Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’kulakwa Mwamuna ndi Mkazi Kukhalira Limodzi Asanakwatirane?

Kodi N’kulakwa Mwamuna ndi Mkazi Kukhalira Limodzi Asanakwatirane?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi N’kulakwa Mwamuna ndi Mkazi Kukhalira Limodzi Asanakwatirane?

KODI mungagule chovala popanda kuchiyesa kaye? N’zokayikitsa kuti mungatero, chifukwa zingakuwonongetseni ndalama ndiponso nthawi ngati mutafika kunyumba n’kupeza kuti chovalacho sichikukukwanani.

Anthu ambiri amaganiza kuti zimenezi n’zofanana ndi ukwati. Iwo amaona kuti ndi bwino kuti ayambe ayesa kaye kukhala limodzi ndi munthu amene akufuna kudzakwatirana nayeyo. Anthuwa amanena kuti, ‘Ngati sitikugwirizana, aliyense angayendere yake popanda kupita kukhoti kukathetsa ukwati, zomwe zingatiwonongetse nthawi ndi ndalama zambiri.’

Anthu amene amaganiza zimenezi mwina amakhala kuti aonapo anthu okwatirana omwe sakondana kapena mnzawo akuchitidwa nkhanza ndi mwamuna kapena mkazi wake. Choncho iwo angaone kuti ndi nzeru kuti asanalowe m’banja ayambe akhala limodzi ndi mkazi kapena mwamuna amene akufuna kudzakwatirana naye.

Koma kodi Baibulo limati chiyani pankhani imeneyi? Kuti tiyankhe funso limeneli, choyamba tiyenera kuganizira zimene Mawu a Mulungu amanena zokhudza chiyambi cha ukwati.

“Thupi Limodzi”

Baibulo limasonyeza kuti ukwati ndi wolemekezeka, ndipo zimenezi si zodabwitsa chifukwa Yehova Mulungu ndi amene anauyambitsa. (Genesis 2:21-24) Kungoyambira pachiyambi, Yehova anafuna kuti mwamuna ndi mkazi wake akhale “thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Yesu anatchulanso mfundo yomweyi ndipo ananena kuti: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mateyo 19:6.

Komabe mabanja ena amatha. * Zimenezi zimachitika osati chifukwa chakuti ukwati ndi wolakwika koma chifukwa chakuti mmodzi kapena onse awiri alephera kutsatira zimene analonjeza pokwatirana.

Tiyerekezere kuti mwamuna ndi mkazi wake ali ndi galimoto koma saisamalira mogwirizana ndi malangizo a opanga galimotoyo. Kodi itawonongeka, vuto lingakhale la ndani? Wopanga galimotoyo, kapena mwamuna ndi mkazi wakeyo?

N’chimodzimodzinso ndi banja. Ngati mwamuna ndi mkazi wake akuyesetsa kuthetsa mavuto awo pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo, n’zovuta kuti banja lawo lithe. Banjalo limakhala lolimba chifukwa chakuti aliyense amayesetsa kuchita zimene analonjeza pokwatirana. Zimenezi zimathandiza kuti mwamuna ndi mkazi wake azikondana.

‘Pewani Dama’

Anthu ena angaonebe kuti palibe vuto ngati mwamuna ndi mkazi ayamba kukhalira limodzi asanakwatirane. Iwo angaganize kuti kuchita zimenezi n’kumene kumasonyeza kuti ukwati ndi wolemekezeka.

Baibulo limasonyeza kuti maganizo amenewa ndi olakwika. Paulo analimbikitsa anthu “kupewa dama.” (1 Atesalonika 4:3) Mawu akuti “dama” amatanthauza kugonana kulikonse kwa anthu amene sanakwatirane, kuphatikizapo mwamuna ndi mkazi amene amakhalira limodzi asanakwatirane. Choncho, malinga ndi zimene Baibulo limanena, n’kulakwa kuti mwamuna ndi mkazi azikhalira limodzi asanakwatirane, ngakhale atakhala ndi cholinga chodzakwatirana.

