Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugwiritsitsa Dzanja Lamanja la Mulungu

Kugwiritsitsa Dzanja Lamanja la Mulungu

Kugwiritsitsa Dzanja Lamanja la Mulungu

▪ Jezreel, yemwe amakhala ku Mexico, anabadwa ndi matenda amene amachititsa kuti khungu lizisupuka ndiponso kulimba. Iye anati: “Matendawa amachititsa kuti ndisamaoneke bwino, ngakhale kuti si opatsirana.”

Kuyambira ali mwana, Jezreel wakhala akulandira chithandizo m’zipatala zosiyanasiyana. Ali ndi zaka ziwiri, anagonekedwa m’chipatala ndipo anaikidwa m’chipinda chayekha chomwe ankapoperamo mankhwala n’cholinga choti khungu lake lisagwidwe ndi matenda ena. Komabe iye sanachire. Ataona kuti sakuchira anangomupatsa malangizo omuthandiza kuti asamakhumudwe anthu akamamusala.

Anthu amene amaganiza kuti matenda a Jezreel ndi opatsirana amamusala. Limeneli linali vuto kwambiri ali mwana chifukwa anzake ankamuthawa akafuna kucheza nawo. Jezreel anati: “Ana ena ankandiseka ndiponso kundipatsa maina achipongwe, monga Malemu kapena Mzukwa.”

Komabe, chifukwa chakuti matendawa amaonekera kwa anthu, Jezreel amapeza mwayi wowauza mfundo za m’Baibulo zimene amakhulupirira. Nthawi zambiri, anthu amafunsa kuti adziwe ngati anapsa ndi moto. Iye akayankha kuti sanapse ndi moto, amamufunsa chimene chinachitika kuti akhale ndi khungu lotero. Iye amawauza kuti ali ndi matenda apakhungu amene panopa alibe mankhwala.

Ndipo amawauzanso kuti: “Ndikuyembekezera kuti ndidzachira Yehova Mulungu akadzakwaniritsa lonjezo lake lakuti anthu amene amamumvera akhale m’dziko latsopano lopanda matenda ndi zopweteka zilizonse.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Zimenezi zathandiza Jezreel kuyamba kuphunzitsa anthu Baibulo, ndipo anthu ambiri amene wawaphunzitsa abatizidwa n’kukhala Mboni za Yehova.

Jezreel anati: “Ndimathokoza kuti ndinabadwira m’banja lachikhristu. Ndipo Chifukwa chokhala wa Mboni za Yehova, ndili ndi anzanga ambiri apamtima. Anzangawa sandisala chifukwa cha maonekedwe anga. Ndinabatizidwa ndili ndi zaka 17. Panopa papita zaka 14 ndipo ndakhala ndikutumikira Mlengi wathu m’njira zambiri.”

Jezreel amakonda kwambiri mawu a Yehova opezeka pa lemba la Yesaya 41:10, 13 amene amati: “Usawope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe . . . ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja lachilungamo. Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usawope ndidzakuthandiza iwe.”

Kugwiritsitsa dzanja lamanja la Mulungu kwathandiza Jezreel kuti asamachite manyazi, komanso kuti asamakhumudwe anthu ena akamamusala. Iye pamodzi ndi enanso ambiri akuyembekezera kuti matenda awo adzatha m’dziko latsopano la Mulungu.