Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Oipa Adzakapsa Kumoto?

Kodi Anthu Oipa Adzakapsa Kumoto?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Anthu Oipa Adzakapsa Kumoto?

GERTRUDE anali mlaliki wa tchalitchi cha Pentekosito ndipo ankakhulupirira kuti anthu oipa amakapsa kumoto. Iye sankagwirizana ndi maganizo akuti kulibe moto chifukwa ankaona kuti zimenezi zitakhala zoona, ndiye kuti Mulungu si wachilungamo. Iye ankaganizanso kuti kutakhala kuti kulibe moto, ndiye kuti anthu azipitiriza kuchita zinthu zoipa kwambiri chifukwa aziona kuti sadzalangidwa. Gertrude sankafuna kusintha maganizo ake pankhani yakuti anthu adzakapsa kumoto. Iye anati: “Ndingasiye kulambira Mulungu zitakhala kuti anthu oipa sadzakapsa kumoto.”

Koma kodi n’zoonadi kuti anthu oipa adzakapsa kumoto monga mmene zipembedzo zambiri zimaphunzitsira? Ngati zimenezi si zoona, kodi iwo adzalandira chilango chotani?

Chilango Choyamba Chimene Mulungu Anapereka

Baibulo limanena kuti pachiyambi Mulungu analenga anthu awiri angwiro, Adamu ndi Hava. (Genesis 1:27; Deuteronomo 32:4) Iye anawaika anthuwo m’munda wokongola ndipo anawapatsa mwayi wokhala ndi moyo kwamuyaya. Komabe, Mulungu analamula Adamu kuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.”—Genesis 2:16, 17.

N’zomvetsa chisoni kuti makolo athu oyambirirawa analephera kukhala okhulupirika kwa Mulungu posamvera lamulo losavuta limeneli. Choncho, Mlengi anawapatsa chilango cha imfa. Iye anauza Adamu kuti: “M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: Chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: Chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.”—Genesis 3:19.

Zikanakhala kuti Adamu ndi Hava akapsa kumoto, kodi Mulungu sakanawachenjezeratu za chilangochi? Koma Mulungu sananene kuti adzalanga Adamu ndi Hava akafa. Zinali zosatheka kuti Mulungu awalange iwo atafa chifukwa munthu akafa, wafa basi. Baibulo limafotokoza mfundo imeneyi momveka kuti: ‘Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.’Ezekieli 18:4. *

Mlengi wathu ndi amene anatipatsa moyo, choncho amadziwa zonse zokhudza moyo wathu komanso zimene zimachitika munthu akafa. Mawu ake amanena momveka bwino kuti: “Akufa sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Choncho, Adamu ndi Hava sanapite kumoto atamwalira. Iwo anabwerera kufumbi ndipo “sadziwa kanthu bi.”

Kodi Munthu Akafa Amakalangidwa Kwinakwake?

Lemba la Aroma 5:12 limati: “Monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo, imfayo nifalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” Choncho kodi ndi zomveka kuganiza kuti anthu ochimwa amakapsa kumoto, pamene Adamu, yemwe anachititsa kuti anthu onse azifa, anangofa n’kusanduka fumbi?—1 Akorinto 15:22.

Zimene zinachitikira Adamu ndi zimenenso zimachitikira anthu ochimwa. Baibulo limati: “Malipiro a uchimo ndiwo imfa.” Choncho munthu amene wafa ‘amamasuka ku uchimo wake.’ (Aroma 6:7, 23) Mwina mungafunse kuti, ‘Ngati anthu abwino ndi oipa omwe salandira chilango akafa, ndiyeno kodi chilungamo cha Mulungu chili pati?’

Chilungamo cha Mulungu

Mulungu atalenga mwamuna ndi mkazi oyamba aja, anawauza kuti abereke ana ndi kusamalira dziko lapansi. (Genesis 1:28) Cholinga chimenechi sichinasinthe. Patapita nthawi, Mulungu ananena kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.

Onani kuti anthu olungama adzakhala padziko lapansi kosatha. Iwo sadzadwala ndipo adzakhala ndi moyo wosangalala. Zimene Mulungu anafuna pachiyambi kuti padziko lapansi pakhale anthu olungama okhaokha zidzachitika. Zimenezi zidzachitika Mulungu akadzawononga dziko la Satanali n’kubweretsa dziko latsopano.—Yesaya 55:11; Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:4.

Anthu ambirimbiri amene anafa asanaphunzire malamulo a Mulungu adzaukitsidwa ndipo adzapatsidwa malangizo owathandiza kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu. (Yesaya 11:9; Yohane 5:28, 29) Koma aliyense amene adzaphwanye malamulo a Mulungu adzafa “imfa yachiwiri.” Zimenezi zikutanthauza kuti anthuwo akadzafa sadzaukanso.—Chivumbulutso 21:8; Yeremiya 51:57.

Choncho, n’zoonekeratu kuti Yehova, yemwe ndi Mulungu wachikondi, sadzawotcha anthu kumoto. (1 Yohane 4:8) Ndiponso sadzalekerera oipa. N’chifukwa chake lemba la Salmo 145:20, limatitsimikizira kuti: “Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawawononga.” Kodi chimenechi si chikondi komanso chilungamo?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 M’Baibulo mawu akuti moyo amatanthauza munthu yense osati mzimu wake. Lemba la Genesis 2:7 limati: “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.”

KODI MUNAYAMBA MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi chimachitika n’chiyani munthu akafa?—Genesis 3:19.

▪ Kodi anthu akufa amadziwa chilichonse?—Mlaliki 9:5.

▪ Kodi Mulungu adzawapatsa chilango chotani anthu oipa?—Salmo 145:20.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

“Akufa sadziwa kanthu bi.”—Mlaliki 9:5

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

Photo: www.comstock.com