Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndidziwane Bwino Ndi Makolo Anga?

Kodi Ndingatani Kuti Ndidziwane Bwino Ndi Makolo Anga?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Ndidziwane Bwino Ndi Makolo Anga?

Tsiku lina Jessica ndi makolo ake ankadya chakudya chamadzulo pamodzi ndi anzawo. Mmodzi wa anzawowo anauza mayi a Jessica kuti, “Simungakhulupirire nditakuuzani munthu amene ndinamuona tsiku lina. Ndinaona Richard, mnyamata amene munali naye pachibwenzi tili kusekondale uja.”

Jessica sanakhulupirire zimenezi ndipo nthawi yomweyo anagwetsa pansi foloko imene amadyera. Iye anali asanamvepo za Richard.

“Amayi, kodi munakhalapo pachibwenzi ndi munthu wina musanakwatirane ndi bambo?”

KODI inunso munadabwapo mutamva zinazake zokhudza makolo anu zimene simunkazidziwa? Ngati ndi choncho, mwina munaona kuti pali zambiri zoti mudziwe zokhudza makolo anu.

N’chifukwa chiyani pangakhale zinthu zina zokhudza makolo anu zimene simukuzidziwa? Kodi kuwadziwa bwino makolo anu kuli ndi phindu lililonse? Nanga mungatani kuti muwadziwe bwino?

Pali Zambiri Zoti Mudziwe

N’chifukwa chiyani pangakhale zinthu zina zokhudza makolo anu zimene simukuzidziwa? Nthawi zina zimenezi zimachitika chifukwa chakuti makolo amakhala kutali. Mwachitsanzo, Jacob, * amene ali ndi zaka 22, anati: “Makolo anga anasudzulana kalekale, ndili ndi zaka 8. Kuchokera nthawi imeneyo, ndinkaonana ndi bambo anga patalipatali. Pali zambiri zimene ndimafuna kudziwa zokhudza bambo anga.”

Ngakhale kuti mwina mwakhala ndi makolo anu kwa zaka zambiri, n’zotheka kuti sanakuuzeni zinthu zonse zokhudza iwowo. Angachite zimenezi chifukwa chakuti, mofanana ndi munthu wina aliyense, iwo amachita manyazi ndi zinthu zolakwika zimene anachita kalekale. (Aroma 3:23) Komanso iwo angaope kuti ngati atakuuzani zolakwa zawo, inuyo mungasiye kuwalemekeza kapena kuwamvera.

Koma nthawi zambiri makolo sakuuzani zinthu zokhudza iwowo chifukwa chakuti simunawafunsepo. Mnyamata wina, dzina lake Cameron, anati: “Zimadabwitsa kuti umatha kukhala zaka zambiri ndi makolo ako koma osadziwa zinthu zambiri zokhudza moyo wawo.” Ngati inuyo simukuwadziwa bwino makolo anu, mungachite bwino kuyesetsa kuti muwadziwe. Kodi kuchita zimenezi kuli ndi phindu lotani?

Phindu Loyamba: Makolo anu angasangalale. N’zosakayikitsa kuti makolo anu angasangalale ngati atadziwa kuti mukufuna kuwadziwa bwino. Iwo angayankhe mwachikondi mafunso amene mungawafunse.—Mateyo 7:12.

Phindu Lachiwiri: Mungadziwe mmene makolo anu amaganizira. Mwachitsanzo, ngati kale makolo anu anali osauka, mungamvetse chifukwa chake safuna kuwononga ndalama mwachisawawa.

Kudziwa mmene makolo anu amaganizira n’kothandiza kwambiri. Mnyamata wina, dzina lake Cody, anati: “Kudziwa mmene makolo anga amaganizira kwandithandiza kuti ndizidziwiratu mmene iwo angamvere ndikawauza zinthu zinazake.”—Miyambo 15:23.

