Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kutha kwa Banja Kumakhudza Bwanji Ana?

Kodi Kutha kwa Banja Kumakhudza Bwanji Ana?

Kodi Kutha kwa Banja Kumakhudza Bwanji Ana?

AKATSWIRI a zam’banja ankaganiza kuti apeza malangizo abwino othandiza mabanja amene anali ndi mavuto. Iwo ankauza mabanja kuti: ‘Musadandaule za ana. Muzingoganizira zimene mungachite kuti inuyo mukhale wosangalala. Ana ndi opirira kwambiri. Iwo amaona kuti ndi bwino kukhala ndi mayi kapena bambo okha m’malo mokhala ndi makolo onse awiri amene amangokangana.’

Komabe, alangizi ena a za m’banja amene kale ankalimbikitsa anthu kuti akamakumana ndi mavuto m’banja azingolithetsa, panopa asintha maganizo awo. Iwo ayamba kunena kuti ‘kuthetsa banja kuli ngati nkhondo, aliyense amavulalapo, kuphatikizapo ana.’

Kutha kwa Banja ndi Nkhani Yaikulu

Anthu ambiri amaganiza kuti kutha kwa banja ndi nkhani yaing’ono monga mmene amasonyezera m’mafilimu ndi pa TV. M’mafilimu ndi pa TV nthawi zambiri amaonetsa mwamuna ndi mkazi wake atathetsa ukwati. Mayi amatsala ndi ana ndipo amakakwatiwa ndi mwamuna wina amene ali ndi ana akenso. Mlungu uliwonse banja latsopanolo limakumana ndi mavuto osiyanasiyana amene amawathetsa pa mphindi 30 zokha. Ndipo akamathetsa mavutowo amanena mawu anthabwala anthu n’kumaseka.

Mwina zimene tafotokozazi zimachititsa kuti mafilimu a pa TV azikhala osangalatsa. Koma kutha kwa banja si kosangalatsa. Katswiri wina dzina lake M. Gary Neuman analemba m’buku lake kuti: “Nthawi zambiri banja limakathera kukhoti, mwamuna kapena mkazi akakasuma. Mukasankha kuti banja lithe, mungalandidwe mwana, nyumba kapena kulipira ndalama. Mungayesetse kudandaulira woweruza koma mwina iye sangasinthe chigamulo. Mapeto ake woweruzayo, yemwe mwina simukudziwana naye n’komwe, angakuuzeni masiku amene muyenera kukaona mwana wanu pa mwezi, ndiponso ndalama zimene muyenera kumamupatsa. Zimene woweruzayu angakulamuleni kuchita zingakhale zosiyana kwambiri ndi zimene inuyo mukanachita panokha.”—Emotional Infidelity.

Nthawi zambiri kuthetsa banja kumangoyambitsa mavuto ena. Chilichonse chimasintha, kungoyambira kokhala komanso ndalama, ndipo nthawi zambiri kusintha kwake kumakhala kopweteka. Komanso kutha kwa banja kumawakhudza kwambiri ana.

Mmene Ana Amakhudzidwira

Kutha kwa banja kumakhudza ana a msinkhu uliwonse. Ena amanena kuti ana okulirapo samakhudzidwa kwambiri chifukwa chakuti amakhala okhwima maganizo ndipo amakhala atatsala pang’ono kusiyana ndi makolo awo. Koma akatswiri ena apeza kuti ana aakulu ndi amene amakhudzidwa kwambiri, ndipo zifukwa zimene anthu enawo amapereka n’zimenenso zimachititsa kuti anawa azikhudzidwa kwambiri. * Taganizirani mfundo zotsatirazi:

▪ Ana akamakula m’pamenenso amafunika kuthandizidwa kwambiri posankha zochita. Ngakhale kuti panthawiyi amafuna ufulu wosankha okha zochita, achinyamatawa amafunika kupatsidwa malangizo odalirika ndi makolo awo.

▪ Ana akamakula m’pamenenso amafunitsitsa kukhala ndi anzawo odalirika. Koma kutha kwa ukwati, kumachititsa kuti achinyamata asamadalire, kukhulupirira kapena kukonda anthu ena. Ndipo akakula amatha kupeweratu kuyanjana ndi anthu ena.

▪ Ngakhale kuti ana a misinkhu yonse zimawapweteka mtima banja likatha, achinyamata zimawapweteka mtima kwambiri ndipo amatha kuyamba moyo wauchigawenga, kumwa mowa mwauchidakwa, ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

Zimenezi sizikusonyeza kuti achinyamata onse amene banja la makolo awo latha, tsogolo lawonso limasokonekera. Iwo akhoza kukhala ndi tsogolo labwino malinga ngati amagwirizanabe ndi makolo awo onse. * Komabe n’kulakwitsa kuganiza kuti banja likatha, ana ziwayendera bwino kapena kukangana kutha. Ndipotu ena amaona kuti banja likatha m’pamene amakangana kwambiri ndi yemwe anali mwamuna kapena mkazi wawo pankhani zimene samaziyembekezera monga zokhudza ndalama kapena ana. Choncho kutha kwa banja sikuthetsa mavuto koma kumangochititsa kuti mwamuna ndi mkazi wake achoke kunyumba n’kumakakangana kukhoti.