Anthu ena amakayikira ngati zimene Baibulo limanena pankhani imeneyi zili zothandiza masiku ano? Ndipotu m’mayiko ambiri anthu samaona zachilendo ngati anthu osakwatirana akukhalira limodzi, kaya anthuwo ali ndi cholinga chodzakwatirana kapena ayi. Koma taganizirani izi: Kodi anthu amene amakhalira limodzi asanakwatirane, zinthu zimawayendera bwino? Kodi iwo amakhala osangalala kwambiri kuposa anthu amene anakwatirana? Kodi mwamuna ndi mkazi amene anakhalira limodzi asanakwatirane amakhala okhulupirika akalowa m’banja? Kafukufuku amasonyeza kuti anthu amene amakhalira limodzi asanakwatirane, akadzakwatirana sagwirizana ndipo nthawi zambiri mabanja awo amatha.

Koma anthu ena anganene kuti kafukufuku ameneyu si wolondola. Mwachitsanzo, katswiri wina ananena kuti mavuto amene anthu omwe amayamba akhalira limodzi asanakwatirane amakumana nawo pamoyo wawo amakhala osiyana ndi mavuto a anthu amene amakwatirana popanda kukhalira limodzi. Choncho, malinga ndi katswiriyu, zimene zimachititsa kuti mabanja azitha si kukhalira limodzi koma “mmene anthuwo amaonera ukwati.”

Ngakhale zitakhala kuti zimene ananena katswiriyu ndi zoona, zimenezi zikungosonyeza kufunika koona ukwati mmene Mulungu amauonera. Baibulo limati: “Ukwati ukhale wolemekezeka pakati pa onse.” (Aheberi 13:4) Ngati mwamuna ndi mkazi alumbira kuti adzakhala thupi limodzi ndipo akupitirizabe kuona kuti ukwati wawo ndi wolemekezeka, ukwatiwo sungathe.—Mlaliki 4:12.

Ndiyeno poganizira chitsanzo chimene tafotokoza kumayambiriro kwa nkhaniyi, ndi bwino kuyesa kaye chovala musanachigule. Komabe chitsanzo chimenechi sichikusonyeza kuti ndi bwino kukhalira limodzi musanakwatirane. M’malomwake chikusonyeza kuti ndi bwino kukhala ndi nthawi yokwanira yodziwana ndi munthu amene mukufuna kudzakwatirana nayeyo. Ngakhale kuti anthu ambiri amainyalanyaza, mfundo imeneyi ndi yofunika kwambiri kuti banja lanu liziyenda bwino.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Baibulo limanena kuti mwamuna kapena mkazi angathetse ukwati n’kukwatiranso ngati mnzake wachita chigololo.—Mateyo 19:9.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti anthu osakwatirana asamagonane?—Salmo 84:11; 1 Akorinto 6:18.

▪ Kodi munthu yemwe mukufuna kudzakwatirana naye ayenera kukhala ndi makhalidwe otani?—Rute 1:16, 17; Miyambo 31:10-31.

[Bokosi patsamba 29]

“AMACHIMWIRA THUPI LAKE”

Baibulo limati: “Amene amachita dama amachimwira thupi lake.” (1 Akorinto 6:18) Mfundo imeneyi ndi yoona makamaka tikaganizira kuti masiku ano anthu ambiri akufa ndi matenda a Edzi komanso matenda ena opatsirana. Komanso si zokhazo. Kafukufuku amasonyeza kuti achinyamata ambiri amene amagonana asanakwatirane amavutika maganizo ndiponso amafuna kudzipha. Mavuto enanso ndi monga kutenga mimba yosakonzekera, zimene zimachititsa kuti atsikana ena aganize zochotsa mimbayo. Pazifukwa zimene takambiranazi, mungaone kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza masiku ano.