Phindu Lachitatu: Mungamasuke kumawauza zimene zikukuchitikirani. Mtsikana wina wazaka 18, dzina lake Bridgette, anati: “Poyamba ndinkachita manyazi kuwauza bambo anga za mnyamata amene ndimamufuna, koma nditayamba kumasukirana nawo, anandiuza za chibwenzi chawo choyamba ndiponso chisangalalo chimene anali nacho atayamba chibwenzi ndi mtsikanayo. Anandiuzanso zimene zinachitika kuti chibwenzi chawo chithe komanso mmene zinawapwetekera. Zimenezi zinandichititsa kuti ndiwauze zambiri.”

Phindu Lachinayi: Mungaphunzire kulimbana ndi mavuto. Zimene makolo anu akumana nazo pamoyo wawo zingakuthandizeni kulimbana ndi mavuto anu. Joshua, yemwe ali ndi zaka 16, anati: “Ndikufuna kudziwa kuti makolo anga amakwanitsa bwanji kusamalira banja lalikulu. Ndikukhulupirira kuti kudziwa zimenezi kungandithandize kwambiri.” Baibulo limanena kuti: “Kwa okalamba kuli nzeru, ndi kwa a masiku ochuluka luntha.”—Yobu 12:12.

Zimene Mungachite Kuti Muwadziwe

Ngati mukufuna kuwadziwa bwino makolo anu, kodi mungatani? Mungachite zotsatirazi:

Sankhani nthawi yoyenera. Mukhoza kusankha nthawi ina iliyonse yoyenera. Mwachitsanzo, mungayambe kukambirana nawo posewera mpira, pogwira ntchito inayake kapena muli koyenda. Cody, yemwe tinamutchula uja, anati: “Ndawadziwa bwino kwambiri makolo anga chifukwa choyenda nawo ulendo wautali pa galimoto. Nthawi zambiri ndimasangalala kumvera wailesi kapena kugona pamene ndili m’galimoto, koma ndaona kuti kukambirana ndi makolo anga panthawi imeneyi kwandithandiza kuwadziwa bwino.”

Muzifunsa mafunso. Dziwani izi: Ngakhale mutasankha nthawi yoyenera, mayi anu sangakuuzeni zinthu zonse zokhudza iwowo panthawi imene anali pachibwenzi ndi winawake, ndiponso bambo anu sangakuuzeni nthawi imene anawononga galimoto ya makolo awo. Koma makolo anu angakufotokozereni zimenezi ngati matawafunsa.—Mafunso ena othandiza akupezeka  m’bokosi la patsamba 12.

Musawakakamize kunena zimene sakufuna. Nthawi zina mungafunse makolo anu funso koma iwo n’kuyamba kufotokoza zinthu zina. Ngati zimenezi zitachitika, mungachite bwino kuwasiya kuti apitirize kufotokoza m’malo mowakakamiza kuyankha funso lanu. Dziwani kuti cholinga chanu sikungodziwa zinazake zokhudza iwowo, koma kudziwana nawo bwino. Njira imodzi yochitira zimenezi n’kukambirana nawo nkhani zimene zingawasangalatse.Afilipi 2:4.

Chitani zinthu mozindikira. Baibulo limati: “Maganizo a munthu ali ngati chitsime chakuya, koma munthu wozindikira angatungemo madzi.” (Miyambo 20:5, Today’s English Version) Mufunika kuchita zinthu mozindikira makamaka mukamakambirana ndi makolo anu nkhani zimene sangamasuke kukambirana nanu. Mwachitsanzo, mwina mukufuna kudziwa zinthu zolakwika zimene bambo anu anachita pamene anali ndi zaka zofanana ndi zanu ndiponso mmene akanachitira panopo. Musanayambe kukambirana nawo nkhani zoterezi mungachite bwino kunena kuti, “Ndimafuna ndikufunseni za . . .”

Khalani wosamala. Makolo anu akamakuuzani nkhani zokhudza iwowo, yesetsani kukhala “wofulumira kumva, wodekha polankhula.” (Yakobe 1:19) Pamene mukukambirana, si bwino kuwanyoza chifukwa cha zimene akuuzani. Pewani kunena kuti, “Koma zoona munachitadi zimenezi?” kapena kunena kuti, “Ndamvetsa tsopano chifukwa chake mumavuta.” Zimenezi zingachititse kuti makolo anu asakuuzeni zambiri. Ndiponso si bwino kuuza anthu ena nkhani zokhudza makolo anu.