Njira Yachitatu

Nanga mungatani ngati banja lanu silikuyenda bwino ndipo mukuganiza zolithetsa? Nkhaniyi ili ndi mfundo zofunika kuziganizira. Kuthetsa banja si njira yabwino yothetsera mavuto.

Komabe muyenera kumvetsa bwino mfundo imeneyi. Sitikutanthauza kuti ngati banja lanu silikuyenda bwino, njira yabwino ndi yoti muzingopirira. Pali njira ina yothandiza imene mungatsatire: Thetsani mavuto a banja lanu osati banjalo. Musafulumire kuganiza kuti njira imeneyi si yothandiza chifukwa chakuti banja lanu lili pa mavuto aakulu. Dzifunseni mafunso otsatirawa:

▪ ‘Kodi ndinakopeka ndi mkazi kapena mwamuna ameneyu chifukwa cha makhalidwe abwino ati? Kodi makhalidwewo anatha panopa?’—Miyambo 31:10, 29.

▪ ‘Kodi sizingatheke kuti ndiyambirenso kumukonda mkazi kapena mwamuna wangayu?’—Nyimbo ya Solomo 2:2; 4:7.

▪ ‘Ngakhale kuti mkazi kapena mwamuna wanga wasintha khalidwe lake, kodi ineyo ndingatani kuti ndizitsatira mfundo zomwe zili patsamba 3 mpaka 9 m’magazini ino?’—Aroma 12:18.

▪ ‘Kodi ndingathe kufotokozera mkazi kapena mwamuna wanga (pamasom’pamaso kapena pomulembera kalata) zimene tingachite kuti banja lathu liziyenda bwino?’—Yobu 10:1.

▪ ‘Kodi zingatheke kuitana munthu winawake amene timamudalira kuti atiuze zimene tingachite kuti banja lathu liziyenda bwino?’—Miyambo 27:17.

Baibulo limati: “Wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) Mfundo imeneyi imagwira ntchito posankha mkazi kapena mwamuna woti mudzakwatirane naye komanso mukamaganizira zochita ngati banja lanu silikuyenda bwino. Monga tafotokozera patsamba 9 m’magazini ino, ngakhale mabanja amene akuyenda bwino amakumana ndi mavuto. Chofunika ndi kudziwa kuthetsa mavutowo.

Mwachitsanzo: Taganizirani kuti muli paulendo wautali pa galimoto. N’zodziwikiratu kuti simungalephere kukumana ndi mavuto paulendo wanu monga mvula, kuchuluka kwa magalimoto mumsewu, ndiponso kuimitsidwa ndi apolisi. Nthawi zinanso mukhoza kusochera. Kodi mungatani ngati mutakumana ndi zimenezi? Kodi mungabwerere, kapena mungapeze njira ina yothetsera mavutowo n’kumapitiriza ulendo wanu? Kuyambira tsiku limene munakwatirana munayamba ulendo umene uli ndi mavuto ake. Baibulo limati: ‘Olowa m’banja adzakhala ndi nsautso.’ (1 Akorinto 7:28) Apa mfundo ndi yakuti banja lililonse limakumana ndi mavuto, koma nkhani yagona pa mmene mumawathetsera. Kodi mungapeze njira yothetsera mavutowo kuti banja lanu lipitirizebe kuyenda bwino? Ngakhale mutakumana ndi mavuto amene mukuona kuti sangatheke kuwathetsa, mungachite bwino kupeza thandizo.—Yakobe 5:14.

Mulungu Ndi Amene Anayambitsa Banja

Sitiyenera kuona banja mopepuka chifukwa Mulungu ndi amene analiyambitsa. (Genesis 2:24) Choncho mukamaona kuti mavuto anu ndi osatheka kuwathetsa, kumbukirani mfundo zimene takambirana m’nkhani ino.

1. Yambaninso kukonda mkazi kapena mwamuna wanu ngati mmene munkachitira poyamba.—Nyimbo ya Solomo 8:6.

2. Ganizirani zimene inuyo mungachite kuti banja lanu liyambenso kuyenda bwino ndipo chitani zimenezo.—Yakobe 1:22.

3. Mwaulemu ndiponso momveka bwino muuzeni mwamuna kapena mkazi wanu (kaya pamasom’pamaso kapena pomulembera kalata) zimene mungachite kuti banja lanu liziyenda bwino.—Yobu 7:11.

4. Pemphani ena kuti akuthandizeni. Si bwino kuumirira kuti mungathetse mavuto a m’banja lanu panokha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Nkhani ino ikunena za achinyamata koma kutha kwa banja kumakhudzanso ana aang’ono. Kuti mudziwe zambiri, onani Galamukani! ya December 8, 1997, masamba 21-30, ndi ya May 8, 1991, masamba 19-27.

