Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Zimene Achinyamata Amadzifunsa Kodi Ndingatani Ngati M’bale Wanga Wadzipha? (June 2008) Mchemwali wanga asanamwalire, anavutika ndi matenda a maganizo kwa zaka zisanu. Chifukwa chakuti ndinkamuona mmene ankavutikira, ndinkaganiza kuti, ‘moyo wake unali wa mavuto okhaokha.’ Koma nkhani ya mu Galamukani! imeneyi inandithandiza kuti ndiziyesetsa kuganizira zinthu zabwino m’malo moganizira zinthu zoipa. Ndikakumbukira zabwino zomwe zinachitika iye akudwala ndimaona kuti si zoona kuti “moyo wake unali wa mavuto okhaokha.” Nthawi zambiri iye ankasangalala.

S. Y., Japan

Zimene Achinyamata Amadzifunsa N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Sandikhulupirira? (April 2008) Nditawerenga ndiponso kuyamba kutsatira mfundo za m’Baibulo za mu Galamukani! imeneyi, ndinazindikira kuti nzeru komanso kukhulupirirana zimayamba pang’onopang’ono ngati kukwera masitepe. Ndinazindikira kuti ndinafunika kusonyeza makolo anga kuti ndine wodalirika kuti iwowo ayambe kundipatsa ufulu wowonjezereka. Ndinayamba kugwira ntchito zonse zapanyumba zimene ndapatsidwa komanso kulemba homuweki. Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani ngati imeneyi.

T. L., United States

Vuto Lokhala Alubino (July 2008) Ineyo ndili ndi vuto limeneli, ndipo poyamba nkhaniyi ndinasangalala nayo. Koma nditaiwerenga yonse sindinasangalale kuona kuti munalemba mawu akuti “alubino” mobwerezabwereza. Mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponyoza anthu amene ali ndi vuto limeneli.

A. L., United States

Yankho la Galamukani!: Tikupepesa owerenga athu onse amene sanasangalale ndi mawuwa. Tinagwiritsa ntchito mawuwa chifukwa chakuti ndi amene amagwiritsidwa ntchito ndi madokotala. Tikudziwa kuti anthu ena amagwiritsa ntchito mawuwa monyoza. Komabe anthu ena ambiri amene ali ndi vutoli sakhumudwa ndi mawuwa. Ndipo si cholinga chathu kunyoza munthu aliyense.

Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani imeneyi, inenso ndine alubino ngati John amene mwamutchula m’nkhaniyi. Ndinasangalala kuti nkhani yanu inali yoona ndiponso yophunzitsa. Nkhaniyi yathandiza kuti anzanga amvetse vuto langa.

T. M., United States

Chikondi Champhamvu Kuposa Mphepo Yamkuntho (August 2008) Nkhani ngati zimenezi zimandithandiza kuti ndizidalira kwambiri Mulungu m’malo modera nkhawa ndi zimene zichitike m’tsogolo. Zaka zitatu m’mbuyomu a Mboni za Yehova anzanga anatithandiza mwamsanga nyumba ya makolo anga, omwe si Mboni, itawonongeka ndi madzi osefukira. Ndikuthokoza Yehova chifukwa chakuti ndili m’gulu lake.

D. W., Poland

Mbewu ya Chimanga N’njodabwitsa (August 2008) Panyumba pathu tinabzala chimanga koma chimanga chilichonse chimene tinakolola chinali chamagwelu. Titawerenga nkhani yanuyi tinazindikira kuti izi zinali choncho chifukwa chakuti tinkabzala chimanga chochepa. Tinazindikira kuti chimanga chikakhala chochepa, sipakhala mungu wokwanira kuti chimangacho chibereke bwino ngati mmene zimakhalira ndi munda waukulu. Chaka chatha tinkatenga mungu wa pangayaye za chimanga n’kuika pa nyenje za chimanga china ndipo zimenezi zinathandiza kuti pakhale chimanga chopanda magwelu. Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhaniyi.

R. W., Japan