Simunachedwe

Zimene tafotokozazi zingakuthandizeni kuwadziwa bwino makolo anu musanayambe kukhala panokha. Komabe, mfundozi zingakuthandizeninso ngati munayamba kale kukhala panokha. Mwachitsanzo, Jacob yemwe tamutchula poyamba uja amakhala payekha ndipo ananena kuti: “Ndayamba posachedwapa kuwadziwa bwino makolo anga ndipo ndikusangalala kwambiri?”

Choncho kaya mukukhala ndi makolo anu kapena nokha, musaone kuti mwachedwa kudziwana nawo. Ingoyesetsani kutsatira mfundo zimene zili m’nkhani ino.

Nkhani zina zakuti Zimene Achinyamata Amafunsa, mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Maina ena m’nkhaniyi tawasintha.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi ndi zinthu ziti zimene zatchulidwa m’nkhaniyi zimene mungakonde kufunsa makolo anu?

▪ Kodi kuwadziwa bwino makolo anu kungakuthandizeni bwanji kudzidziwa nokha?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]

  Mafunso oti mufunse makolo anu

UKWATI: Kodi munakumana bwanji ndi mayi (kapena bambo)? Kodi n’chiyani chinachititsa kuti muyambe kukondana? Kodi munkakhala kuti mutakwatirana?

ALI ANA: Kodi munabadwira kuti? Kodi munkakhala bwanji ndi abale anu? Kodi makolo anu anali ovuta kapena ayi?

MAPHUNZIRO: Kodi munkakonda phunziro liti kusukulu? Kodi munkalephera phunziro liti? Kodi munali ndi mphunzitsi amene munkamukonda kwambiri? Kodi munkamukonda kwambiri chifukwa chiyani?

NTCHITO: Kodi ntchito yanu yoyamba inali yotani? Kodi munkaikonda? Mukanapatsidwa mwayi wosankha ntchito ina, kodi mukanasankha ntchito yotani?

ZIMENE AMAKONDA: Ngati mutapatsidwa mwayi wopita dziko lina, kodi mungakonde kupita dziko liti? Kodi mungakonde kuphunzira masewera kapena luso lotani?

MOYO WAWO WAUZIMU: Kodi munakulira m’banja lachikhristu? Ngati sanakulire m’banja lachikhristu mungawafunse kuti, Kodi munaphunzira bwanji Baibulo? Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene zinkakuvutani kuzitsatira?

ZINTHU ZOFUNIKA KWA IWO: Kodi mumaona kuti chimafunika ndi chiyani kuti anthu akhale ogwirizana? kuti azisangalala pamoyo wawo? kuti mabanja awo aziyenda bwino? Kodi ndi malangizo otani amene mumaona kuti anakuthandizani kwambiri?

Yesani izi: Sankhani ena mwa mafunso amene ali pamwambawa ndipo ganizirani mmene makolo anu angawayankhire. Kenako afunseni makolo anu mafunsowa ndipo yerekezani mayankho awo ndi mayankho amene munaganizira.

[Bokosi patsamba 13]

MAWU KWA MAKOLO

Tiyerekeze kuti mukudya chakudya chamadzulo ndi mwamuna wanu, mwana wanu wamkazi ndiponso anzanu. Pamene mukucheza, mmodzi wa anzanuwo akutchula munthu wina amene munali naye pachibwenzi poyamba musanapezane ndi mwamuna wanu. Nkhani imeneyi munali musanauzepo mwana wanuyo. Choncho akufuna kudziwa zambiri. Kodi mungatani?

Nthawi zambiri ndi bwino kuyankha mafunso ake. Dziwani kuti kuyankha mafunso a mwana wanu n’kofunika chifukwa zimakupatsani mpata wokambirana, ndipo mpata woterewu ndi wosowa.