^ ndime 13 Nthawi zina zimenezi sizitheka makamaka ngati bambo kapena mayi wathawa kapena akukana kusamalira ana kapenanso ndi wankhanza.—1 Timoteyo 5:8.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 19]

‘PANOPA BANJA LANGA LIYENDA BWINO’

Kafukufuku amasonyeza kuti banja lachiwiri limakhala ndi mavuto aakulu komanso silichedwa kutha kuposa loyamba, ndipo lachitatu ndi limene limathanso mofulumira kwambiri kuposa lachiwiri. M. Gary Neuman analemba m’buku lake kuti: “Ngati mukukumana ndi mavuto m’banja loyamba, sikuti munasankha molakwika, koma vuto ndi inuyo. Kumbukirani kuti poyamba munkakonda kwambiri mwamuna kapena mkazi wanuyo. Dziwani kuti nonse awiri munachititsa kuti banja lanu lifike pomwe lili panopa.” Pomaliza, Neuman ananena kuti: “Ndi bwino kuthetsa mavuto amene mukukumana nawo kusiyana n’kuthetsa banja lanu.”—Emotional Infidelity.

[Chithunzi patsamba 21]

ZIMENE MUNGACHITE BANJA LIKATHA

Baibulo limasonyeza kuti ngati zinthu zitafika povuta kwambiri banja lingathe. * Ngati banja lanu latha, kodi mungathandize bwanji ana anu kuti asataye mtima?

Afotokozereni zimene zikuchitika. Ngati zingatheke, makolo nonse awiri muyenera kufotokozera ana anu zimene zikuchitika m’banja mwanu. Auzeni kuti nonsenu mwaganiza zothetsa banjalo, ndiponso kuti iwo si amene achititsa kuti banjalo lithe. Atsimikizireni kuti nonse mupitirizabe kuwakonda.

Musamakangane. Makolo ena amapitirizabe kukangana patapita nthawi yaitali banja litatha. Malinga ndi zimene katswiri wina ananena, makolowa “akathetsa banja lawo, amapitirizabe kukangana ngati asilikali amene akambirana zosiya nkhondo koma akulephera kutsatira zomwe akambiranazo.” Zimenezi zimachititsa kuti ana asamagwirizane ndi makolo. Ndiponso zimachititsa kuti ana azikonda mayi kapena bambo okha. Mwachitsanzo, mwana angauze mayi ake kuti: “Bambo amandilola kubwera panyumba nthawi iliyonse imene ndikufuna. N’chifukwa chiyani inuyo mumandiletsa?” Zikatere, mayiwo amayamba kumulekerera mwanayo kuti asawaone ngati woipa.

Muzilola kuti ana anu azifotokoza maganizo awo. Ana anu anganene kuti, ‘Ngati makolo anasiya kukondana, ndiye kuti angasiyenso kutikonda,’ kapena, ‘Ngati makolo athu sanatsatire malamulo, kuli bwanji ifeyo?’ Kuti muthandize ana anu kuchotsa mantha komanso kuthetsa maganizo olakwika amenewa, muziwapatsa nthawi yofotokoza maganizo awo. Koma chenjezo ndi lakuti: Musayambe kuuza ana anu nkhawa zanu zonse. Kumbukirani kuti iwo ndi ana anu, osati anzanu owauza zakukhosi kwanu.

Limbikitsani ana anu kuti azikonda mkazi kapena mwamuna wanu wakale. Kumbukirani kuti mwamuna kapena mkazi amene munasiyana naye banja amakhalabe kholo la mwanayo. Kulankhula zinthu zoipa zokhudza mkazi kapena mwamuna wanu wakale kungawononge ana. Buku lina limati: “Ngati makolo amagwiritsa ntchito ana ngati zida zonyozera mwamuna kapena mkazi wawo wakale, adziwe kuti adzakolola zimene akufesa.”—Teens in Turmoil—A Path to Change for Parents, Adolescents, and Their Families.

Muzichita zinthu zokuthandizani. Nthawi zina mungakhumudwe kwambiri. Koma musataye mtima. Pitirizani kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni. Ngati ndinu Mkhristu, muzilimbikira kuchita zinthu zauzimu. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni inuyo komanso ana anu kuti musamakhumudwe kwambiri.—Salmo 18:2; Mateyo 28:19, 20; Aheberi 10:24, 25.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 38 Malinga ndi zimene Baibulo limanena, banja lingathe ngati mmodzi wachita chigololo. Ndipo zikatere, winayo atha kukwatiranso. (Mateyo 19:9) Wina akachita chigololo, mwamuna kapena mkazi wake ndi amene ali ndi ufulu wosankha kuthetsa banjalo, koma osati achibale kapena anthu ena.—Agalatiya 6:5.

[Chithunzi patsamba 20]

Yesetsani kutsatira zimene munalumbira patsiku la ukwati wanu

[Chithunzi patsamba 21]

Ngati nonse awiri mwaloledwa kusamalira mwana, mulimbikitseni mwanayo kuti azigwirizana ndi mkazi kapena mwamuna wanu wakale