Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Masoka achilengedwe 9 pa masoka 10 aliwonse akuchitika chifukwa cha kusokonekera kwa nyengo. Malipoti akusonyeza kuti masoka achilengedwe awonjezereka kuchoka pa 200 kufika pa 400 pachaka, m’zaka 20 zapitazi.”—ANATERO JOHN HOLMES, YEMWE NDI MLEMBI WAMKULU KU NTHAMBI YA BUNGWE LA UNITED NATIONS YOONA ZA MASOKA ACHILENGEDWE.

Anthu Ambiri Sadziwa Ufulu Wawo

Malamulo a bungwe la UN onena za ufulu wa eni nthaka m’mayiko osiyanasiyana, omwe anavomerezedwa mu 2007, tsopano anamasuliridwa mu zilankhulo za Maya ndi Nahuatl, zomwe ndi zilankhula zikuluzikulu ku Mexico. Nyuzipepala ina inati: “Anthu pafupifupi 10 miliyoni [ku Mexico] sadziwa ufulu wawo. Choncho, anthu sadziwa kuti akuponderezedwa.” (El Universal) Anthu ena akuti kumasulira malamulowa kuthandiza kuti anthuwa asamaponderezedwe.

Kugulitsa Unamwali

Magazini ina inati akatswiri oona za chikhalidwe adabwa kuti atsikana ena ku Poland, omwe sanagonepo ndi mwamuna akumalolera kugona ndi amuna n’cholinga choti apeze ndalama. Katswiri wina, dzina lake Jacek Kurzępa, ku yunivesite ya Zielona Góra, anati: “Atsikanawa akumauzidwa kuti masiku ano palibe chaulere.” Atsikana ena ambiri omwe sanagonepo ndi mwamuna akumadzitsatsa malonda pa Intaneti. Koma mavuto amene atsikanawa amakumana nawo akagona ndi amuna ndi aakulu kuposa ndalama zimene amapeza. Kurzępa anati: “Kuchita zimenezi kumawononga moyo wawo wonse komanso kumadzasokoneza banja lawo akadzakwatiwa.”—Newsweek Polska.

Kunkhalango ya Amazon Kunali Matawuni

Anthu ena akukhulupirira kuti m’madera ambiri kum’mwera kwa nkhalango ya Amazon kunali matawuni omwe “anali ndi mipanda yaitali.” Akatswiri oona za chikhalidwe cha anthu ku Mato Grosso, m’dziko la Brazil, ndi amene ananena zimenezi. Kunkhalangoyi anapeza “mabwinja a matawuni okhala ndi mipanda ndiponso midzi ing’onoing’ono” pamalo aakulu makilomita 30,000 m’litali ndi m’lifupi. Matawuni ena anali aakulu mahekitala 60. Lipoti lochokera ku yunivesite ya ku Florida linati matawuniwa anamangidwa “m’zaka za pakati pa 1250 ndi 1650, panthawi imene anthu ochokera ku Ulaya ndiponso matenda omwe anabweretsa anapha anthu ambiri pamalowa.”

Maluwa Amathandiza Anthu Ochitidwa Opaleshoni

Kwa nthawi yaitali anthu akhala akuganiza kuti kukhala pafupi ndi maluwa kumachepetsa nkhawa, kumachititsa kuti munthu uzimva bwino komanso kumachepetsa ululu munthu akamadwala. Kafukufuku wina waposachedwapa watsimikizira kuti zimenezi ndi zoona. Magazini ina inati: “Odwala ena anaikidwa m’zipinda zimene zinalibe maluwa ndipo ena anaikidwa m’zipinda zokhala ndi maluwa.” (Science Daily) Odwala amene anali ndi maluwa m’zipinda zawo sankamva ululu waukulu, sankafunika mankhwala ambiri opha ululu, mtima wawo sunkagunda kwambiri komanso ankasangalala ndi zipinda zawo kuposa amene analibe maluwa. Pafupifupi 93 peresenti ya anthu omwe anali ndi maluwa m’zipinda zawo ananena kuti maluwawo ankachititsa kuti zipinda zawo zikhale “zosangalatsa kwambiri.”