Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zipatso Zofunika Kwambiri

Zipatso Zofunika Kwambiri

Zipatso Zofunika Kwambiri

▪ Mukamayenda m’dziko la Russia m’miyezi ya September, October ndi November, mumaona mitengo inayake yaing’onoing’ono imene imakhala ndi zipatso zooneka ngati nthudza. Zipatsozi zimakhala zambiri moti zimakuta nthambi yonse ndipo zimaoneka zokongola kwambiri.

Anthu amadya zipatsozi koma amafunika kusamala akamathyola chifukwa mtengo wake umakhala ndi minga. Komanso zipatsozi sizichedwa kuthudzuka choncho amathyola chipatso chilichonse pachokha. Mitengo ya zipatso zimenezi imakonda kumera m’madera ozizira, monga m’mapiri a kumpoto chakumadzulo kwa Ulaya, m’mapiri a Altai chapakati pa dziko la Asia, ndiponso kumadzulo ndi kumpoto kwa dziko la China komanso kumpoto kwa mapiri a Himalaya. Anthu a ku China, Russia ndi Tibet akhala akulima zipatsozi kwa zaka zambiri.

Mabuku a zamankhwala akale kwambiri a ku Tibet ndi Girisi amafotokoza za zipatso zimenezi. Dzina lachigiriki la mtengo wa zipatsozi ndi Hippophaë, ndipo limatanthauza kuti “hatchi ya ubweya wosalala.” Ena amaganiza kuti mtengowu anaupatsa dzina limeneli chifukwa chakuti ku Girisi anthu ankadyetsa mahatchi ochitira mpikisano zipatsozi kapena masamba a mitengo yake n’cholinga chakuti zizikhala ndi ubweya wosalala.

Zipatso zimenezi zinafika ku United States ndi Canada m’zaka za m’ma 1900 ndi anthu ochokera ku Russia. Mayiko ambiri amalima zipatso zimenezi masiku ano ndipo amazigwiritsira ntchito monga chakudya ndi mankhwala.

Zipatso zimenezi zimakhalanso ndi vitamini C ndi E, ndi zinthu zina zothandiza m’thupi la munthu. Akatswiri ena azachipatala akuti zipatsozi zimathandiza anthu odwala matenda a khansa, mtima, zilonda za m’mimba, matenda apakhungu ndi matenda a chiwindi. Zipatso zimenezi amapangiranso zakumwa zokoma zimene zimathandizanso anthu odwala matenda osiyanasiyana.

Zipatsozi zimakhala ndi njere zazing’ono zakuda. Njerezi zimakhala ndi mafuta ofunika kwambiri. Akatswiri ena amati mafutawa amawonjezera chitetezo cha m’thupi. Mafutawa amawagwiritsiranso ntchito popanga mafuta ena osalalitsa khungu.

Sitikukayikira kuti mukadzapita ku Russia, mudzasangalala kwambiri kuona zipatso zokongola komanso zofunika kwambiri zimenezi. Zipatso zimenezi ndi chimodzi mwa zinthu zambiri zimene zimasonyeza kuti Mlengi ndi wanzeru komanso wabwino kwambiri.