocheza nawo. Mwachitsanzo, panthawi ina “anthu anayamba kum’bweretsera ana aang’ono kuti awaike manja.” Kodi Yesu anatani? “Anatenga anawo m’manja mwake ndi kuyamba kuwadalitsa.” (Maliko 10:13, 16) Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa makolo.

Muzikambirana Momasuka: Baibulo limati: “Zolingalira zizimidwa popanda upo.” (Miyambo 15:22) Kukambirana momasuka n’kofunika ana akakhala aang’ono. Koma n’kofunika kwambiri pamene anawo afika zaka zapakati pa 13 ndi 19, chifukwa nthawi imeneyi achinyamata sakhala nthawi yaitali panyumba koma nthawi zambiri amakhala ndi anzawo akusukulu kapena anzawo ena. Ngati makolo sakambirana ndi ana awo momasuka, anawo zimawavuta kuuza makolo awowo zakukhosi kwawo.

Muziwadzudzula Moyenerera: Lemba la Miyambo 15:5 limati: “Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake; koma wosamalira chidzudzulo amachenjera.” Mawu akuti chidzudzulo, amatanthauza kuwongolera kapena kuphunzitsa, ngakhale kuti nthawi zina pangafunike kupereka chilango. Wachinyamata sangasinthe ngati sanapatsidwe chilango. Komabe makolo ayenera kukhala ndi malire popereka chilangocho. Ayenera kupewa kukhwimitsa zinthu kwambiri mpaka kukhumudwitsa ana awo n’kuyamba kumadziona kuti ndi anthu osafunika. (Akolose 3:21) Komabe, makolo sayenera kulekerera ana awo, mpaka kulephera kuwaphunzitsa. Kuchita zinthu mowalekerera kungabweretse mavuto ambiri. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 29 Kuti mudziwe zambiri, onani buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, mutu 5 ndi 6. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.