Kodi muyenera kuuza mwana wanu zinthu zotani zokhudza moyo wanu? Makolo ambiri safuna kuuza ana awo zinthu zochititsa manyazi zimene iwowo anachita. Komabe kuwauza zinthu zina zolakwika zimene munachita ndiponso mavuto amene mwakumana nawo pamoyo wanu kungawathandize. N’chifukwa chiyani tikutero?

Taganizirani chitsanzo cha mtumwi Paulo. Panthawi ina iye ananena kuti: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili nane. . . . Munthu wovutika ine!” (Aroma 7:21-24) Yehova Mulungu ndi amene anachititsa kuti mawu amenewa alembedwe ndiponso kusungidwa mpaka pano kuti azitithandiza. (2 Timoteyo 3:16) Ndipo amatithandizadi chifukwa ifenso nthawi zina timalephera kuchita zabwino ngati mmene Paulo ananenera.

Choncho kuuza ana anu zimene munachita bwino ndi zimene munalakwitsa, kungawalimbikitse kuti nawonso azikuuzani zolakwa zawo. Mwina mungaone kuti kuchita zimenezi n’kovuta chifukwa chakuti m’nthawi yanu makolo sankauza ana zolakwa zawo. Koma dziwani kuti mfundo za m’Malemba ndiponso zimene ana amafuna sizinasinthe. (Salmo 119:144) Kukambirana ndi ana anu mavuto amene mwakumana nawo pamoyo wanu komanso mmene mwawathetsera kungawathandize kuthana ndi mavuto awo. Mnyamata wina dzina lake Cameron anati: “Ukadziwa kuti makolo ako anakumana ndi zinthu zofanana ndi zimene ukukumana nazo, umawamvetsa ndipo umazindikira kuti iweyo si wosiyana ndi iwowo. Choncho panthawi ina ukakumana ndi vuto linalake, umafuna udziwe ngati makolo ako anakumananso ndi vuto limeneli.”

Chenjezo: Musamapatse ana anu uphungu nthawi iliyonse imene mwawauza zimene zinakuchitikirani. Mwina mungaope kuti ngati simuwapatsa uphungu, ana anuwo angaone kuti palibe vuto kuchitanso zolakwa zomwezo. Koma m’malo mouza ana anu zimene ayenera kuphunzirapo pa zimene mwakambiranazo (Mwachitsanzo kunena kuti, “Choncho, musadzachite zimenezi.”), fotokozani mmene mukumvera. (Mwachitsanzo, kunena kuti, “Pamenepa ndikuona kuti ndikanachita bwino ndikanatere chifukwa . . .”) Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muphunzitse ana anu mfundo yofunika kuchokera pa zimene munakumana nazo popanda kuwakhumudwitsa.—Aefeso 6:4.

[Bokosi patsamba 13]

“Tsiku lina ndinauza mayi anga kuti ndimakhala womasuka kucheza ndi anzanga akusukulu m’malo mocheza ndi Akhristu anzanga. Tsiku lotsatira ndinapeza kalata patebulo imene iwo anandilembera. M’kalatamo ananena kuti nawonso panthawi ina ankaona kuti alibe anzawo enieni mumpingo. Iwo anandikumbutsa za anthu ena a m’Baibulo amene ankatumikira Mulungu ngakhale kuti analibe munthu wina wowalimbikitsa. Mayi anandiyamikiranso chifukwa cha kuyesetsa kwanga kupeza anzanga abwino. Ndinasangalala kwambiri kudziwa kuti mayi anga komanso anthu ena anakumananso ndi vuto lofanana ndi langa. Zimene mayi ananena zinandilimbikitsa kwambiri, ndipo zinandithandiza kupitiriza kuchita zinthu zabwino.”—Anatero Junko, mtsikana wazaka 17 wa ku Japan.

[Chithunzi patsamba 11]

Pemphani makolo anu kuti akuonetseni zithunzi zawo kapena zinthu zina zakale. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muyambe kukambirana nawo momasuka