Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo 1: Muzikonda Kwambiri Banja Lanu

Mfundo 1: Muzikonda Kwambiri Banja Lanu

Mfundo 1: Muzikonda Kwambiri Banja Lanu

“Mutsimikizire kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

Mungachite bwanji? Kuti banja lanu liziyenda bwino, muzikonda mwamuna kapena mkazi wanu kuposa mmene mumakondera zinthu zina monga katundu wanu, ntchito, anzanu ndiponso achibale. Mufunika kuthera nthawi yochuluka muli ndi mkazi kapena mwamuna wanu komanso ana anu. Nthawi zina mungafunike kusiya kuchita zinthu zina kuti muthandize banja lanu.—Afilipi 2:4.

Kufunika kwake. Baibulo limasonyeza kuti banja ndi lofunika kwambiri. Mtumwi Paulo analemba kuti munthu amene sasamalira banja lake “ndi woipa kuposa munthu wopanda chikhulupiriro.” (1 Timoteyo 5:8) Anthu ena amasiya kukonda banja lawo n’kuyamba kukonda zinthu zina. Mwachitsanzo, mlangizi wina wa zam’banja ananena kuti anthu ambiri amene anabwera kumsonkhano umene iye anachititsa, ankaoneka kuti amakonda kwambiri ntchito kuposa banja lawo. Iye ananena kuti anthuwo ankangofuna kuuzidwa njira yachidule yothetsera mavuto a m’banja mofulumira n’cholinga choti akhale ndi nthawi yambiri yokagwira ntchito yawo. Zimenezi zikusonyeza kuti n’zophweka kunena kuti timakonda kwambiri banja lathu koma kuchita zimene tikunenazo n’kovuta.

Yesani izi. Yankhani mafunso otsatirawa kuti mudziwe ngati mumakonda kwambiri banja lanu.

Kodi ndimamvetsera ngati mwamuna, mkazi, kapena mwana wanga akufuna kulankhula nane?

Ndikamauza anzanga zinthu zimene ndimachita, kodi nthawi zambiri ndimanena zinthu zimene ndimachita ndi banja langa?

Kodi ndingakane udindo winawake (kuntchito kapena kwina kulikonse) kuti ndizikhala ndi nthawi yokwanira yosamalira banja langa?

Ngati yankho lanu ndi lakuti inde pa mafunso onsewa, mungaganize kuti mumakonda kwambiri banja lanu. Koma kodi mkazi ndi ana anu anganene chiyani zokhudza inuyo atafunsidwa mafunso amenewa? Zimene iwo anganene zingakuthandizeni kudziwa ngati mukuchita bwino kapena ayi. Ndipo kufunsa ena kuti mudziwe maganizo awo kungakuthandizenso pa mfundo zimene tikambirane kutsogoloku.

Chitani izi. Ganizirani chinthu chimodzi kapena ziwiri zimene mungachite kuti musonyeze kuti mumakonda banja lanu kuposa zinthu zina. (Mwachitsanzo, mungachepetse kuchita zinthu zimene zimakuwonongerani nthawi imene mungaigwiritse ntchito posamalira mkazi ndiponso ana anu.)

Mungachite bwino kuuza banja lanu zimene mwasankha kuchita. Inuyo mukasonyeza kuti mukufuna kusintha, enawonso angafune kuchita chimodzimodzi.

[Chithunzi patsamba 3]

Mkazi ndi ana amasangalala ndi bambo amene amawakonda kwambiri